1Tsono Tobiyasi adaitana mngelo Rafaele, namuuza kuti,
2“Azariyasi, mbale wanga, tenga antchito anai ndi ngamira ziŵiri, upite ku Ragesi kwa Gabaele. Ukamupatse kalata yachipangano yakeyi.
3Ukatenge ndalama zija, kenaka ubwere naye ku phwando la ukwati wanga.
4Kumbukira kuti bambo wanga wakhala akuŵerenga masiku, ndiye ndikati ndichedwe ngakhale tsiku limodzi, ndidzamuvutitsa. Komabe malumbiro amene Raguele wachita sindingathe kuŵaswa.”
5Motero Rafaele adapita ndi antchito anaiwo ndi ngamira ziŵirizo ku Ragesi, ku dziko la Mediya, nakagona kwa Gabaele. Adamupatsa kalata yake ija, namudziŵitsa kuti Tobiyasi, mwana wa Tobiti, wakwatira, ndipo kuti akumuitana ku phwando laukwati. Pamenepo Gabaele adamuŵerengera matumba a ndalama zija ali ndi zimatiro zosasweka, naŵasenzetsa ngamira zija.
6Ndipo aŵiriwo adanyamuka m'maŵa, napita ku phwando laukwati. Adaloŵa kunyumba kwa Raguele, napeza Tobiyasi atakhala podyera. Iye adadzuka naŵalonjera. Gabaele adalira misozi, nayamika Mulungu. Adati, “Ndiwe mnyamata wabwino kwambiri, mwana wa munthu wolungama ndi wokoma mtima, ndi wothandiza osauka. Ambuye akupatse madalitso akumwamba iwe ndi mkazi wako, atate ako ndi apongozi wako. Atamandike Mulungu chifukwa poona iweyo, ndikuchita ngati ndikuwona msuweni wanga Tobiti.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.