Mphu. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za chimwemwe choona

1Ngwodala munthu amene sanachimweko polankhula,

ndipo sayenera kuvutika mu mtima chifukwa cha machimo.

2Ngwodala munthu amene mtima wake sumutsutsa,

munthu amene sadataye chikhulupiriro chake.

Za njiru ndi umbombo

3Chuma sichimkhala bwino munthu wakaliwumira.

Kodi munthu wanjiru chuma ali nacho ntchito yanji?

4Munthu wodziwunjikira chuma podzimana,

amangosungira anzake,

ndi ena amene adzasangalale nacho chuma chakecho.

5Kodi munthu wodziwumira mtima,

angathandize anzake bwanji?

Iye yemwe sadzakondwera nacho chuma chakecho.

6Palibe munthu wouma mtima kwambiri kupambana munthu

wodziwumira mtima mwiniwake yemwe.

Pamenepa ndiye pali chilango cha kuuma mtima kwake.

7Akachita zabwino,

ndiye kuti zachitika mwangozi,

potsiriza kuipa kwake kumadzaonekerabe poyera.

8Ngwoipitsitsa munthu wa diso lanjiru,

amafulatira anzake, osasamalako za moyo wao.

9Maso a munthu woumira sakhutira nazo zinthu zake.

Mtima wake umachita kukhwinyata nawo umbombo.

10Munthu wakaliwumira amachita umbombo ndi chakudya chomwe,

m'nyumba mwake njala siichoka.

Chuma chigwire ntchito zabwino

11Mwana wanga, ukometse moyo wako monga m'mene ungathere,

nthaŵi zonse uzipereka nsembe zoyenera kwa Ambuye.

12Kumbukira kuti imfa idzakufikira ndithu tsiku lina,

koma nthaŵi yeniyeni yopita ku manda sungaidziŵe.

13Usanafe, uzichitira anzako zabwino,

uziŵathandiza monga momwe ungathere.

14Usadzimane zisangalatso zalero,

ndipo zabwino zimene ukuzikhumbira moyenera zisakupite.

15Nanga sudzasiyira ena chuma chako

chimene udachivutikira?

Ndipo zako zonse zimene udakhetsera thukuta

adzaombezera kuti agaŵane bwino.

16Tsono khala munthu wopatsa,

kwinaku uzilandira anzako akakupatsa kanthu.

Dyeratu, kumanda kulibe zabwino.

17Amoyo onse amajujuka ngati nsalu,

paja pali lamulo lachikhalire lakuti,

“Munthu aliyense adzafa basi!”

18Monga amachitira masamba mu mtengo wogudira,

ena akuyoyoka, ena akuphukira,

ndi m'menenso imachitira mibadwo ya anthu:

wina ukufa, wina ukubadwa.

19Ntchito zonse za munthu zimaola,

mwini wake akapita, nazonso zii.

Za chimwemwe cha munthu wanzeru

20 Miy. 8.32-35 Ngwodala munthu amene amasinkhasinkha za luntha,

ndipo amagwiritsadi ntchito nzeru.

21Ngwodala munthu amene amalingalira

njira zake za luntha,

adzasinkhasinkhanso zinsinsi zake.

22Amalithamangira ngati mlenje wosaka nyama,

amalalira lunthalo m'njira yake.

23Amalisuzumira pa mawindo ake,

ndipo amamvetsera pakhomo pake.

24Ngwodala amene amakhala pafupi ndi nyumba ya luntha,

ndipo amakhoma hema lake pafupi ndi chipupa

cha nyumbayo.

25Amamanga hema lake pafupi pa lunthalo,

pamene mpokoma kukhalapo.

26Amaika ana ake mumthunzi mwake,

ndi kumanga msasa m'munsi mwa nthambi zake.

27Luntha limamteteza ku mafundi,

ndipo iye amakhazikika mu ulemerero wa lunthalo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help