Yes. 59 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mneneri adzudzula machimo a anthu

1Chauta si wosoŵa mphamvu,

kuti angalephere kukupulumutsani,

ndipo si gonthi,

kuti nkupanda kumva zimene mukupempha.

2Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu,

ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo.

Choncho saamva zimene inu mumanena.

3Manja anu ali psuu ndi magazi a anthu amene mudapha.

Mudadziipitsa ndi machimo anu ambiri.

Pakamwa panu palankhula zabodza, pamanena zoipa.

4Palibe amene amaimba mnzake mlandu molungama,

palibe wopita ku bwalo lamilandu moona.

Amadalira zopanda pake, amangonena mabodza.

Amangolingalira zamphulupulu,

nachitadi zoipa zimene akuganiza.

5Ziwembu zao nzoopsa ngati mazira a mphiri,

komanso nzosalimba konse ngati ukonde wa kangaude.

Wodya mazira a mphiri amafa.

Likasweka dzira limodzi mumatuluka mphiri.

6Ukonde wa kangaude sangauvale ngati nsalu,

chimene anthu amapangacho sangafunde konse.

Ntchito zao nzoipa

ndipo amakonda kuchita zandeu ndi manja ao.

7 Aro. 3.15-17 Amathamangira kukachita zoipa,

sachedwa kupha anthu osalakwa.

Maganizo ao onse ali pa zoipa.

Kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja,

ndiponso amaononga.

8Kumene kuli iwowo, anthu sapeza mtendere.

Zonse zimene amachita nzopanda chilungamo.

Amayenda m'njira zokhotakhota,

ndipo aliyense woyenda m'njira zimenezo

sadzapeza mtendere.

Anthu alapa machimo ao

9Anthu akuti,

“Chifukwa cha zonsezo

chilungamo chatikhalira kutali,

ndipo kukhala aungwiro nkosatheka.

Timafunafuna kuŵala,

koma timangopeza mdima.

Timayembekeza kuti kudzakhala mbee,

koma kuli bii.

10Timapapasapapasa ngati anthu akhungu,

tili ngati anthu opanda maso.

Timaphunthwa masana ngati usiku.

Ndife amoyo ndithu,

komabe tili ngati anthu akufa.

11Tonse timabangula ngati zimbalangondo,

ndipo timalira modandaula ngati nkhunda.

Timayembekeza kuweruza kolungama,

koma sitikupeza.

Timadikiranso chipulumutso,

koma chili nafe kutali.

12Inu Chauta, takuchimwirani kwambiri.

Machimo athu akutitsutsa,

zolakwa zathu zili pa ife,

ndipo sitingakanepo nchimodzi chomwe.

13Takupandukirani, takukanani,

Inu Chauta,

ndipo takana kukutsatani.

Tapanikiza anzathu, takupandukirani Inu.

Maganizo athu ndi abodza,

mau athu ndi onama.

14Kuweruza kolungama kwalekeka,

ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika.

Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu,

ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko.

15Zoona zikusoŵa kumeneko,

ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa,

amapeza mavuto.”

Chauta akonzekera kuwombola anthu ake

Chauta adaziwona zimenezi

ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo.

16 Yes. 63.5 Chauta adaona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe

adadabwa kuti palibe wochitapo kanthu.

Tsono adapambana ndi mphamvu zakezake,

ndipo adadzilimbitsa ndi kulungama kwake.

17 Lun. 5.17-23; Aef. 6.14, 17; 1Ate. 5.8 Adavala chilungamo

ngati chovala chachitsulo chapachifuwa,

ndipo kumutu kwake adavala chisoti chachipulumutso.

Adavala kulipsira ngati mkanjo,

ndipo mkwiyo udakhala ngati chofunda chake,

18Chauta adzalanga adani a anthu

ake molingana ndi zochita zao:

adzaonetsa ukali kwa omuukira,

ndipo adzalipsira adani ake.

Adzalanga ngakhale okhala m'maiko akutali.

19Motero anthu adzaopa Chauta

kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe.

Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro,

wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.

20 Aro. 11.26 Chauta akuuza anthu ake kuti,

“Ndidzabwera ku Yerusalemu

kudzapulumutsa a fuko la Yakobe

amene adaleka machimo ao.

21“Ndipo ndidzapangana nawo chipangano chakuti, ‘Kuyambira tsopano mpaka muyaya, mzimu wanga umene uli pa iwe, ndiponso mau anga amene ndidaika m'kamwa mwako, sizidzachokeranso m'kamwa mwako kapena m'kamwa mwa ana ako kapena mwa adzukulu ako mpakampaka.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help