Yes. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aisraele abwerako kuchokera ku ukapolo

1Chauta adzachitira chifundo a m'banja la Yakobe, adzasankhanso Aisraele ndi kuŵalola kuti akhalenso m'dziko lao. Akunja adzabwera kudzakhala nao ndi kuphatikira ku banja la Yakobe.

2Anthu a mitundu ina adzaperekeza Aisraele ku dziko limene Chauta adaŵapatsa. Kumeneko anthuwo adzakhala otumikira Aisraele ngati akapolo ndi adzakazi. Aisraele adzagwira ukapolo anthu amene kale adaali ambuyao ndi kumalamulira anthu amene kale ankaŵazunza.

Kunyodola mfumu ya ku Babiloni

3Chauta adzakupumitsani ku zoŵaŵa ndi mavuto, ndiponso ku ntchito yakalavulagaga imene anthu ankakugwiritsani.

4Motero mudzanyodola mfumu ya ku Babiloni, mudzati,

“Watha bwanji wopsinja uja?

Kwatha bwanji kudzikuza kwake kuja?

5Chauta wathyola mkwapulo wa anthu oipa,

wasakaza ndodo yaufumu ya olamulira.

6Iwowo ankakantha mitundu ya anthu

mokwiya pomaŵamenya kosalekeza.

Ankalamulira mitundu ya anthu mwaukali

ndi kumaŵazunza kosalekeza.

7Dziko lonse lapansi lapumula,

tsopano lakhala bata,

ndipo anthu akuimba mokondwa.

8Mitengo ya paini ikukondwerera

kugwa kwa Babiloni.

Mikungudza ya ku Lebanoni ikuti,

‘Chigwetsedwere chako pansi, mfumu iwe,

palibe wina amene adabwera kudzatigwetsa.’

9“Kumanda kwatekeseka kuti kukulandire

podzafika iwe mfumu ya ku Babiloni.

Mandawo adzutsa mizimu ya anthu akufa

kuti ikulonjere iwe,

adzutsa mizimu ya onse amene adaali

atsogoleri pa dziko lapansi.

Akuŵaimiritsa pa mipando yao yaufumu

onse amene adaali mafumu a mitundu ya anthu.

10Onsewo adzalankhula,

ndipo adzakuuza kuti:

‘Iwenso watheratu mphamvu monga ife!

Tsopano tafanana.’

11Ulemerero wako, pamodzi ndi nyimbo

za pa azeze ako, zonse zatha,

waloŵa nazo m'manda.

Bedi lako ndi mphutsi,

chofunda chako ndi nyongolotsi.

12 Chiv. 8.10; 9.1 “Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,

iwe Nthanda, mwana wa Mbandakucha?

Wagwetsedwa pansi bwanji,

iwe amene unkagonjetsa mitundu ya anthu?

13 Mt. 11.23; Lk. 10.15 Mumtima mwako unkati,

‘Ndidzakwera mpaka kumwamba.

Ndidzakhazika mpando wanga waufumu

pamwamba pa nyenyezi za Mulungu.

Ndidzakhala pampandopo pa phiri la

kumpoto kumene imasonkhanako milungu yonse.

14Ndidzakwera pamwamba pa mitambo,

ndidzafanafana naye Wopambanazonse.’

15Koma watsitsidwa m'manda,

pansi penipeni pa dzenje.

16“Anthu akufa akakuwona

azidzakupenyetsetsa nkuyamba kulingalira

za iwe kuti,

‘Kodi uyu si munthu uja ankanjenjemeretsa

dziko lapansi, ndi kugwedeza maufumu?

17Kodi si ameneyu uja adasandutsa dziko

lapansi chipululu ndi kugwetsa mizinda,

ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwao?’

18Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona

mwaulemerero aliyense m'manda akeake.

19Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako

ngati nthambi yoola ndi yonyansa.

Mtembo wako waphimbidwa ndi ophedwa

amene adabayidwa ndi lupanga,

naponyedwa m'dzenje lamiyala.

Udzakhala ngati mtembo woponderezedwa.

20“Sudzaikidwa nao m'manda mwaulemerero,

chifukwa chakuti waononga dziko lako, wapha anthu ako.

“Zidzukulu za anthu ochita zoipa

zisadzakumbukike mpang'ono pomwe.

21Mukonzekere kupha ana aamuna a mfumuyi,

chifukwa cha kulakwa kwa atate ao, kuwopa

kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi

ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda.”

Mulungu adzaononga Babiloni

22Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzauthira nkhondo mzinda wa Babiloni. Ndidzathetseratu dzina lake ndi onse otsaliramo. Sipadzapulumuka ana ndi zidzukulu zomwe. Ndatero Ine Chauta.

23Mzindawo ndidzausandutsa dambo lamatope ndi malo okhalamo akanungu. Ndidzausesa ndi tsache lofafaniza zonse zotsala. Ndatero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Mulungu adzaononga Aasiriya

24 Yes. 10.5-34; Nah. 1.1—3.19; Zef. 2.13-15 Chauta Wamphamvuzonse walumbira kuti,

“Monga momwe ndaganizira,

zidzachitikadi choncho,

ndipo monga momwe ndatsimikizira

zidzakhala momwemo ndithu.

25“Ndidzaŵaononga Aasiriya m'dziko langa,

ndipo ndidzaŵapondereza ndi mapazi pa mapiri anga.

Tsono anthu anga ndidzaŵavula goli

limene Aasiriya adaŵaveka,

ndidzaŵachotsera katundu wolemetsa pa mapewa ao.

26“Zimenezi ndizo zimene ndagamula

kuti zidzachitike pa dziko lonse lapansi.

Ndatambalitsa dzanja langa

kuti ndilange anthu a mitundu yonse.”

27Chauta Wamphamvuzonse ndiye watsimikiza

kuti zimenezi zichitike,

nanga ndaninso angathe kumletsa?

Dzanja lake nlotambalitsa,

nanga ndaninso angalibweze?

Mulungu adzaononga Afilisti

28 2Maf. 16.20; 2Mbi. 28.27 Chaka chimene mfumu Ahazi adafa, padamveka ulosi uwu:

29 Yer. 47.1-7; Ezek. 25.15-17; Yow. 3.4-8; Amo. 1.6-8; Zef. 2.4-7; Zek. 9.5-7 “Musakondwe inu anthu a ku Filistiya,

poona kuti adatha Aasiriya

amene adaali ngati ndodo yokumenyani.

Mu mtundu wa njoka wamba mudzatuluka mphiri,

ndipo mu mtundu wa mphiriyo

mudzatuluka chinjoka chaliŵiro chaululu.

30“Osauka zedi adzapeza chakudya,

amphaŵi adzakhala pabwino.

Koma mtundu wanu Afilistinu ndidzauwononga ndi njala,

ndi otsalira omwe ndidzaŵapha.

31“Lirani kwamphamvu inu apachipata!

Pemphani chithandizo mofuula, inu amumzinda!

Njenjemerani ndi mantha nonse Afilisti!

Onani fumbi likuchita kuti kodoo kuchokera kumpoto,

ndipo mwa ankhondo akubwerawo palibe wamantha.”

32Kodi tidzaŵayankhanji amithenga a ku Filistiyawo?

Tidzati, “Chauta adakhazikitsa kale Ziyoni,

ndipo mu mzinda umenewu

anthu ake ozunzika amapeza populumukira.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help