1Nthaŵi imeneyo mfumu Hezekiya adaadwala, ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi, adapita kukamuwona, namuuza kuti, “Chauta akuti ukonze zonse bwino lomwe, poti ufa, suchira ai.”
2Pomwepo Hezekiya adatembenuka nayang'ana ku khoma, nayamba kupemphera kwa Chauta kuti,
3“Inu Chauta, mukumbukire kuti ndakhala ndikukutumikirani mokhulupirika ndi modzipereka. Ndipo nthaŵi zonse ndinali kuchita zokukomerani.” Atatero adayamba kulira ndi mtima woŵaŵa.
4Tsono Chauta adalamula Yesaya kuti,
5“Pitanso kwa Hezekiya, ukamuuze kuti, ‘Ine Chauta, Mulungu wa kholo lako Davide, ndamva pemphero lako, ndipo misozi yako ndaiwona. Nchifukwa chake ndidzakuwonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako.
6Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya, ndipo mzindawu ndidzautchinjiriza.’ ”
7Yesaya adauza Hezekiya kuti, “Chauta adzakupatsani chizindikiro kutsimikiza kuti adzasunga lonjezo lake.
8Akuti, ‘Chithunzithunzi chimene dzuŵa likuchititsa pa makwerero a Ahazi, ndidzachibweza m'mbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzicho chidabwereradi m'mbuyo makwerero khumi.
Nyimbo yothokoza ya Hezekiya.9Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda, amene adaadwala kenaka nkuchira:
10“Ndinkaganiza kuti ndizipita ku dziko la akufa,
ndidakali mnyamata wabiriŵiri,
ndipo kuti ndidzakhala komweko mpakampaka.
11Ndinkaganiza kuti pa dziko lino la anthu amoyo,
sindidzaonanso Chauta,
anthu okhala pansi pano sindidzaŵapenyanso.
12Moyo wanga walandidwa ndi kuchotsedwa,
ngati hema logwetsedwa,
ngati nsalu yodulidwa ku makina ake oombera.
Kuyambira m'maŵa mpaka usiku mwakhala mukunditsiriza.
13Usiku wonse mpaka m'maŵa ndinkalira ndi ululu.
Munkaphwanya mafupa anga onse,
monga umachitira mkango.
Kuyambira m'maŵa mpaka usiku
mwakhala mukunditsiriza.
14“Ndinkalira ngati namzeze wovutika,
ndinkabuula ngati nkhunda yodandaula.
Maso anga adaatopa nkuyang'ana kumwamba.
Inu Ambuye, ndili m'mavuto, dzanditetezeni.
15Kodi ndinganene chiyani?
Chauta walankhula nane,
ndipo wachita zimenezi ndiye amene.
Pa moyo wanga wonse ndidzakhala wovutika,
chifukwa cha kuŵaŵa kwa mtima wanga.
16“Inu Ambuye, anthu amakhala moyo ndi zimenezi,
moyo wa mzimu wanga uli mu zomwezo.
Mundichiritse ndi kundibwezera moyo.
17Chimene ndidamvera zoŵaŵa nkuti ndipeze bwino.
Mwapulumutsa moyo wanga ku manda,
mwataya machimo anga onse kumbuyo kwanu.
18
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.