1Chauta adauza Mose kuti,
2“Lamula Aisraele kuti achotse wakhate aliyense m'zithando, aliyense wotulutsa zinthu zoipa m'thupi mwake, ndiponso munthu wodziipitsa pokhudza mtembo.
3Muchotse anthu onse otere, amuna kapena akazi. Muziŵatulutsira kunja kwa zithando kuti angaipitse zithando zao, poti Ine ndimakhala pakati pa anthu anga.”
4Tsono Aisraele adachitadi zimenezi, ndipo adaŵatulutsira kunja anthuwo. Ankachitadi monga momwe Chauta adaauzira Mose.
Kubweza zinthu za eniake5 Lev. 6.1-7 Chauta adauza Mose kuti,
6“Uza Aisraele kuti, mwamuna kapena mkazi akachita munthu mnzake choipa chilichonse chimene anthu amati wochita zotere ndi wosakhulupirika kwa Chauta, munthuyo ndi wochimwadi.
7Aulule tchimo limene wachimwalo. Abweze zonse zimene adaononga, ndipo aonjeze chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake ndi kupatsa amene adamchimwirayo.
8Koma munthu akapanda kukhala ndi wachibale woti nkulandira zinthu zobwezedwa zija m'malo mwa zoonongedwazo, apereke zobwezedwazo kwa Chauta kuti zikhale za wansembe, kuwonjezera pa nkhosa yamphongo yadipo ija imene amachitira mwambo wopepesera machimo ake.
9Zopereka zonse zopatulika za Aisraele zimene amabwera nazo kwa wansembe, zikhale zake za wansembe.
10Zopereka zopatulika za munthu aliyense, nzake za iye yemweyo. Koma chilichonse chimene munthu apereka kwa wansembe, nchake cha wansembeyo.”
Za mkazi wosakhulupirika11Chauta adauza Mose kuti,
12“Uza Aisraele kuti, mwina mkazi adzazembera mwamuna wake namachita zosakhulupirika.
13Mwamuna wina atachita naye chigololo, zimenezo zitha kubisika, mwamuna wake osazidziŵa. Mkaziyo atha kukhala wosazindikirika kuti wadziipitsa, chifukwa chosoŵa mboni yomtsutsa, popeza kuti sadampezerere akuchita kumene.
14Pamenepo mwamuna wakeyo akayamba kuchitira nsanje mkazi wake amene wadziipitsayo, kapena akayamba kuchitira nsanje mkazi wakeyo ngakhale sadadziipitse,
15mwamunayo abwere ndi mkazi wakeyo kwa wansembe. Ndipo aperekere nsembe ya ufa wabarele wokwanira kilogaramu limodzi. Asathirepo mafuta kapena lubani pa nsembeyo, poti ndi chopereka cha chakudya choperekera nsanje, nsembe yotsutsa munthu, yoperekedwa kuti tchimo lakelo lizidziŵika.
16“Wansembe abwere ndi mkaziyo pafupi ndi kumuimika pamaso pa Chauta.
17Wansembeyo atengeko madzi oyera m'mbiya, ndipo atapeko fumbi la m'Chihema cha Mulungu ndi kulithira m'madzimo.
18Mkaziyo amuimike pamaso pa Chauta ndi kummasula tsitsi, ndipo aike m'manja mwake nsembe yaufa yachikumbutso, chopereka cha chakudya choperekera nsanje ija. Wansembeyo atenge madzi oŵaŵa m'manja mwake, madzi odzetsa matemberero.
19Tsono amlumbiritse mkaziyo kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sadagone nawe, ndipo ngati sudachite kanthu kokuipitsa pamene unali m'manja mwa mwamuna wako, madzi oŵaŵa ali apaŵa usatenge nawo matemberero.
20Koma ngati udamzemberapo mwamuna wako, ngakhale kuti unali m'manja mwake, nudziipitsa, ndipo ngati udagona ndi mwamuna wina wosakhala mwamuna wako,’
21(apo wansembeyo amlumbiritse mkaziyo ndi mau amatemberero, ndi kumuuza kuti), ‘Chauta alisandutse dzina lako matemberero pakati pa anthu a mtundu wako Chauta afwapitse m'chiwuno mwako, ndi kutupitsa thupi lako.
22Madzi ali apa amatembereroŵa aloŵe m'matumbo mwako, atupitse thupi lako, ndipo afwapitse m'chiwuno mwako.’ Tsono mkaziyo avomere kuti, ‘Inde momwemo! Inde momwemo!’
23“Wansembe alembe m'buku matemberero ameneŵa ndipo aŵafafanize poŵaviika m'madzi oŵaŵa aja.
24Mkaziyo ayenera kumwa madzi oŵaŵawo, madzi amatemberero, mpaka aloŵe m'mimba mwake, kuti amve ululu woopsa.
25Apo wansembe achotse m'manja mwa mkaziyo chopereka cha chakudya choperekera nsanje ija. Aipereke moweyula pamaso pa Chauta, ndipo abwere nayo ku guwa.
26Wansembe atapeko ufa wa dzanja limodzi kuti ukhale chikumbutso ndi kuutenthera pa guwa. Pambuyo pake apatse mkaziyo madzi aja kuti amwe.
27Mkazi atamwa madziwo, akakhala kuti adadziipitsa, kapena sadakhale wokhulupirika kwa mwamuna wake, madzi amatemberero aja adzaloŵa m'mimba mwake, ndipo iyeyo adzamva ululu woopsa. Thupi lake lidzatupa, m'chiwuno mwake mudzafwapa, ndipo mkaziyo adzakhala wotembereredwa pakati pa anthu a mtundu wake.
28Koma mkaziyo akakhala kuti sadadziipitse ndipo alibe tchimo, adzakhala wopanda mlandu, ndipo azidzabala ana.
29“Limeneli ndilo lamulo la za nsanje, pamene mkazi azembera mwamuna wake, nadziipitsa, ngakhale kuti ali m'manja mwa mwamuna wakeyo,
30kapena mwamuna akayamba kuchitira mkazi wake nsanje ndipo akumganizira zoipa. Mwamunayo amuimike mkazi wake pamaso pa Chauta, ndipo wansembe amchitire monga momwe lamulo likunenera.
31Mwamuna adzakhala wopanda tchimo lililonse, koma mkazi ndiye adzasenza tchimo lake.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.