1Mfumu Davide anali wokalamba kwambiri. Ndipo ngakhale ankamufunditsa mabulangete, sankamvabe kufunda.
2Nchifukwa chake nduna zake zidamuuza kuti, “Inu amfumu, tikupezereni namwali woti azikusungani ndi kumakusamalani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti inu amfumu muzifundidwa.”
3Choncho adafunafuna namwali wokongola m'dziko lonse la Israele, ndipo adapeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.
4Namwaliyo anali wokongola kwambiri. Tsono adakhala wosamala mfumu ndi kumaitumikira. Koma mfumuyo sidakhale naye malo amodzi namwaliyo.
Adoniya adzilonga ufumu5 2Sam. 3.4 Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, adayamba kudzikuza namanena kuti, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Motero adadzipezera magaleta ndi anthu okwera pa akavalo, ndiponso anthu operekeza makumi asanu oti azithamanga patsogolo pake.
6Bambo wake Davide anali asanamdzudzulepo nkamodzi komwe pomufunsa kuti, “Kodi zakutizakutizi ukuchitiranji?” Adoniyayo anali wokongola, ndipo adaapondana ndi Abisalomu.
7Iyeyo adapangana ndi Yowabu, mwana wa Zeruya, ndiponso Abiyatara wansembe. Choncho iwowo adamtsata Adoniya namamthandiza.
8Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso mneneri Natani, Simei, Rei, pamodzi ndi anthu amphamvu aja a Davide, sadamtsate Adoniyayo.
9Tsiku lina Adoniya adapereka nsembe za nkhosa, ng'ombe ndiponso anaang'ombe onenepa ku Mwala wa Njoka umene uli pafupi ndi Enirogele. Adaitana abale ake onse, ana a mfumu, ndi akazembe onse a ku Yuda.
10Koma sadaitaneko mneneri Natani, Benaya, anthu amphamvu aja a mfumu Davide, kapenanso Solomoni mbale wake.
11 2Sam. 12.24 Natani adafunsa Bateseba, mai wa Solomoni, kuti, “Kodi simudamve kuti Adoniya, mwana wa Hagiti, wadzilonga ufumu, chikhalirecho Davide mbuyathu sakuzidziŵa zimenezo?
12Nchifukwa chake tsono ndikupatseni nzeru kuti mupulumutse moyo wanu pamodzi ndi moyo wa mwana wanu Solomoni.
13Pitani msanga kwa mfumu Davide, mukamfunse kuti, ‘Kodi inu mbuyanga mfumu, suja mudandilonjeza molumbira ine mdzakazi wanu, kuti mwana wanga Solomoni ndiye amene adzaloŵe ufumu m'malo mwanu nadzakhala pa mpando wanu m'malo mwanu? Nanga chifukwa chiyani Adoniya waloŵa ufumu?’
14Tsono pamene inu muzikalankhula ndi mfumu, inenso ndidzaloŵa pambuyo panu, kuti ndikachitire umboni mau anuwo.”
15Choncho Bateseba adapita kwa mfumu, nakaloŵa m'chipinda chake. (Apo nkuti mfumuyo itakalamba kotheratu, ndipo Abisagi Msunamu uja ankasamala mfumuyo).
16Bateseba adagwada nalambira mfumu. Tsono mfumu idamufunsa kuti, “Kodi nkwabwino?”
17Bateseba adati, “Ai nkwabwino. Koma mbuyanga, paja inu mudaandilonjeza molumbira ine mdzakazi wanu m'dzina la Chauta Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye amene adzaloŵe ufumu m'malo mwanga, nadzakhala pa mpando wanga.’
18Komabe tsono, onani, Adoniya wadzilonga ufumu, inuyo mbuyanga osazidziŵa zimenezo.
19Iyeyo wapha ng'ombe, anaang'ombe onenepa, ndiponso nkhosa zambiri, kuperekera nsembe, ndipo waitana ana anu onse, wansembe Abiyatara ndiponso Yowabu mkulu wankhondo. Solomoni mwana wanu sadamuitaneko ai.
20Mwakuti tsopano, mbuyanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muŵauze munthu amene adzakhale pa mpando wanu waufumu, m'malo mwanu.
21Mukapanda kutero, zidzachitike nzakuti inu mbuyanga mutatisiya, kulondola kumene kudapita makolo anu, ine pamodzi ndi mwana wanga Solomoni adzatiyesa ogalukira mfumu.”
22Tsono Batesebayo akulankhula ndi mfumu, mneneri Natani adaloŵa.
23Anthu adauza mfumu kuti, “Kwafika mneneri Natani.” Tsono iye atafika pamaso pa mfumu, adaŵeramitsa mutu wake pansi.
24Ndipo adafunsa mfumu kuti, “Mbuyanga mfumu, kodi inu mudalengeza zoti Adoniya ndiye adzakhale mfumu ndi kukhala pampando panu?
25Pakuti lero lomwe lino wakapha ng'ombe, anaang'ombe onenepa, ndi nkhosa zambiri, kuperekera nsembe. Ndipo waitana ana anu onse pamodzi ndi Yowabu mkulu wa ankhondo, ndi wansembe Abiyatara. Onsewo akudya ndi kumwa naye Adoniyayo tsopano lino, ndipo akunena kuti, ‘Adzachite kufa ndi ukalamba mfumu Adoniya.’
26Koma ine mtumiki wanu, wansembe Zadoki ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso Solomoni mwana wanu, tonsefe sadatiitaneko.
27Kodi zimenezi mwalamula ndinu mbuyanga mfumu? Bwanji nanga simudauze anthu anu za mwana amene adzakhale pa mpando wanu waufumu m'malo mwanu?”
