Ahe. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za chikhulupiriro cha anthu akale

1Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu.

2Mphu. 44.10—50.21; 1Am. 2.51-64Pokhala ndi chikhulupiriro, makolo anthu akale aja Mulungu adaonetsa kuti ankakondwera nawo.

3 Gen. 1.1; Mas. 33.6, 9; Yoh. 1.3 Pokhala ndi chikhulupiriro timamvetsa kuti zonse zimene zilipo zidalengedwa ndi mau a Mulungu, mwakuti zinthu zoonekazi zidachokera ku zinthu zosaoneka.

4 Gen. 4.3-10 Pokhala ndi chikhulupiriro, Abele adapereka kwa Mulungu nsembe yopambana ya Kaini, navomerezedwa kuti ngwolungama, chifukwa Mulungu mwiniwake adaamchitira umboni pakulandira zopereka zake. Mwakuti ngakhale iye adafa, koma chifukwa cha chikhulupiriro chakecho, akulankhulabe mpaka pano.

5 Gen. 5.21-24; Mphu. 44.16 Pokhala ndi chikhulupiriro, Enoki adatengedwa kupita Kumwamba, osafa konse. Sadapezekenso, popeza kuti Mulungu adamtenga. Malembo amamchitira umboni kuti asanatengedwe, anali wokondweretsa Mulungu.

6Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.

7 Gen. 6.13-22 Pokhala ndi chikhulupiriro, Nowa adalandira machenjezo a Mulungu onena za zinthu zomwe mpaka nthaŵi imeneyo zinali zisanaoneke. Adamvera, napanga chombo kuti apulumutse onse a m'banja mwake. Potero adaŵatsutsa kuti ngolakwa anthu a dziko lapansi, nalandira chilungamo chimene Mulungu amapatsa anthu omkhulupirira.

8 Gen. 12.1-5 Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu adamvera pamene Mulungu adamuitana kuti apite ku dziko lina limene adaamlonjeza kuti lidzakhala lake. Ngakhale sankadziŵa kumene ankapita, adapitabe.

9Gen. 35.27 Pokhala ndi chikhulupiriro chomwecho, ankakhala ngati mlendo m'dzikolo limene Mulungu adaamlonjeza. Ankakhala m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobe, amene nawonso anali atalandira lonjezo lomwelo la Mulungu.

10Monsemo Abrahamu ankadikira mzinda wa maziko okhazikika. Mzindawo, Mmisiri woganiziratu mamangidwe ake ndiponso woumanga, ndi Mulungu.

11 Gen. 18.11-14; 21.2 Pokhala ndi chikhulupiriro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika.

12Gen. 15.5; 22.17; 32.12 Nchifukwa chake mwa munthu mmodzi, wotinso anali ngati wakufa, mudatuluka mibadwo yochuluka ngati nyenyezi, ndi yosaŵerengeka ngati mchenga wa pa gombe la nyanja.

13 Gen. 23.4; 1Mbi. 29.15; Mas. 39.12 Onseŵa adasunga chikhulupiriro chao mpaka kufa. Sadalandire zimene Mulungu adaaŵalonjeza, koma adangoziwonera chapatali ndi kuzikondwerera. Adaavomera kuti pansi pano analidi alendo osakhazikika.

14Paja anthu olankhula motere, amaonekeratu kuti akufunafuna malo ao enieni okhazikikamo.

15Akadakhala kuti ankaganizirako za kudziko kumene adaachokera, bwenzi atapeza danga lakuti abwerere kwakaleko.

16Koma monga zilirimu tikuwona kuti ankafuna dziko lina, lokoma kopambana, ndiye kuti dziko la Kumwamba. Nchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wao, popeza kuti Iye adaŵakonzera mzinda.

17 Gen. 22.1-14 Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu, pamene Mulungu adamuyesa, adapereka Isaki ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu adaampatsa lonjezo, adakhala wokonzeka kupereka ngati nsembe mwana wake mmodzi yekhayo.

18Gen. 21.12 Za mwana ameneyu Mulungu anali atanena kuti, “Mwa Isaki udzakhala ndi zidzukulu.”

19Abrahamu ankakhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa munthu kwa akufa. Tsono tingathe kunena mofanizira kuti adamlandiranso Isakiyo ngati wouka kwa akufa.

20 Gen. 27.27-29, 39, 40 Pokhala ndi chikhulupiriro, Isaki adapemphera ana ake, Yakobe ndi Esau, madalitso am'tsogolo.

21 Gen. 48.1-20; Gen. 47.31 Pokhala ndi chikhulupiriro, Yakobe pakufa, adadalitsa ana a Yosefe mmodzimmodzi. Pochita zimenezi anali atayedzamira pa ndodo yake, akupembedza Mulungu.

