Mas. 150 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tamandani Chauta!

1Tamandani Chauta!

Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika.

Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu.

2Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu,

mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.

3Mtamandeni pomuimbira lipenga,

mtamandeni ndi gitara ndi zeze.

4Mtamandeni poimba ng'oma ndi povina,

mtamandeni ndi zipangizo zansambo ndi mngoli.

5Mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira,

mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira kwambiri.

6Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Chauta.

Tamandani Chauta!

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help