2 Mbi. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mneneri Mikaya achenjeza Ahabu(1 Maf. 22.1-28)

1Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemerero waukulu. Tsono adachita chigwirizano chaukwati ndi banja la Ahabu.

2Patapita zaka zina, Yehosafatiyo adapita kwa Ahabu ku Samariya. Ahabuyo adapha nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri kuphera Yehosafatiyo ndi anthu amene anali naye, pofuna kumkopa kuti akalimbane ndi Ramoti-Giliyadi.

3Ndiye Ahabu mfumu ya ku Israele adafunsa Yehosafati mfumu ya ku Yuda kuti, “Kodi udzapita nane limodzi ku Ramoti-Giliyadi?” Iyeyo adayankha kuti, “Ine ndili nanu limodzi, anthu anga nganu. Ifeyo tidzakhala nanu pa nkhondo.”

4Yehosafati adauza mfumu ya ku Israele kuti, “Poyamba upemphe nzeru kwa Chauta.”

5Tsono mfumu ya ku Israele idasonkhanitsa aneneri ake 400, ndipo idaŵafunsa kuti, “Kodi ife tipite kukamenyana nkhondo ndi Ramoti-Giliyadi, kaya kapena ineyo ndileke?” Aneneriwo adamuuza kuti, “Pitani, pakuti Mulungu aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”

6Koma Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi pano palibe mneneri wina wa Chauta woti tipempheko nzeru?”

7Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Alipo wina amene angapemphe nzeru kwa Chauta, dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imila. Koma ine ndimadana naye ameneyo popeza kuti sandilosera zabwino, nthaŵi zonse amangondilosera zoipa.” Tsono Yehosafati adati, “Iyai mfumu, musatero.”

8Apo mfumu ya ku Israele idaitana imodzi mwa nduna nkuiwuza kuti, “Takaitanani Mikaya, mwana wa Imila, abwere kuno msanga.”

9Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo.

10Wina mwa iwo, Zedeki, mwana wa Kenana, adaadzisulira nyanga zachitsulo. Iyeyo adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndi nyangazi udzamegonjetsa Asiriya ndi kuŵaonongeratu.’ ”

11Aneneri onsewo adalosa chimodzimodzi, adati, “Pitani ku Ramoti-Giliyadi, ndipo mukapambana. Chauta aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”

12Wamthenga uja amene adaapita kukaitana Mikaya, adamuuza Mikayayo kuti, “Onani, mau onse amene akunena aneneri, akulosera mfumu zabwino. Ndiye nanunso mau anu akhale ofanafana ndi mau awo. Muzilosa zabwino.”

13Koma Mikaya adati, “Pali Chauta wamoyo, zimene Mulungu wanga andiuze, ndizo ndidzalankhule.”

14Tsono atafika kwa Ahabu, mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi Mikaya, ife tipite kukamenya nkhondo ku Ramoti-Giliyadi, kapena ineyo ndileke?” Iye adayankha kuti, “Pitani, mukapambana, anthuwo akaperekedwa kwa inu.”

15Koma mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi ndikulumbiritse kangati, kuti undiwuze zoona zokhazokha m'dzina la Chauta?”

16Num. 27.17; Ezek. 34.5; Mt. 9.36; Mk. 6.34 Mikaya adati, “Ndidaona Aisraele onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono Chauta adati, ‘Ameneŵa alibe mbuyawo. Aliyense apite kwao mwamtendere.’ ”

17Pamenepo mfumu ya ku Israele adauza Yehosafati kuti, “Suja ndidaakuuzani kuti ameneyu sadzandilosera zabwino koma zoipa zokha?”

18Apo Mikaya adati, “Mverani tsono mau a Chauta. Ine ndidapenya Chauta atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse lakumwamba litaima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere.

19Tsono Chauta adati, ‘Kodi ndani amene akamnyengerere Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akafe ku Ramoti-Giliyadi?’ Wina ankanena zina, winanso nkumanena zina.

20Apo mzimu wina udadzaima pamaso pa Chauta, nunena kuti, ‘Ndikamnyengerera ndine.’ Tsono Chauta adaufunsa kuti, ‘Ukamnyengerera bwanji?’

21Udati, ‘Ndidzapita, nkumakanena zabodza kudzera mwa aneneri ake onse.’ Pamenepo Chauta adati, ‘Ukakatero, ukakhozadi. Pita ukamnyengerere.’

22Tsonotu ngati Chauta waika mzimu wabodza m'kamwa mwa aneneri anuŵa, ndiye kuti Iye yemwe waneneratu kuti mukaona tsoka.”

23Tsono Zedeki uja, mwana wa Kenana, adadza pafupi namenya Mikaya pa tsaya, namufunsa kuti, “Kodi mzimu wa Chauta udadzera njira iti kuti uchoke mwa ine, uzikalankhula ndi iwe?”

24Mikaya adati, “Udzadziŵa pa tsiku limene uzikaloŵa m'chipinda china ndi china cham'kati kuti ukabisale.”

25Pamenepo Ahabu, mfumu ya ku Israele, adati, “Mgwireni Mikayayu, mupite naye kwa Amoni, mkulu wa mzinda, ndiponso kwa Yowasi mwana wa mfumu.

26Mukaŵauze mau angaŵa akuti, ‘Munthu uyu muikeni m'ndende, ndipo muzimpatsa chakudya pang'ono ndi madzi pang'ono, mpaka ine nditabwerera mwamtendere.’ ”

27Mikaya adati, “Mukabwerera mwamtendere, ndiye kuti Chauta sadalankhule kudzera mwa ine.” Ndipo adaonjeza kuti, “Anthu nonsenu, mumve zimene ndanenazi.”

Kufa kwa Ahabu(1 Maf. 22.29-35)

28Zitatero Ahabu, mfumu ya ku Israele, ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adapita ku Ramoti-Giliyadi.

29Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Ine ndidzizimbayitsa, ndipo ndipita kunkhondoko, koma iwe uvale malaya ako aufumu.” Choncho mfumu ya ku Israele idadzizimbayitsa, onsewo nkupita ku nkhondo.

30Mfumu ya ku Siriya nkuti italamula oyendetsa magaleta kuti asamenye nkhondo ndi wina aliyense, wamng'ono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israele basi.

31Tsono pamene oyendetsa magaletawo adaona Yehosafati, adati, “Ndithudi ameneyo ndiye mfumu ya ku Israele.” Choncho adabwerera kudzalimbana naye. Koma Yehosafati adayamba kufuula, ndipo Chauta adamthandiza. Mulungu adaŵabweza m'mbuyo.

32Ndiye kuti oyendetsa magaleta aja ataona kuti ameneyu si mfumu ya ku Israele, adabwerera osamtsatanso.

33Koma munthu wina adakoka uta wake mwachiponyeponye, ndipo adalasa mfumu ya ku Israele pa maluma a malaya ake achitsulo. Pamenepo mfumuyo idauza woyendetsa galeta lake kuti, “Bwerera, undichotse pankhondo pano chifukwa ndavulazidwa.”

34Nkhondo idakula kwambiri tsiku limenelo, mwakuti mfumu ya ku Israeleyo idangokhala tsonga m'galeta lake itayang'anana ndi Asiriya mpaka madzulo. Motero pamene dzuŵa linkaloŵa, idafa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help