22 Gen. 50.24, 25; Eks. 13.19 Pokhala ndi chikhulupiriro, Yosefe ali pafupi kutsirizika, adanenapo za kutuluka kwa Aisraele mu Ejipito, naŵauziratu za m'mene adaayenera kudzachitira ndi mafupa ake.

23 Eks. 2.2; Eks. 1.22 Pokhala ndi chikhulupiriro, atabadwa Mose, makolo ake adamubisa miyezi itatu, poona kuti mwana waoyo anali wokongola. Sadaope konse lamulo lamphamvu la mfumu.

24 Eks. 2.10-12 Pokhala ndi chikhulupiriro, Mose atakula adakana kutchedwa mdzukulu wa Farao, mfumu ya ku Ejipito.

25Iye adasankha kuzunzikira nawo limodzi ana a Mulungu, koposa kukondwerera zosangalatsa za uchimo kanthaŵi pang'ono.

26Adaaona kuti kuzunzika chifukwa cha Wodzozedwa wa Mulungu kunali chuma chachikulu koposa chuma chonse cha ku Ejipito, pakuti maso ake anali ndithu pa mphotho yakutsogolo.

27Pokhala ndi chikhulupiriro, Mose adachoka ku Ejipito, osaopa ukali wa mfumu, popeza kuti ankapirira ngati munthu woona Mulungu wosaonekayu.

28Eks. 12.21-30 Pokhala ndi chikhulupiriro, adachita nawo chikondwerero cha Paska, nalamula kuti anthu awaze magazi pa zitseko kuti mngelo woononga ana achisamba uja asakhudze ana achisamba a Aisraele.

29 Eks. 14.21-31 Pokhala ndi chikhulupiriro, Aisraele adaoloka Nyanja Yofiira ngati pamtunda pouma. Koma Aejipito, kuti nawonso ayesere kuwoloka, adamizidwa.

30 Yos. 6.12-21 Pokhala ndi chikhulupiriro, malinga a mzinda wa Yeriko adagwa, Aisraele ataŵazungulira masiku asanu ndi aŵiri.

31Yos. 6.22-25; Yos. 2.1-21 Pokhala ndi chikhulupiriro, Rahabu, mkazi wadama uja, sadafe nawo limodzi anthu osamvera aja, pakuti adaaŵalandira bwino azondi aja kunyumba kwake.

32 Owe. 6.11—8.32; Owe. 4.6—5.31; Owe. 13.2—16.31; Owe. 11.1—12.7; 1Sam. 16.1—1Maf. 2.11; 1Sam. 1.1—25.1 Kodi ndinenenso chiyani tsopano? Nthaŵi yachepa yoti ndinene za anthu enanso ambiri monga Gideoni, Balaki, Samisoni, Yefita, Davide, Samuele ndiponso aneneri.

33Dan. 6.1-27 Pokhala ndi chikhulupiriro anthu ameneŵa adagonjetsa maufumu, adakhazikitsa chilungamo, ndipo adalandira zimene Mulungu adaaŵalonjeza. Ena adapuya mikango pakamwa,

34Dan. 3.1-30 ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.

351Maf. 17.17-24; 2Maf. 4.25-37; 2Am. 6.18—7.42 Akazi ena adalandiranso anthu ao amene adafa, ataŵaukitsa.

Ena adazunzidwa koopsa mpaka kufa, osalola kuti aŵamasule, chifukwa chofuna kudzaukanso ndi moyo wabwino kopambana.

361Maf. 22.26, 27; 2Mbi. 18.25, 26; Yer. 20.2; 37.15; 38.6 Ena, anthu adaŵaseka ndi kuŵakwapula. Adamangidwa ndi maunyolo naponyedwa m'ndende.

372Mbi. 24.21 Ena adaŵapha pakuŵaponya miyala; ena adaŵacheka pakati; ndipo ena adaŵapha ndi lupanga. Ankayenda uku ndi uku atavala zikopa zankhosa kapena zambuzi, umphaŵi wokhawokha, anthu nkumaŵazunza ndi kuŵavutitsa.

38Anthu ameneŵa, pansi pano sipadaŵayenere! Ankangoyenda m'zipululu ndi m'mapiri namabisala m'mapanga ndi m'maenje apansi.

39Anthu onseŵa, ngakhale adaaŵachitira umboni wokoma chifukwa cha chikhulupiriro chao, sadalandire zimene Mulungu adaalonjeza.

40Ndiye kuti Mulungu anali ataganiziratu zotikonzera zabwino zopambana, kotero kuti sadafune kuti anthu onse aja asafikire ku ungwiro popanda ife.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help