1“Ndife Ayuda okhala ku Yerusalemu ndi m'dziko la Yudeya, tikupereka moni kwa abale athu achiyuda okhala ku Ejipito.
2“Mulungu akupatseni mtendere ndi zabwino zonse. Akumbukire chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, atumiki ake okhulupirika.
3Akupatseni nonsenu mtima wokonda kumpembedza ndi kuchita kufuna kwake molimbika ndi mokondwa.
4Atsekule mitima yanu kuti ivomere mau ake ndi Malamulo ake, ndipo akupatseni mtendere.
5Amvere mapemphero anu ndi kuyanjananso nanu, ndipo asakusiyeni pa nthaŵi ya mavuto.
6Tsopano ife kuno tikukupemphererani.
7“Nthaŵi ya ufumu wa Demetriyo, chaka cha 169, ife Ayuda tidaakulemberani, pamene tinali m'mavuto aakulu, amene adaatigwera zaka zimenezo. Paja nthaŵi imene ija Yasoni ndi gulu lake adaaukira dziko lathu loyera ndi ufumu wathu.
8Adatentha zipata za ku Nyumba ya Mulungu ndi kupha anthu osalakwa. Koma ife tidapemphera kwa Ambuye, Iwo nkutimvera. Tidapereka nsembe ndi zopereka zaufa. Tidayatsanso nyale ndi kuika mitanda ya buledi pamaso pa Ambuye.
9Tsopano tikukulemberaninso kuti mukumbukire masiku a chikondwerero chamahema cha mwezi wa Kisilevi, chaka cha 188.”
Kalata kwa Aristobulo10“Ndife anthu a ku Yerusalemu ndi a ku Yudeya, a bungwe la akuluakulu pamodzi ndi Yudasi, tikupereka moni kwa Aristobulo, wa mtundu wa ansembe odzozedwa, ndi mlangizi wa mfumu Ptolemeyo. Moninso kwa Ayuda okhala ku Ejipito. Tonse tikuŵafunira moyo wabwino.
11“Poti Mulungu adatipulumutsa ku zoopsa zazikulu, tikumthokoza kwambiri chifukwa chotithandiza pa nkhondo yomenyana ndi mfumu.
12Ndi Mulungu yemwe amene adapirikitsa adani aja amene ankafuna kuthira nkhondo mzinda woyera.
13 1Am. 6.1-4; 2Am. 9.1-10 “Ndiye kuti mfumu idapita ku Persiya ndi gulu lankhondo. Gulu lake linkaoneka ngati losapambanika. Komabe iwo adaphedwa m'nyumba ya Naneya, mulungu wao wamkazi, chifukwa ansembe a Naneya adaaŵanyenga ndi mabodza ao.
14Mfumu Antioko idankadi ndi abwenzi ake ku nyumba ya mulungu wamkaziyo kuchita ngati ikufuna kumkwatira. Koma kwenikweni inkangofuna kupata pafupi chonse chuma chake, kukhala ngati choloŵa chake.
15Ansembe a Naneya adachiwonetsa chumacho kwa mfumu, iyo nkuloŵa ndi anthu oŵerengeka m'nyumba ya Naneyayo.
16Antioko ataloŵa, ansembe adatseka pakhomo. Kenaka adatsekula chitseko chobisika cham'mwamba, nayamba kuponya miyala. Adapha mfumu ndi anthu amene anali nayo. Pambuyo pake adaŵachekacheka, naponyera mitu yao anthu amene anali panja.
17Atamandike Mulungu wathu pa zonse, Iye amene adaononga anthu omunyozawo.
18“Popeza kuti tikufuna kuchita chikondwerero cha kuyeretsanso Nyumba ya Mulungu pa tsiku la 25 la mwezi wa Kisilevi, taganiza kuti tikudziŵitseni, kuti inunso muchite chikondwererocho monga chamahema chija. Muzikumbukiranso moto umene Nehemiya adaauwona pamene ankapereka nsembe, iye atamanganso Nyumba ya Mulungu ndi guwa la nsembe.
