1Mwana wanga, ukafuna kutumikira Ambuye,
ukonzekere kuyesedwa ndi masautso.
2Ukhale wa mtima woona,
ndiponso munthu wosatepatepa.
Usataye mtima msanga pa nthaŵi ya zovuta.
3Ukangamire Mulungu osamsiya,
kuti udzapeze ulemerero pa kutha kwa moyo wako.
4Upirire zilizonse zokugwera,
ndipo ukamva manyazi nthaŵi zina,
ukhalebe wopirira.
5 Lun. 3.5, 6; 1Pet. 1.7 Pajatu golide amamuyesa m'ng'anjo ya moto,
ndipo Ambuye amayesa anthu m'ng'anjo ya zotsitsa.
6Ukhulupirire Ambuye, ndipo adzakuthandiza.
Utsate njira yolungama ndipo uŵakhulupirire.
7Inu amene mumaopa Ambuye,
muyembekeze chifundo chao.
Musaŵafulatire kuti mungagwe.
8Inu amene mumaopa Ambuye, muŵakhulupirire,
ndipo simudzalephera kulandira mphotho.
9Inu amene mumaopa Ambuye,
mukhulupirire zinthu zabwino pa moyo wanu,
mukhulupirire chikondwerero chamuyaya
ndiponso chifundo.
10Muganizire za mibadwo yakale
ndipo muwone kuti kodi alipo
amene adaakhulupirira Ambuye,
Iwo namuchititsa manyazi?
Kodi alipo amene adaalimbikira kuwopa Ambuye,
Iwo namusiya?
Kodi alipo amene adaapempha Ambuye kanthu,
Iwo osamumvera?
11Pajatu Ambuye ngokoma mtima ndiponso achifundo.
Amakhululukira machimo,
amapulumutsa anthu pa nthaŵi ya mavuto.
12Tsoka kwa anthu a mtima wolefuka
ndi a manja olobodoka.
Tsoka kwa wochimwa
amene ali ndi mtima wapaŵiripaŵiri.
13Tsoka kwa amene ali ndi mtima wosalimbikira ndi
wosakhulupirira,
chifukwa cha chimenecho sadzathandizidwa.
14Tsoka kwa inu amene mudalekeza kulimbikira kwanu.
Nanga mudzatani tsiku lodzakulangani Ambuye?
15 Lun. 6.18; Yoh. 14.15, 21, 23 Anthu oopa Ambuye amamvera mau ao.
Onse okonda Ambuye amatsata njira zao.
16Anthu oopa Ambuye
amayesetsa kuchita chifuniro cha Ambuyewo.
Anthu okonda Ambuye
amatsata Malamulo ao.
17Anthu oopa Ambuye amakonzeratu mitima yao,
amadzichepetsa pamaso pa Ambuye.
18Amati,
“Tiyeni tigwe m'manja mwa Ambuye,
osati m'manja mwa anthu,
popeza kuti chifundo chao
nchachikulu ngati ufumu wao.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.