Solomoni alongedwa ufumu28Apo mfumu Davide adati, “Mundiitanire Bateseba, abwere kuno.” Bateseba adaloŵa, nakaimirira pamaso pa mfumu.
29Ndipo mfumu idalumbira kuti, “Pali Chauta wamoyo, amene adapulumutsa moyo wanga ku mavuto onse,
30monga momwe ndidaakulonjezera molumbira m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, kuti mwana wako Solomoni ndiye amene adzaloŵe ufumu ndi kukhala pa mpando wanga, m'malo mwanga, ndikubwerezanso zomwezo lero.”
31Pomwepo Bateseba adaŵeramitsa mutu wake pansi nalambira mfumu, nati, “Mbuyanga mfumu Davide akhale ndi moyo mpaka muyaya!”
32Pamenepo mfumu Davide adati, “Mundiitanire wansembe Zadoki, mneneri Natani, ndi Benaya mwana wa Yehoyada.” Onsewo adafika pamaso pa mfumu.
33Tsono mfumu idaŵauza kuti, “Tengani anthu anga, ndipo mukweze Solomoni mwana wanga pa bulu wanga, mupite naye ku Gihoni.
34Kumeneko wansembe Zadoki ndi mneneri Natani akamdzoze kuti akhale mfumu yolamulira Israele. Kenaka mukalize lipenga, ndi kufuula kuti, ‘Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni.’
35Tsono inu muzikamtsata pambuyo pobwerera kuno, kudzakhala pa mpando wanga waufumu. Iyeyo ndiye akhale mfumu m'malo mwanga. Ndamsankha iyeyo kuti akhale wolamulira Israele ndi Yuda.”
36Apo Benaya mwana wa Yehoyada adayankha kuti, “Indedi, zichitikedi motero. Chauta, Mulungu wa mbuyanga mfumu, akwaniritse zimenezi.
37Monga momwe Chauta wakhalira nanu mbuyanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni, ndipo ufumu wake aukweze ndithu, ngakhale kupambana ufumu wanu, mbuyanga mfumu Davide.”
38Tsono wansembe Zadoki, mneneri Natani ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso Akereti ndi Apeleti oteteza mfumu aja, adapita nakamkweza Solomoni pa bulu wa mfumu Davide, kupita naye ku Gihoni.
39Kumeneko wansembe Zadoki adatenga nsupa ya mafuta ya ku hema la Chauta, nadzoza Solomoni. Pomwepo adaliza lipenga, ndipo anthu onsewo adafuula kuti, “Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni!”
40Anthuwo adapita namamtsatira pambuyo akuliza zitoliro ndi kukondwerera kwambiri, kotero kuti dziko lidagwedezeka chifukwa cha phokosolo.
41Pamene Adoniya ndi anthu onse oitanidwa amene anali naye ankamaliza madyerero ao, adalimva phokosolo. Yowabu atamva kulira kwalipenga, adafunsa kuti, “Kodi phokoso limeneli mumzindamo, kwachitikanji?”
42Akulankhulabe, adangoona Yonatani mwana wa wansembe Abiyatara wafika. Adoniya adamuuza kuti, “Loŵa, chifukwa ndiwe munthu wabwino, mwina mwake wabwera ndi uthenga wabwino.”
43Tsono Yonatani adayankha kuti, “Iyai, zinthu zaipa uku! Mbuyathu mfumu Davide walonga Solomoni ufumu.
44Adatuma wansembe Zadoki, mneneri Natani, ndi Benaya mwana wa Yehoyada ndiponso Akereti ndi Apeleti ku Gihoni. Ndipo iwo adamkweza Solomoniyo pa bulu wa mfumu.
45Tsono Zadoki wansembe uja ndi mneneri Natani adamdzoza Solomoni ku Gihoniko kuti akhale mfumu. Ndipo kuchokera kumeneko akhala akukondwerera, kotero kuti mumzinda monse muli phokoso. Ndiye lumbwe mwamvali.
46Solomoni wakhala pa mpando waufumu.
47Kuwonjezera pamenepo, nduna za mfumu zidadzamuyamika mbuyathu mfumu Davide nkumanena kuti, ‘Mulungu wanu akweze dzina la Solomoni kupambana dzina lanu, ndipo akweze ufumu wake kupambana ufumu wanu.’ Ndipo mfumu idaŵerama niyamba kupemphera pa bedi.
48Idati, ‘Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene lero walola kuti mmodzi mwa ana anga akhale pa mpando wanga waufumu, ine ndemwe ndikuwona.’ ”
49Pomwepo anthu onse amene Adoniya adaaŵaitana aja adayamba kunjenjemera, ndipo adamwazikana aliyense kumapita kwao.
50Pamenepo Adoniya adayamba kuwopa Solomoni. Adapita ku Nyumba ya Mulungu nakagwira nsonga za guwa lansembe.
51Tsono ena adauza Solomoni kuti, “Adoniya akukuwopani, inu mfumu Solomoni, ndipo wakagwira nsonga za guwa lansembe, ndipo akunena kuti poyamba afuna kuti inu mfumu Solomoni mulumbire kuti simudzamupha mtumiki wanuyo.”
52Solomoni adati, “Iyeyo akakhala womvera, sitimchita choipa chilichonse, koma akakhala woipa mtima, adzafa basi.”
53Kenaka mfumu Solomoni adatuma anthu kukamtenga Adoniya kuguwa kuja. Iye adabwera kudzalambira mfumu Solomoni. Ndipo Solomoni adamuuza kuti, “Chabwino, ungathe kupita kunyumba kwako.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.