1Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe, ndiponso Salome adakagula zonunkhira kuti akadzoze mtembo wa Yesu.
2M'mamaŵa ndithu pa tsiku lotsatira Sabatayo, adapita kumanda kuja, dzuŵa litatuluka.
3Ankafunsana kuti, “Kodi ndani akatichotsere chimwala cha pakhomo pa manda chija?”
4Koma poyang'anitsitsa adaona kuti chimwalacho achigubuduza kale; tsonotu chinali chachikuludi.
5Ataloŵa m'mandamo adaona mnyamata wakhala pansi mbali ya ku dzanja lamanja, atavala mkanjo woyera. Azimaiwo adadzidzimuka.
6Koma mnyamatayo adaŵauza kuti, “Musade nkhaŵa. Mukufuna Yesu wa ku Nazarete, uja adaampachika pa mtandayu. Wauka, sali muno. Taonani, si apa pamene adaamuika.
7Mt. 26.32; Mk. 14.28 Koma inu pitani mukauze ophunzira ake, makamaka Petro, kuti, ‘Iye watsogola kunka ku Galileya. Mukamuwonera kumeneko, monga muja adakuuziranimu.’ ”
8Pamenepo azimaiwo adatuluka nkuthaŵako kumandako, popeza kuti adaagwidwa ndi mantha, mpaka kumangonjenjemera. Ndipo chifukwa cha manthawo sadauze munthu aliyense kanthu.
Yesu aonekera Maria wa ku Magadala(Mt. 28.9-10; Yoh. 20.11-18)[
9Yesu atauka kwa akufa, m'maŵa ndithu, tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, poyambayamba adaaonekera Maria wa ku Magadala, uja adaamtulutsa mizimu yoipa isanu ndi iŵiriyu.
10Mariayo adapita kukauza amene ankakhala ndi Yesu aja. Iwowo nkuti ali ndi chisoni ndipo akungolira.
11Ngakhale atamva kuti Yesu ali moyo, ndipo kuti Maria wamuwona, iwo sadakhulupirire.
Yesu aonekera ophunzira ake aŵiri(Lk. 24.13-35)12Pambuyo pake Yesu, ali ndi maonekedwe osiyana, adaonekera ophunzira ake ena aŵiri, pamene iwowo anali pa ulendo kunja kwa mzinda wa Yerusalemu.
13Ophunzirawo adabwerera kudzauza anzao aja, koma iwonso sadaŵakhulupirire.
Yesu atuma ophunzira ake(Mt. 28.16-20; Lk. 24.36-49; Yoh. 20.19-23; Ntc. 1.6-8)14Potsiriza Yesu adaonekera ophunzira khumi ndi mmodzi aja alikudya. Adaŵadzudzula chifukwa cha kusakhulupirira kwao ndi kupulupudza kwao, chifukwa sadakhulupirire anzao aja amene adaamuwona Iye atauka kwa akufa.
15Ntc. 1.8Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino.
16Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa.
17Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo,
18ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.”
Yesu atengedwa kupita kumwamba(Lk. 24.50-53; Ntc. 1.9-11)19 Ntc. 1.9-11 Ambuye Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita Kumwamba, nakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
20Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.]
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.