2 Pet. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za aneneri ndi aphunzitsi onyenga

1Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga.

2Ambiri adzatsata mkhalidwe wodzilekerera ndipo anthu adzanyoza njira ya choona chifukwa cha iwowo.

3Chifukwa chokondetsa chuma, iwo adzayesa kupeza phindu pakukuuzani mau onyenga. Komatu chilango chao nchokonzeratu kale, ndipo chiwonongeko chao chikuŵadikira.

4Pakuti Mulungu sadaŵalekerere angelo amene adachimwa aja, koma adaŵaponya m'ng'anjo yamoto, m'maenje amdima momwe ali omangidwa kudikira chiweruzo.

5Gen. 6.1—7.24; Lun. 10.4 Mulungu sadaŵalekererenso anthu akale aja, koma adangosunga Nowa yekha, mlaliki wa chilungamo, pamodzi ndi anzake asanu ndi aŵiri, pamene adadzetsa chigumula pa dziko la anthu osasamala za Iye Mulunguyo.

6Gen. 19.24 Ndiponso Mulungu adaweruza mzinda wa Sodomu ndi wa Gomora naiwononga ndi moto, kuti chimenechi chikhale chitsanzo chochenjeza anthu amene adzakhale osasamala za Mulungu.

7Gen. 19.1-16; Lun. 10.6-8Koma adapulumutsa Loti munthu wolungama, amene ankavutika ndi makhalidwe odzilekerera a anthu ochimwa aja.

8Munthu wolungama uja, pokhala pakati pao, analikumva ndi kuwona machitidwe ao oipa, ndipo tsiku ndi tsiku mtima wake wolungama unkavutikadi.

9Ndiye kuti pamene anthu osamala za Mulungu akuyesedwa, Iye amadziŵa kuŵapulumutsa kwake. Koma amadziŵanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo.

10Makamaka adzalanga anthu amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi namanyoza ulamuliro.

Aphunzitsi onyenga ndi odzikuza, osasamala munthu, saopa kuchita chipongwe aulemerero a Kumwamba.

11Chonsecho ngakhale angelo, amene ali aakulu ndi amphamvu kuposa aphunzitsi onyengaŵa, sanyazitsa aulemererowo pamaso pa Ambuye.

12Koma anthu aŵa ali ngati nyama chabe, zolengedwa zopanda nzeru, zobadwira kuti zizigwidwa ndi kumaphedwa. Amanyoza mwachipongwe zinthu zosazidziŵa. Ndipo monga nyama zija, iwo omwe adzaonongedwa,

13nadzalangidwa molingana ndi kuipa kwao. Chimene chimaŵakomera nkumangochita zokondweretsa thupi nthaŵi yamasana. Ali ngati mathotho ndi maŵanga onyansa, chifukwa podya nanu pamodzi amakondwera kuchita zonyenga.

14Maso ao ndi adama, osafuna kuleka kuchimwa. Amanyengerera anthu a mtima wosakhazikika. Ali ndi mtima wozoloŵera kuumirira chuma. Anthu otembereredwa!

15Num. 22.4-35 Adasiya njira yolungama, adasokera potsata njira ya Balamu, mwana wa Beori, amene ankafunitsa kupata mphotho pochita zosalungama.

16Koma adadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama yosalankhula, adalankhula ngati munthu, kuletsa zamisala za mneneriyo.

17Aphunzitsi onyengaŵa ali ngati akasupe opanda madzi, ngati nkhungu yokankhidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu adaŵasungira mdima wakuda wabii.

18Iwowotu amalankhula mau odzitama auchitsiru, ndipo ndi zilakolako zonyansa zathupi amanyengerera anthu amene angopulumuka chatsopano pakati pa anzao oipa.

19Amaŵalonjeza ufulu, chonsecho eniakewo ndi akapolo a chivunde. Pajatu munthu amasanduka kapolo wa chimene chamugonjetsa.

20Chifukwatu ngati anthu apulumuka ku zodetsa za dziko lino lapansi, pakudziŵa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, pambuyo pake nkugwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zoipa zomwezo, potsiriza adzakhala oipa koposa m'mene analiri poyamba.

21Kukadakhala bwino kwa iwo akadakhala osadziŵa njira ya chilungamo, koposa kuileka atadziŵa lamulo loyera limene Mulungu adaŵapatsa.

22Miy. 26.11Pakutero akutsimikiza kuti ngwoona mwambi uja wakuti, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndi wina ujanso wakuti, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhuliranso m'matope.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help