1 Mt. 12.3, 4; Mk. 2.25, 26; Lk. 6.3 Davide adakafika ku Nobu kwa wansembe Ahimeleki. Ahimelekiyo adadzamchingamira akunjenjemera, namufunsa kuti, “Zatani kuti muli nokha popanda ndi mmodzi yemwe wokuperekezani?”
2Davide adayankha kuti, “Mfumu yandituma ndipo yandilamula kuti ndisauze munthu wina aliyense zimene yanditumazo. Kunena za anthu anga, ndapangana nawo kuti tikakumane pa malo ena ake.
3Kodi muli ndi chakudya? Mundipatseko mitanda isanu yabuledi kapena chakudya chilichonse chimene muli nacho pano.”
4Wansembeyo adayankha kuti, “Pano ndilibe buledi wamba, koma alipo ndi buledi wachipembedzo. Ngati anthu anu sadakhale ndi akazi ao, angathe kudya.”
5Davide adayankha kuti, “Kunena zoona, nthaŵi zonse tikakhala pa ulendo, timakhala odzimanga. Anthu anga amakhala odzimanga ngakhale pa ulendo wamba, nanji lero pamene tili pa ulendo woterewu!”
6Lev. 24.5-9 Apo wansembeyo adapereka buledi wachipembedzo kwa Davide, pakuti kunalibe buledi wina, koma buledi yekha woperekedwa kwa Chauta. Buledi wake ndi amene anali atamchotsa pamaso pa Chauta kuti akaikepo wina wamoto.
7Tsiku limenelo munthu wina mwa antchito a Saulo anali pomwepo, pakuti adaayenera kuchita mwambo wachipembedzo ku nyumba ya Chauta. Munthuyo dzina lake anali Doegi Mwedomu, kapitao wa abusa a Saulo.
8Davide adafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi kulibe mkondo kuno kapena lupanga? Paja ine sindidabwere ndi lupanga langa kapena zida zanga chifukwa ntchito ya mfumuyo inali yofulumira.”
91Sam. 17.51Wansembeyo adayankha kuti, “Lupanga la Goliyati Mfilisti uja amene mudamupha ku chigwa cha Ela, nlokulunga m'nsalu paseli pa chovala cha efodi. Ngati mufuna, mungathe kutenga limenelo, chifukwa kulibenso lina kuno, koma lokhalo.” Davide adati, “Palibe lina lofanafana ndi limenelo. Patseni lomwelo.”
10Tsiku lomwelo Davide adanyamuka kuthaŵa Saulo, ndipo adapita kwa Akisi mfumu ya ku Gati.
111Sam. 18.7; 29.5 Tsono nduna za Akisi zidamufunsa Akisiyo kuti, “Kodi ameneyu si Davide, mfumu ya dziko? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankamuimbira kuti,
“ ‘Saulo wapha zikwi, inde,
koma Davide wapha zikwi khumikhumi!’ ”
12 Mas. 56 Mau ameneŵa Davide adamloŵa mu mtima kwambiri, ndipo adayamba kuwopa Akisi mfumu ya ku Gati.
13Mas. 34Choncho adasintha khalidwe lake pamaso pao, nadzisandutsa ngati wamisala, namangolembalemba pa zitseko za chipata, malovu ali chuchuchu kutsikira ku ndevu.
14Tsono Akisi adauza nduna zake kuti, “Mukuwona kuti munthuyu ngwamisala. Chifukwa chiyani tsono mwabwera naye kwa ine?
15Kodi ndikusoŵa anthu amisala kuti muzibwera naye kuno munthu ameneyu, namachita zamisala zake pamaso panga? Ha! Munthu wotereyu angaloŵe bwanji m'nyumba mwanga muno?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.