1 1Ako. 4.16; Afi. 3.17 Muzinditsanzira ine monga momwe inenso ndimatsanzira Khristu.
Za ulemu wa akazi popembedza2Ndikukuyamikani chifukwa mumandikumbukira pa zonse, ndipo mumasunga miyambo imene ndidakusiyirani.
3Koma ndifuna kuti mudziŵe kuti Khristu ndiye mutu wa mwamuna aliyense, mwamuna ndiye mutu wa mkazi, ndipo Mulungu ndiye mutu wa Khristu.
4Ngati mwamuna apemphera kapena kulalika mau a Mulungu, atavala kanthu kumutu, akunyoza mutu wake.
5Koma mkazi akamapemphera kapena kulalika mau a Mulungu, osavala kanthu kumutu, akunyoza mutu wake. Kuteroko sikusiyana ndi kungometa mpala.
6Ngati mkazi sazivala kanthu kumutu, kunali bwino atangodula tsitsi lake. Koma popeza kuti nchamanyazi kwa mkazi kumeta mpala, kapena kudula tsitsi lake, ndiyetu azivala kanthu kumutu.
7Gen. 1.26, 27 Kwa mwamuna palibe chifukwa choti azivalira kanthu kumutu, pakuti amaonetsa maonekedwe ndi ulemerero wa Mulungu. Koma mkazi amaonetsa ulemerero wa mwamuna.
8Gen. 2.18-23 Pajatu mwamuna sadapangidwe kuchokera kwa mkazi, koma mkazi ndiye adapangidwa kuchokera kwa mwamuna.
9Ndiponso mwamuna sadalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi ndiye adalengedwa chifukwa cha mwamuna.
10Tsono, chifukwa cha angelo, mkazi azivala kanthu kumutu, kuti chikhale chizindikiro cha ulemu wake.
11Komabe m'maso mwa Ambuye mkazi sali kanthu popanda mwamuna, ndiponso mwamuna sali kanthu popanda mkazi.
12Inde mkazi adapangidwa kuchokera kwa mwamuna, komanso tsopano mwamuna amabadwa mwa mkazi. Ndipo zinthu zonse zimachokera kwa Mulungu.
13Weruzani nokha ngati nkoyenera kuti mkazi azipembedza Mulungu osavala kanthu kumutu.
14Kodi chibadwa chathu chomwe sichitiphunzitsa kuti nchamanyazi kwa mwamuna kukhala ndi tsitsi lalitali,
15koma kuti kwa mkazi nchaulemu? Mulungu adapatsa mkazi tsitsi lalitali loti aziphimbira mutu wake.
16Tsono ngati wina afuna kutsutsapo pa zimenezi, ndingoti ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe mwambo wina ai ndi womwewu basi.
Za Mgonero wa Ambuye17Tsopano pali mfundo ina imene sindingakuyamikireni. Ndiye kuti misonkhano yanu imabweretsa zoipa osati zabwino ai.
18Choyamba, ndikumva kuti mukamasonkhana mu mpingo, mumapatulana. Ndipo ndikhulupirira kuti zimenezi kwinaku nzoona.
19Nkofunika ndithu kuti pakhale kusiyana maganizo pakati panu, kuti amene ali okhoza pakati panu adziŵike.
20Pamene musonkhana pamodzi, chimene mumadyatu si Mgonero wa Ambuye.
21Inu mumati mukamadya, aliyense angoyambapo kudya chakudya chakechake, kotero kuti wina amakhala ndi njala, m'menemo wina waledzera.
22Zokuwonerani zimenezi! Kodi mulibe nyumba zomakadyeramo ndi kumweramo? Kodi kapena mufuna kunyazitsa Mpingo wa Mulungu ndi kuŵachititsa manyazi amene alibe kanthu, eti? Ndikuuzeni chiyani tsono? Ndingakuyamikeni ngati? Iyai, pa zimenezi sindingakuyamikeni konse.
23Inetu zimene ndidalandira kwa Ambuye ndi zimene nanenso ndidazipereka kwa inu, zakuti usiku umene adaperekedwa uja, Ambuye Yesu adaatenga mkate.
24Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.”
25Eks. 24.8; Yer. 31.31-34; Eks. 24.6-8 Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.”
26Pakuti nthaŵi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso.
27Nchifukwa chake tsono, munthu akadya mkate umenewu, kapena kumwa chikho cha Ambuyechi mosayenera, apalamula mlandu wonyoza thupi la Ambuye ndiponso magazi ao.
28Koma munthu aziyamba wadziwona bwino asanadyeko mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi.
29Pakuti amene adya mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi, koma osalizindikira thupi la Ambuye, akudziitanira chilango pamene akudya ndi kumwa.
30Nchifukwa chake ambiri mwa inu akudwala, akufooka, ndipo ena amwalirapo kale.
31Tikadadziyang'ana bwino, sitikadalangidwa.
32Koma Ambuye amatilanga, kuti tiphunzirepo nzeru, kuwopa kuti tingaimbidwe mlandu pamodzi ndi anthu odalira zapansipano.
33Tsono abale anga, pamene musonkhana kuti mudye Mgonero wa Ambuye, muzidikirana.
34Ngati wina ali ndi njala, ayambe wadya kwao, kuti Mulungu angakulangeni chifukwa cha kusonkhana kwanu. Koma zina zimene sindidatchule, ndidzazilongosola ndikabwera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.