Mphu. 41 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za imfa

1Iwe imfa, kukumbukira iwe nkoŵaŵa kwambiri

kwa munthu amene ali pa mtendere

pakati pa chuma chake,

munthu amene alibe zomdetsa nkhaŵa,

amene zonse zikumuyendera bwino,

amenenso akali ndi mphamvu

zokondwerera chakudya chake.

2Iwe imfa, kufika kwako nkokomera munthu wosauka

ndi wopanda mphamvu,

wokalamba kwambiri ndi wodera nkhaŵa zinthu zambiri,

wokhumudwa ndi wosathanso kupirira.

3Usachite mantha ndi lamulo lakuti udzafa.

Kumbukira amene adafa iwe uli moyo

ndipo amene adzafa iwe utafa kale.

4Ndi lamulo la Ambuye kuti zinthu zonse zamoyo zidzafa,

koma iwe ungatsutsane bwanji ndi kufuna kwa

Mulungu Wopambanazonse?

Ngakhale ukhale ndi moyo zaka khumi, zana kapena chikwi,

m'manda sadzakufunsa kanthu pa zimenezi.

Za chilango cha anthu oipa

5Ngoipitsitsa ana a anthu ochimwa,

amene amaleredwa pakati pa anthu osalabadako za Mulungu.

6Chuma cholandira ana otereŵa chidzatha,

zidzukulu zaonso zidzakhala zotsutsidwa nthaŵi zonse.

7Munthu wosapembedza Mulungu ana ake

adzamloza chala,

poti iwo omwe ngonyozeka chifukwa cha bambo waoyo.

8Tsoka kwa inu anthu osapembedza Mulungu,

inu amene mudasiya Malamulo a Mulungu Wopambanazonse.

9Mukabadwa, mwabadwira matemberero,

mukadzafa, mudzakhalabe otembereredwa.

10Chimene chimachokera m'nthaka,

chidzabwerera kunthaka komweko,

chimodzimodzinso anthu osapembedza Mulungu,

amachoka m'matemberero kukagwa m'chiwonongeko.

11Anthu amalira akufa ao,

koma ndi dzina lomwe loipa la munthu wochimwa lidzaiŵalika.

12Samalirani mbiri yanu,

chifukwa idzakhala nanu nthaŵi yaitali

kupambana matumba chikwi chimodzi a golide.

13Masiku a moyo wabwino ngoŵerengeka,

koma mbiri yabwino imakhala mpaka muyaya.

Za mtima wa manyazi

14Ana anga, sungani malangizo anga,

ndipo mudzakhala ndi mtendere.

Nzeru zobisika zili ngati chuma chobisika,

ziŵiri zonsezi zilibe phindu.

15Ndi bwino kubisa uchitsiru,

koposa kubisa nzeru.

16Tsono malangizo angaŵa muŵamvere ndi ulemu.

Si manyazi aliwonse amene muyenera kukhala nawo,

ndiponso si anthu onse angathe kuweruza zinthu moyenera.

17Mkhalidwe wadama uzichita nawo manyazi

pamaso pa atate ako kapena amai ako.

Mabodza uzichita nawo manyazi

pamaso pa kalonga kapena mfumu.

18Zochimwa zako uzichita nazo manyazi

pamaso pa mtsogoleri kapena woweruza milandu.

Zolakwa zako uzichita nazo manyazi

pamaso pa mpingo.

Zinthu zosalungama uzichita nazo manyazi

pamaso pa anzako kapena abwenzi ako.

19Ngati waba, uzichita manyazi pamaso pa anthu

oyandikana nawo.

Uzichita manyazi ngati udaphwanya lonjezo kapena

chipangano.

Uzichita manyazi ndi mazoloŵero aumbombo pakudya.

Uzichita manyazi ukapereka kapena kulandira

kanthu moderera.

20Uzichita nako manyazi kukana kumbwezera

moni kwa mnzako,

kapena kuyang'anitsitsa mkazi wadama.

21Uzichita nako manyazi kufulatira wachibale,

kapena kulanda wina zimene zili zake,

kapena kupenyetsetsa mkazi wamwini.

22Uzichita nako manyazi kuseŵera ndi mdzakazi

wa munthu wina,

usayerekeze kuyandikira bedi lake.

Uzichita nako manyazi kutonza abwenzi ako,

kapena kuŵanyoza utaŵapatsa kanthu.

23Uzichita nako manyazi kubwerezabwereza mphekesera,

kapena kuulula zinsinsi za anthu ena.

Ukatero udzakhala ndi manyazi oyenera,

ndipo anthu onse adzakukomera mtima.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help