2 Sam. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kupanduka kwa Sheba.

1 1Maf. 12.16; 2Mbi. 10.16 Zidangochitika kuti kumeneko kunali munthu wina wachabechabe dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini. Iyeyo tsiku lina adaliza lipenga, nati,

“Ife tilibe chathu mu ufumu wa Davide,

tilibe choloŵa mwa mwana wa Yese!

Inu Aisraele, aliyense apite kunyumba kwake!”

2Choncho Aisraele onse adaleka kumtsata Davide, nayamba kutsata Sheba, mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda adakhalabe nganganga pambuyo pa mfumu yao, kuyambira ku Yordani mpaka ku Yerusalemu.

3 2Sam. 16.22 Davide atafika ku nyumba yake ku Yerusalemu, adatenga azikazi ake khumi amene adaaŵasiya kuti azisunga mudzi, naŵatsekera m'nyumba m'mene adaaikamo mlonda woŵalonda. Ankaŵapatsa chakudya, koma Davide sankaloŵa m'nyumbamo kwa akaziwo. Adaŵatsekera m'nyumba choncho mpaka tsiku la kufa kwao, ndipo ankakhala ngati akazi amasiye.

4Tsono mfumu idauza Amasa kuti, “Itanire anthu onse a ku Yuda, abwere kuno pasanapite masiku atatu, ndipo iweyo udzakhalepo.”

5Motero Amasa adakaitana Ayuda. Koma adachedwa, napitiriza nthaŵi imene adaamuikira.

6Pamenepo Davide adauza Abisai kuti, “Sheba, mwana wa Bikiri, adzativuta kwambiri kupambana Abisalomu. Tenga ankhondo anga mulondole Shebayo kuti angadzipezere mizinda yamalinga namativutitsa.”

7Choncho Abisai uja, pamodzi ndi ankhondo a Yowabu, ndi Akereti, ndi Apeleti, ndi anyonga onse, adatuluka ku Yerusalemu kumalondola Sheba, mwana wa Bikiri.

8Nthaŵi imene adafika ku mwala waukulu umene uli ku Gibiyoni, Amasa adabwera kudzakumana nawo. Tsono Yowabu adaavala malaya ankhondo, ndipo pamwamba pa malayawo m'chiwuno mwake, panali lamba womangirirapo lupanga lam'chimake. Pamene ankayenda, lidasololoka.

9Tsono Yowabu adafunsa Amasa kuti, “Kodi nkwabwino mbale wanga?” Pamenepo Yowabuyo adamgwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja kuti amumpsompsone.

10Koma Amasa sadaachenjera nalo lupanga limene linali m'dzanja lina la Yowabu. Pomwepo Yowabuyo adamubaya nalo lupangalo m'mimba kamodzi kokha, mpaka matumbo ake kukhuthuka, naafa pomwepo.

Tsono Yowabu ndi Abisai mbale wake adalondola Sheba mwana wa Bikiri.

11Wina mwa ankhondo a Yowabu adakaimirira pambali pa mtembo wa Amasa, nati, “Aliyense wokhumba Yowabu ndi Davide, mlekeni atsate Yowabuyo.”

12Monsemo nkuti Amasa atagona pa mseu ndi kuvimvinizika m'magazi ake. Ndipo aliyense amene ankabwera, ankati akamuona, nkuima. Tsono munthu wa Yowabu uja ataona kuti anthu akuima, adanyamula Amasa uja, kumchotsa mumseumo, nakamuika ku thengo, nkumfunditsa chovala.

13Amasayo atachotsedwa pamseupo, anthu onse adatsatira Yowabu, kuti alondole Sheba mwana wa Bikiri.

14Sheba adapita ndithu kubzola mafuko onse a Aisraele mpaka kukafika ku Abele wa ku Betemaki. Abikiri onse adasonkhana, naloŵa naye mumzindamo.

15Ndipo anthu onse amene anali ndi Yowabu adabwera, nadzamzinga ndi zithando zankhondo Shebayo ku Abele wa ku Betemaki. Tsono adauundira mitumbira yankhondo mzindawo, nikagunda ku linga. Choncho ankagumula khoma kuti aligwetse.

16Ndiye mkazi wina wanzeru adayamba kuitana mumzindamo kuti, “Tamverani! Tamverani! Tauzani aYowabu abwere kuno kuti ndilankhule nawo.”

17Yowabuyo adadza pafupi ndi mkaziyo, ndipo mkazi uja adamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu aYowabu?” Yowabu adayankha kuti, “Ndine amene.” Mkaziyo adamuuza kuti, “Pepani bambo, mumvere mau anga.” Apo Yowabu adayankha kuti, “Inde, ndilikumva!”

18Apo mkazi uja adati, “Paja anthu kale ankati, ‘Kapempheni nzeru ku Abele.’ Nkhani zao ankazitha motero.

19Ife ndife anthu amtendere ndi okhulupirika m'dziko la Israele. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene uli ngati mai m'dziko la Israele. Chifukwa chiyani mukuti mufafanize choloŵa cha Chauta?”

20Yowabu adayankha kuti, “Iyai, ine sindikufuna konse kuwononga mzinda uno.

21Cholinga si chimenechi. Koma munthu wina wa ku dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri, adaukira mfumu Davide. Mumpereke yekhayo, ndipo mzindawu ndiwuleka.” Mkazi uja adauza Yowabu kuti, “Tikuponyerani mutu wake pa khoma.”

22Kenaka mkaziyo mwa nzeru zake adapita kwa anthu, naŵasimbira nkhaniyi. Choncho anthuwo adadula mutu wa Sheba, mwana wa Bikiri, namponyera Yowabu. Pamenepo Yowabu adaliza lipenga, ndipo ankhondo ake adachoka kumzindako, aliyense kupita kwao, ndipo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu.

Nduna za Davide.

23Yowabu ankalamulira gulu lonse lankhondo la Aisraele. Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, ankalamulira Akereti ndi Apeleti.

24Adoniramu anali mkulu woyang'anira za thangata. Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri ya dziko.

25Seva anali mlembi wa mfumu. Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe.

26Ndipo Ira Myairi nayenso anali wansembe wa Davide.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help