1Tsono Solomoni atamaliza kumanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu, ndiponso zonse zimene iye ankafuna kuti amange,
21Maf. 3.5; 2Mbi. 1.7 Chauta adamuwonekera kachiŵiri, monga momwe adaachitira ku Gibiyoni kuja.
3Ndipo Chauta adamuuza kuti, “Ndamva pemphero lako ndi kupemba kwako kumene wachita pamaso panga. Ine ndaipatula Nyumba wamangayi, ndaikamo dzina langa kuti anthu azidzandipembedzeramo mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga zidzakhala m'menemo nthaŵi zonse.
4Kunena za iweyo, ukamayenda pamaso panga mokhulupirika ndi molungama, monga m'mene ankayendera Davide bambo wako, ukamachita zonse zimene ndidakulamula ndi kumvera mau anga ndi malangizo anga,
51Maf. 2.4 pamenepo, Ine ndidzaukhazikitsa mpaka muyaya mpando wako waufumu wolamulira Aisraele, monga momwe ndidalonjezera Davide bambo wako kuti, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pa mpando waufumu wa Israele.’
6Koma iwe ndi ana ako mukapatuka ndi kuleka kunditsata Ine, mukasiya malangizo ndi malamulo anga amene ndidakupatsani, nkuyamba kutumikira milungu ina ndi kumaipembedza,
7pamenepo ndidzaŵachotsa Aisraelewo m'dziko limene ndidaŵapatsa. Ndipo Nyumba ino imene ndaipatulira dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga. Motero Aisraele adzasanduka ngati mwambi ndi chisudzo chabe pakati pa anthu a mitundu yonse.
82Maf. 25.9; 2Mbi. 36.19 Nyumba yotchuka ndi yokomayi idzasanduka bwinja, ndipo aliyense wopitapo adzadabwa nadzaimba likhweru, nkumafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta walichita zotere dzikoli ndiponso Nyumbayi?’
9Tsono azidzati, ‘Nchifukwa chakuti anthuwo adasiya Chauta Mulungu wao, amene adatulutsa makolo ao ku dziko la Ejipito, ndipo adadzifunira milungu ina namaipembedza ndi kumaitumikira. Nkuwona Chautayo waŵachita zoipa zonsezi.’ ”
Mizinda yoperekedwa kwa Hiramu(2 Mbi. 8.1-2)10Ntchito yomanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu idamtengera Solomoni zaka makumi aŵiri.
11Mfumu Hiramu wa ku Tiro ndiye ankapereka kwa Solomoni mitengo ya mkungudza, ya paini, ndiponso golide monga m'mene Solomoni ankazifunira. Ndipo mfumu Solomoni adapatsa Hiramu mizinda makumi aŵiri ya m'dziko la Galilea.
12Hiramu adabwera kuchokera ku Tiro kuti adzaone mizinda imene Solomoni adampatsa, koma sidamkondweretse.
13Nchifukwa chake adafunsa kuti, “Kodi iwe mbale wanga, monga ndi imeneyi mizinda imene wandipatsa?” Choncho imatchulidwa kuti dziko la Kabule mpaka lero lino.
14Hiramu anali atatumiza kwa mfumu golide woposa makilogramu 4,000.
Solomoni achita zinanso zazikulu(2 Mbi. 8.3-18)15Izi ndizo zimene adachita mfumu Solomoni: adalamula anthu kuti agwire ntchito yathangata pomanga Nyumba ya Chauta, nyumba yake, linga lotchedwa Milo kudzanso khoma lozinga Yerusalemu, ndiponso mizinda ya Hazori, Megido ndi Gezere.
16(Farao mfumu ya ku Ejipito anali atalanda mzinda wa Gezere, nautentha. Adaapha Akanani amene ankakhala mumzindamo ndipo adaupereka kuti ukhale mphatso kwa mwana wake wamkazi, uja adaakwatiwa ndi Solomoniyu.
17Choncho Solomoni adachita kuumanganso mzinda wa Gezerewo). Adamanganso mizinda iyi: Betehoroni wakunsi,
18Baalati, ndi Tamara wakuchipululu, m'dziko la Yuda,
19ndiponso mizinda yonse yosungiramo chuma chake ndi magaleta ake, mizinda ya anthu ake okwera pa akavalo, ndiponso chilichonse chimene Solomoniyo ankafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku maiko onse amene iye ankalamulira.
20Koma analipo anthu ena otsalira a mitundu yosiyanasiyana: Aamori, Ahiti, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Ameneŵa sanali Aisraele,
21ndiye kuti zidzukulu zao zotsalira m'dzikomo. Onsewo zimene Aisraele sadathe kuŵaononga kotheratu. Anthu ameneŵa Solomoni ankaŵagwiritsa ntchito yathangata, ndipo akugwirabe ntchito imeneyo mpaka lero lino.
22Koma Aisraele Solomoni sankaŵagwiritsa ntchito yaukapolo. Iwowo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri ankhondo, olamulira ocheperapo a ankhondo, ndiponso oyang'anira magaleta ake, ndi anthu ake okwera pa akavalo.
23Kunali akapitao akuluakulu oyang'anira ntchito za Solomoni. Onsewo analipo 550 ndipo ankayang'anira anthu antchito.
24Nthaŵi imeneyo mwana wamkazi wa Farao adachoka ku mzinda wa Davide napita ku nyumba yake imene Solomoni adammangira. Pambuyo pake Solomoni adamanga linga la Milo.
25 Eks. 23.17; 34.23; Deut. 16.16 Solomoni ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano katatu pa chaka. Ankapereka nsembezo pa guwa limene adamangira Chauta, ndipo ankafukiza lubani pamaso pa Chauta. Choncho ankasamalira zokhudza Nyumbayo.
26Mfumu Solomoni adapanga zombo zambiri ku Eziyoni-Gebere pafupi ndi Elati, pa gombe la Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu.
27Ndipo mfumu Hiramu adatumiza zombo zake pamodzi ndi atumiki ake, ndiye kuti amalinyero odziŵa zam'nyanja, kukagwira ntchito pamodzi ndi anthu a Solomoni.
28Tsono amalinyerowo adapita ku Ofiri, ndipo adakatengako golide wokwanira makilogramu 14,000, nabwera naye kwa mfumu Solomoni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.