Eks. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kubadwa kwa Mose ndi kupulumuka kwake

1Munthu wina wa fuko la Levi adakwatira mkazi wa fuko lomwelo.

2Ntc. 7.20; Ahe. 11.23 Mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, adamubisa miyezi itatu.

3Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sangathe kumubisanso, maiyo adatenga kadengu kabango, nakamata phula. Tsono mwanayo adamuika m'menemo, nakabisa kadenguko pakati pa bango lalitali m'madzi, pafupi ndi chibumi cha mtsinjewo.

4Ndipo mlongo wake wa mwanayo adaimirira pafupi namangopenyetsetsa, kuti aone zimene zimchitikire mwanayo.

5Nthaŵi ina mwana wamkazi wa Farao adapita kumtsinje komweko kukasamba. Iyeyo anali ndi adzakazi ake, ndipo onsewo ankangoyenda m'mbali mwa mtsinje muja. Tsono mwana wa Farao uja adakaona kadengu kaja m'bangomo, natuma mdzakazi wake kuti akakatenge.

6Atakatsekula kadengu kaja, adapezamo kamwana kakamuna kakungolira. Mtsikanayo adachita nako chifundo kamwanako, ndipo adati, “Kameneka ndi kamwana kachihebri.”

7Apo mlongo wake wa mwanayo adafunsa kuti, “Bwanji ndikakuitanireni mai wachihebri woti akakulerereni mwanayu?” Mwana wa Farao uja adayankha kuti,

8“Chabwino, pita.” Mlongo wakeyo adapita nakaitana amai ake a mwanayo.

9Tsono mwana wa Farao uja adauza maiyo kuti, “Mtengeni mwanayu, mukandilerere, ine ndidzakulipirani.” Motero mai uja adamtenga mwanayo, nakamlera.

10Ntc. 7.21 Mwana uja atakula adakampereka kwa mwana wa Farao, ndipo adasanduka mwana wake ndithu. Mwana wa Faraoyo adamutcha Mose, chifukwa adati, “Ndidamuvuula m'madzi.”

Mose athaŵira ku Midiyani

11 Ntc. 7.23-28 Ahe. 11.24 Tsiku lina Mose, atakula ndithu, adapita kukacheza kwa anthu a mtundu wake uja, ndipo adaona m'mene ankaŵagwiritsira ntchito moŵazunza kwambiri. Adaona Mwejipito wina akumenya Muhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake.

12Pamenepo Mose atayang'ana uku ndi uku, naona kuti kulibe anthu, adamupha Mwejipitoyo, nafotsera mtembo wake mu mchenga.

13M'maŵa mwake atabweranso, adaona kuti Ahebri aŵiri akumenyana. Mose adafunsa wolakwayo kuti, “Chifukwa chiyani ukumumenya mnzako?”

14Iye uja adafunsa Mose kuti, “Kodi ndani adakuika kuti uzitilamula ndi kumatiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga muja udaphera Mwejipito uja?” Pamenepo Mose adachita mantha kwambiri naganiza mumtima mwake kuti, “Ha, anthu akudziŵa zimene ndidachita zija!”

15Ntc. 7.29; Ahe. 11.27 Tsono Farao atamva, adayesetsa kuti aphe Mose, koma Mose adathaŵa nakakhala ku dziko la Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina adakhala pansi pafupi ndi chitsime.

16Amene anali wansembe ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi aŵiri. Ana aakaziwo adabwera kudzatunga madzi, kuti adzaze m'chomwera nkhosa ndi mbuzi za bambo wao.

17Koma kudabwera abusa ena naŵapirikitsa atsikanawo. Apo Mose uja adaimirira naŵathandiza atsikana aja, ndipo adamwetsa zoŵeta zao zonse zija.

18Atsikana atabwerera kwa bambo wao Reuele, bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Bwanji mwabwerako msanga chotere lero?”

19Iwo aja adayankha kuti, “Mwejipito wina ndiye amene watitchinjiriza kwa abusa, ndipo watitungira madzi omwetsa zoŵeta zonsezi.”

20Tsono bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Nanga iyeyo ali kuti? Chifukwa chiyani mwamsiya komweko munthu ameneyo? Pitani mukamuitane, adzadye nao kuno.”

21Choncho Mose adavomera kukhala nao komweko, ndipo Reuele adapatsa Moseyo mwana wake Zipora kuti akhale mkazi wake.

22Zipora adabala mwana wamwamuna. Pamenepo Mose adati, “Ndine mlendo m'dziko lachilendo.” Motero adamutcha mwanayo Geresomo.

23Patapita nthaŵi yaitali ndithu, mfumu ya ku Ejipito ija idamwalira. Monsemo Aisraele ankangolira nawo ukapolo wao uja, namapempha chithandizo, ndipo kulira kwao kudamveka kwa Mulungu.

24Gen. 15.13, 14 Mulungu adamva kudandaula kwaoko, nakumbukira chipangano chake chija chimene adachita ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.

25Mulungu ataŵapenya Aisraelewo, adaŵamvera chifundo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help