Eza. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chipembedzo chiyambikanso

1Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, ana a Aisraele ali m'midzi mwao, anthu adasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi.

2Eks. 27.1 Pamenepo Yesuwa, mwana wa Zadoki, ndi ansembe anzake, pamodzi ndi Zerubabele, mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, adayamba kumanga guwa la Mulungu wa Aisraele. Adafuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza, monga adalembera m'buku la malamulo a Mose, munthu wa Mulungu uja.

3Num. 28.1-8 Ngakhale kuti ankaopa mitundu ina ya anthu am'maikowo, adamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo ankapereka nsembe zopsereza kwa Chauta paguwapo m'maŵa ndi madzulo.

4Num. 29.12-38 Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe kudalembedwera. Masiku onse ankaperekanso nsembe zopsereza potsata chiŵerengero chake chofunika tsiku ndi tsiku, monga kudalembedwera.

5Num. 28.11—29.39 Pambuyo pake ankapereka nsembe zopsereza monga mwa nthaŵi zonse, nsembe zopereka pokhala mwezi ndi pa masiku onse achikondwerero oikidwa otamandira Chauta, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Chauta.

6Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanunchiŵiri, adayamba kupereka nsembe zopserezazi kwa Chauta. Koma maziko a Nyumba ya Mulungu anali asanamangidwebe.

Ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu iyambika

7Tsono anthu adapereka ndalama kwa amisiri osema miyala ndi kwa amisiri a matabwa. Adatumiza chakudya, zakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi ku Tiro, kuti azigulira mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni. Mitengoyo adafika nayo ku nyanja mpaka ku mzinda wa Yopa. Zonsezi ankazichita potsata chilolezo cha Kirusi, mfumu ya ku Persiya.

8Tsono chaka chachiŵiri atabwera ku Yerusalemu, ku mabwinja kumene kunali Nyumba ya Mulungu yakale, mwezi wachiŵiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele ndiponso Yesuwa mwana wa Yozadaki, adayambapo ntchito pamodzi ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse amene anali atabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo. Adasankha Alevi kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri zakubadwa ndi opitirirapo, kuti aziyang'anira ntchito yomanga Nyumba ya Chauta.

9Yesuwa ndi ana ake kudzanso achibale ake, ndiponso Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, onsewo pamodzi adasenza udindo woyang'anira anthu antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo ana a Henadadi, ndiponso Alevi ndi ana ao ndi achibale ao.

10 1Mbi. 25.1 Tsono amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Chauta, ansembe adadza akuimba malipenga atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, adadza akuimba ziwaya zamalipenga ndi kutamanda Chauta, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraele.

111Mbi. 16.34; 2Mbi. 5.13; 7.3; Mas. 100.5; 106.1; 107.1; 118.1; 136.1; Yer. 33.11 Ankaimba ndi mavume mopolokezana, motamanda ndi mothokoza Chauta. Ankati,

“Chauta ndi wabwino,

chikondi chake pa Israele nchamuyaya.”

Ndipo anthu onse ankafuula kwambiri pamene ankatamanda Chauta chifukwa choti maziko a Nyumba ya Chauta anali akumangidwa.

12Tob. 14.5 Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndi atsogoleri a mabanja, ndiponso nkhalamba zimene zidaaona nyumba yoyamba, adalira mokweza mau, ataona maziko a nyumba imeneyi akumangidwa. Komabe ambirinso ankafuula mokondwa.

13Choncho anthu sankatha kusiyanitsa liwu lofuula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, popeza kuti anthuwo ankafuula kwambiri ndipo liwu la kufuulako linkamveka kutali.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help