1Aejipito adalangidwa ndi zolengedwa zotere
monga kudaŵayenera,
adazunzikadi ndi zilombo zosaŵerengeka.
2 Eks. 16.11-13; Num. 11.31, 32 M'malo mwa chilangocho, mtundu wa anthu anu
mudauchitira chifundo.
Ndipo pofuna kuthetsa nkhuli yao,
mudaŵakonzera zinziri, chakudya chokoma.
3Aejipito aja, ngakhale ankafuna kudya,
ataona tizilombo toŵazunza,
adanyansidwa ndi zakudya zofunika zomwe,
koma anthu anu atamva njala nthaŵi pang'ono,
pambuyo pake adalandirako chakudya chokoma.
4Kunali koyenera kuti njala yaikulu
isautse anthu aja ovuta mtundu wanu,
koma anthu anu mudafuna kuti apenye chabe
mavuto ogwera adani aowo.
Mliri wa dzombe ndi njoka5 Num. 21.6-9 Pamene anthu anu ankasauka ndi ukali wa zilombo
ndipo pamene ankafa, njoka zaululu zitaŵaluma,
mkwiyo wanu sudapitirire.
6Iwo adavutika nthaŵi pang'ono ngati chenjezo chabe,
ndipo adalandira pomwepo chizindikiro
cha chipulumutso, choŵakumbutsa malamulo anu.
7Aliyense amene ankatembenukira chizindikirocho, ankapulumuka.
Sindikuti chimene adachiwonacho
ndicho chidaŵapulumutsa,
koma ndi Inuyo amene muli mpulumutsi wa anthu onse.
8Pakutero mudaonetsa adani athu aja
kuti ndinu amene mumapulumutsa ku zoipa zonse.
9Iwowo adafa chifukwa choŵaluma dzombe ndi nchenche,
osapeza mankhwala opulumutsira moyo wao,
chifukwa anali oyenera kulangidwa choncho.
10Koma ana anu, ngakhale mano a njoka zaululu
sadathe kuŵatsiriza,
chifukwa chifundo chanu
chidzaŵathandiza ndi kuŵachiritsa.
11Adalumidwa kuti azikumbukira mau anu,
mudaŵachiritsa msanga, kuti angakuiŵaleni
ndipo angapande kulandira chithandizo chanu.
12Si masamba, si mankhwala adaŵachiritsa,
koma ndi mau anu, Inu Ambuye,
amene amachiza matenda onse.
13Inu muli ndi mphamvu pa moyo ndi pa imfa,
mumafikitsa anthu ku khomo la imfa,
ndi kuŵabweza kuchokera kumeneko.
14Munthu amene ali woipa mtima
angathe kupha munthu mnzake,
koma sangathe kubweza mpweya utachoka,
kapena kupulumutsa mzimu
utaloŵa m'dziko la akufa.
Matalala ndi Mana15Kuthaŵa dzanja lanu nkosatheka.
16Anthu osamvera, okana kukudziŵani,
adakwapulidwa ndi mphamvu za dzanja lanu.
Mvula yamkuntho ndi yamatalala,
ndiponso mvumbi wosakata, zidaŵasautsa,
ndipo moto udaŵatentha.
17Chinali chinthu chozizwitsa
kuti moto udayaka mwamphamvu
ngakhale m'madzi momwe mozimitsa zonse,
chifukwa zonse zapansipano
zimachirikiza anthu olungama.
18Mwina ukali wa moto unkacheperapo
kuti usapsereze tizilombo todzasautsa osamverawo,
kuti motero adaniwo poona zimenezo,
azizindikira chiweruzo cha Mulungu choŵalondola.
19Mwina moto unkayaka kwambiri
ngakhale m'madzi momwe,
kuti uwononge dzinthu dzonse
dza dziko la anthu osamvera.
20 Eks. 16.1-36 Pamalo pa zimenezi mudadyetsa anthu anu
ndi chakudya cha angelo,
mudaŵatumizira buledi wokonzeka kale
wofumira kumwamba,
popanda iwo kugwirapo ntchito.
Chinali chakudya chosangalatsa
ndi chokomera anthu onse,
ngakhale a kukonda kosiyanasiyana.
21Chakudya chanucho
chinkasonyeza kukoma mtima kwanu kosamalira ana anu.
Chinali chokomera aliyense,
ndipo kukoma kwake kunkasinthika
malinga nkukonda kwa munthu aliyense.
22Chipale ndi chisanu choundana chambee
sizidasungunuke m'moto,
kuti anthu anu azindikire kuti unali moto
woyaka pakati pa matalala
ndi pakati pa mvula,
umene unkaononga dzinthu dza adani ao.
23Koma moto womwewo unkaiŵala khalidwe lake,
kuti olungama zakudya zao zisaonongeke.
24Zoonadi, zolengedwa, potumikira Inu Mlengi wake,
zimalimbikira kuti zilange anthu oipa,
koma zimakhululuka ndi kuŵachitira zachifundo
anthu okhulupirira Inu.
25Choncho, nthaŵi yakaleyo,
potenga maonekedwe osiyanasiyana,
zolengedwazo zinkathandiza ufulu wanu wolera onse,
potsata khumbo la anthu okupemphani.
26Tsono ana anu amene mumaŵakonda, Inu Ambuye,
adatha kuphunzira kuti si zokolola zokha
zimene zingadyetse anthu,
koma ndi mau anu amene amasunga anthu okukhulupirirani.
27Zimene sizidaonongeke ndi moto,
zidasungunuka ndi chitungu cha pakanthaŵi,
cha mwendo umodzi wa dzuŵa.
28Choncho tidziŵe kuti
tiyenera kudzuka ndi kukuyamikani,
dzuŵa lisanatuluke,
ndipo tiyenera kupemphera kwa Inu
nthaŵi yomwe ya mbandakucha.
29Koma munthu wosathokoza, chikhulupiriro chake
chidzasungunuka ngati chipale,
ndi kutayika ngati madzi opanda ntchito.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.