1Aefuremu adakonzeka kuti akamenye nkhondo, ndipo adaolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Chifukwa chiyani udaaoloka kukamenya nkhondo ndi Aamoni, ife osatiitana kuti tipite nao? Tikutenthera m'nyumba mwakomu.”
2Yefita adaŵauza kuti, “Ine ndi anthu anga tidaakangana kwambiri ndi Aamoni. Ndidakuitanani, koma inu simudadzandipulumutse kwa iwowo.
3Ndipo nditaona kuti simunkafuna kundipulumutsa, ndidangochita utotomoyo nkuwoloka Yordani kukalimbana nawo Aamoni. Chauta adatithandiza kuŵagonjetsa. Chifukwa chiyani tsono mwabwera kwa ine lero lino kuti mudzachite nane nkhondo?”
4Tsono Yefita adasonkhanitsa anthu onse a ku Giliyadi namenyana nkhondo ndi Aefuremu. Ndipo Agiliyadi adagonjetsa Aefuremu chifukwa chakuti Aefuremuwo ankati, “Inu Agiliyadi ndinu othaŵa ku Efuremu, ochokera pakati pa Aefuremu ndi Amanase.”
5Ndipo Agiliyadi adalanda Aefuremu madooko a mtsinje wa Yordani. Pamene aliyense wothaŵa ku Efuremu ankati, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agiliyadi ankamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Mwefuremu?” Iye akayankha kuti, “Ai”,
6iwo ankamuuza kuti, “Chabwino, nena kuti, ‘Shiboleti.’ ” Munthuyo ankati, “Siboleti,” pakuti sankatha kutchula bwino mauwo. Ankamugwira ndi kumupha pompo pa madooko a mtsinje wa Yordani. Nthaŵi imeneyo adaphedwa Aefuremu 42,000.
7Yefita adaweruza Aisraele zaka zisanu ndi chimodzi. Pambuyo pake Yefita, amene anali Mgiliyadi, adamwalira, ndipo adaikidwa mu mzinda wake wa Giliyadi.
Za Ibizani, Eloni ndi Abidoni.8Atafa Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu adaweruza Aisraele.
9Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu ndiponso ana aakazi makumi atatu. Adakwatitsa ana aakazi makumi atatuwo kwa anthu osakhala a fuko lake, ndipo adakatengera ana ake aamuna aja ana aakazi makumi atatu a fuko lachilendo. Ibizaniyo anali mtsogoleri wa Aisraele zaka zisanu ndi ziŵiri.
10Pambuyo pake adamwalira, ndipo adaikidwa ku Betelehemu.
11Ibizani atafa, Eloni Mzebuloni adasanduka mtsogoleri wa Aisraele. Iyeyu adatsogolera Aisraele zaka khumi.
12Pambuyo pake adamwalira, naikidwa ku Ayaloni m'dziko la Zebuloni.
13Atafa iyeyo, Abidoni mwana wa Hilele Mpiratoni, adatsogolera Aisraele.
14Iye anali ndi ana aamuna makumi anai ndi adzukulu makumi atatu amene ankakwera pa abulu makumi asanu ndi aŵiri. Iye adatsogolera Aisraele zaka zisanu ndi zitatu.
15Ndipo Abidoniyo adamwalira, naikidwa ku Piratoni m'dziko la Efuremu, ku mapiri a Aamaleke.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.