1Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi, chaka chachisanu ndi chinai cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2
“Iwe mwana wa munthu, lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino. Lero ndilo tsiku limene mfumu ya ku Babiloni yazinga Yerusalemu ndi zithando zankhondo.
3Uŵaphere mwambi anthu aupanduŵa. Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti,
“ ‘Ikani mphika pa moto,
ndipo muthiremo madzi.
4Mumphikamo muikemo nthuli za nyama,
nthuli zabwino kwambiri
za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba.
Mudzazemo mafupa abwino.
5Pa gulu la nkhosa musankhulepo nkhosa yabwino kwambiri,
ndipo muike nkhuni pansi pa mphikawo.
Madziwo aŵire,
kenaka muphike nyama ija pamodzi ndi mafupa omwe’.
6“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa mzinda wamagaziwe, tsoka kwa mphika wa dzimbiri lokangamira ndi losachoka. Mutulutsemo nthuli imodziimodzi, osasankhula.
7Magazi amene adakhetsa mumzindamo akadali pakati pake, chifukwa adaŵataya pa thanthwe losalala osati pa dothi, kuti fumbi lingaŵafotsere.
8Ndidaŵasiyadi magaziwo pa mwala wambee, kuti asafotsereke, chifukwa chofuna kuwonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira.
9“Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, Tsoka kwa mzinda wamagaziwo! Inenso ndidzayatsa chimulu chachikulu cha nkhuni.
10Onjeza nkhuni, usonkhe moto, uphike nyama, uiphike bwino, utsanyule msuzi, ndipo upsereze mafupa.
11Tsono uike pa makala mphika wopanda kanthuwo, kuti chitsulo chake chipse, kuchita kuti psuu. Zonyansa zake zonse zisungunuke, dzimbiri lichoke.
12Koma nkuuyeretsa bwanji? Dzimbiri lake lidaloŵerera, silingathe kuchoka ngakhale ndi moto womwe.
13Dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako, poti nditakutsuka sudayere. Tsono sudzayeranso mpaka mkwiyo wanga utakwaniratu pa iwe.
14Ine Chauta ndalankhula zimenezi. Zilikudza ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera m'mbuyo, sindidzakulekerera kapena kukhululuka ai. Ndidzakulanga potsata makhalidwe ako ndi zimene udachita. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Imfa ya mkazi wa Ezekiele15Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti,
16“Iwe mwana wa munthu, ndikulanda mwadzidzidzi mkazi wako amene amakukomera m'maso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi.
17Udzume, koma m'chikatikati, usabume maliro. Nduŵira yako uvale ndithu, nsapatonso uvale. Usaphimbe kumaso kapena kudya chakudya cha olira.”
18Choncho ndidalankhula ndi anthu m'maŵa, madzulo mkazi wanga nkumamwalira. M'maŵa mwake, ndidachita monga momwe adandilamulira.
19Anthu adandifunsa kuti, “Bwanji osatifotokozera tanthauzo lake la zimene ukuchitazi? Kodi ukuchitiranji zotere?”
20Ndidaŵayankha kuti, “Chauta adandipatsira uthenga uwu, adati,
21‘Uza Aisraele mau anga akuti, Ndidzaipitsa Nyumba yanga imene mwakhala mukuinyadira kwambiri. Mumakondwa kwambiri poiwona, ndipo mumaikonda ndi mtima wonse. Ana anu aamuna ndi aakazi amene mudaŵasiya m'mbuyo, adzaphedwa ndi lupanga.’
22Koma inu mudzachita monga ndachitira inemu. Simudzaphimba kumaso, kapena kudya chakudya cha anthu olira.
23Nduŵira mudzavala ndithu ku mutu, nsapatonso mudzavala. Simudzalira maliro kapena kukhetsa misozi. Koma mudzavutika zedi chifukwa cha machimo anu, ndipo muzidzangodzumirana.
24Tsono ine Ezekielene ndidzakhala chitsanzo kwa inu, mudzachita monga momwe ine ndachitira. Chauta akuti zimenezi zikadzachitika, mudzadziŵa kuti Iye ndi Ambuye Chauta.”
25Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsiku lina anthuŵa ndidzaŵachotsera linga lao limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkaŵakomera m'maso poliwona, limenenso ankaikapo mtima kwambiri. Ndidzaŵachotseranso ana ao aamuna ndi aakazi.
26Pa tsiku limenelo wopulumuka adzabwera kudzakuuza zimenezo.
27Pa tsiku lomwelo udzathanso kulankhula, choncho udzalankhula naye wopulumukayo, sudzakhalanso bububu. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.