19Paja pamene makolo athu ankapita ku Persiya, atatengedwa ukapolo, ansembe achifundo a nthaŵiyo adatenga moto pa guwa lansembe, nakaubisa pansi m'chitsime chopanda madzi. Tsono adauphimba mosamala kuti malowo asadziŵike ndi munthu wina aliyense.
20Zitatha zaka zambiri, nthaŵi imene Mulungu adafuna, mfumu ya Persiya idaitana Nehemiya nimtuma ku Yerusalemu. Iye adauza ana a ansembe amene adaabisa moto aja kuti aufunefune motowo. Iwo adafotokoza kuti motowo sadaupeze, adangopeza mafuta achiphalaphala okha.
21Apo Nehemiya adaŵalamula kuti akatapeko mafutawo ndi kubwera nawo kwa iye. Tsono ataika zoperekedwa nsembe pa guwa, Nehemiya adauza ansembe kuti awaze mafuta aja pa nkhuni ndi pa zopereka zoikidwa pamwamba.
22Atatero, padangopita nthaŵi pang'ono, dzuŵa limene linali m'mitambo lidayamba kuŵala. Pomwepo chimoto chidayaka, kotero kuti onse adadabwa kwambiri.
23Pamene nsembe inkapserera, ansembe ndi onse amene anali nawo adapemphera. Yonatani ndiye ankaŵatsogolera, ena onse nkumathira mavume, pamodzi ndi Nehemiya yemwe.
24“Pempherolo linali lotere: Ambuye Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse, woopsa ndi wamphamvu, wolungama ndi woleza mtima, Inu nokha ndinu mfumu, Inu nokha ndinu wachifundo.
25Ndinu nokha mumapatsa zabwino, ndinu nokha wolungama, wamphamvuzonse ndi wamuyaya. Ndinu mumapulumutsa Aisraele ku zoipa zonse. Ndinu mudasankhula makolo athu kuti akhale osankhidwa anu, ndipo mudaŵapatula.
26Landirani nsembeyi m'dzina la anthu anu Aisraele. Muŵasunge ndi kuŵayeretsa.
27Musonkhanitse amene adabalalika uku ndi uku. Mupulumutse amene ali akapolo kwa akunja. Muŵachitire chifundo amene akuzunzidwa ndi kunyozedwa, motero akunja onse adzadziŵe kuti Inu ndinu Mulungu wathu.
28Muŵalange anthu ankhanza ndi onyada amene amatizunza ndi kutichita chipongwe.
29Koma anthu anu muŵakhazike m'malo anu oyera, monga momwe Mose adaaneneratu.
30“Tsono ansembe adaimba nyimbo.
31Zoperekedwa zitapserera, Nehemiya adalamula kuti mafuta otsala aŵawaze pa miyala yaikulu.
32Pompo moto udabuka, koma udazima msanga chifukwa cha kuŵala kochokera pa guwa.
33“Mbiri ya zimenezo idabuka, ndipo adadziŵitsa mfumu ya Apersiya kuti kumalo kumene ansembe otengedwa ukapolo aja adaabisa moto, adapezako mafuta achiphalaphala, ndipo kuti Nehemiya ndi anthu ake mafutawo adayeretsera zoperekedwa nsembe pa guwa.
34Tsono mfumuyo itafufuza nkuwona kuti zonsezo nzoona, idalamula kuti aŵachinge malowo, ndipo adaŵatchula opatulikira Mulungu.
35Malowo ankapindula chuma chambiri ndipo mfumu inkapereka mphatso kwa onse amene adaapeza kuyanja pamaso pake.
36Nehemiya ndi anthu ake adatcha mafutawo dzina loti ‘Nefitara,’ ndiye kuti ‘Kuyeretsa.’ Koma anthu ambiri amaŵatchula kuti, ‘Nafita.’
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.