1 1Maf. 3.6-9; Lun. 7.7 “Mulungu wa makolo anga, Ambuye achifundo
ndinu amene mudalenga zinthu zonse ndi mau anu.
2Ndi nzeru zanu mudalenga munthu,
kuti azilamulira zolengedwa zonse
zimene Inu mudazipanga,
3kuti aweruze dziko lino lapansi
ndi mtima wangwiro ndi wolungama,
ndipo kuti azigamula milandu mosakondera.
4Mundipatse luntha limene limakhala
pafupi ndi mpando wanu wachifumu,
musandichotse m'gulu la ana anu.
5Ndinedi mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu.
Ndine munthu wofooka ndi wa moyo wochepa.
Ndimangomvetsa pang'ono za chilungamo ndi malamulo.
6Ngakhale munthu akhale wangwiro
pakati pa ana a anthu,
koma popanda luntha lochokera kwa Inu,
anthu adzamuyesa wopanda pake.
7“Ndinu mudandisankhula
kuti ndikhale mfumu ya anthu anu,
ndi kumaweruza ana anu aamuna ndi aakazi.
8Mudandilamula kuti ndikumangireni Nyumba
pa phiri lanu loyera,
ndiponso guwa lansembe
mu mzinda umene Inu mumakhalamo,
potsata chitsanzo cha chihema choyera
chimene mudachikonza poyamba paja.
9Luntha limakhala nanu,
ndipo limadziŵa ntchito zanu.
Linali nanu pamene munkalenga dziko lapansi.
Limadziŵa zimene zili zabwino pamaso panu,
ndi zimene zili zolungama
potsatana ndi malamulo anu.
10Mulitumize kuchokera ku dziko loyera lakumwamba
ndi ku mpando wanu waulemerero,
kuti likhale nane ndi kundithandiza pa ntchito zanga,
ndipo lindidziŵitse zokomera Inu.
11Luntha limadziŵa ndi kumvetsa zonse.
Lidzanditsogolera mochenjera pa ntchito zanga
ndipo lidzanditchinjiriza ndi ulemerero wake.
12Tsono ntchito zanga zidzakhala zovomerezeka,
ndidzaweruza anthu anu molungama,
ndipo ndidzakhala woyenerera
mpando waufumu wa atate anga.
13“Kodi ndani angathe kudziŵa maganizo a Mulungu?
Ndani angathe kuzindikira zimene Ambuye akufuna?
14Nzeru za anthu nzopereŵera,
zolinga zathu nzotha kulephera.
15Chifukwa thupi lodzafali limalemetsa mtima,
nyumba yake yadothiyi imavuta mtima woganiza zambiri.
16Nkwapatali kale kwa ife
kulota zimene zili pansi pano,
ndipo timachita kuvutikira kuti timvetse
ngakhale zimene zili pafupi nafe.
Nanji tsono zimene zili kumwamba,
angazitulukire ndani?
17Ndani angathe kudziŵa kufuna kwanu Ambuye,
mutapanda kumupatsa luntha,
kapena kumutumizira mzimu wanu woyera
kuchokera kumwamba?
18Motero njira za anthu a pansi pano
zidalungamitsidwa,
anthu adaphunzira zimene zimakukomerani,
ndipo adapulumuka chifukwa cha luntha.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.