1Naŵa mau amene Mose adauza Aisraele onse pamene anali m'chipululu, patsidya pa mtsinje wa Yordani, m'chigwa cha Araba, kuyang'anana ndi Sufu, pakati pa Parani tsidya lina ndi Tofele, Labani, Hazeroti ndi Dizahabu tsidya linanso.
2Ulendo wa pakati pa Horebu ndi Kadesi-Baranea, kudzera njira ya phiri la Seiri, unali wa masiku 11.
3Pa tsiku loyamba la mwezi wa 11, pa chaka cha 40 kuyambira pamene adatuluka m'dziko la Ejipito, Mose adauza anthu a ku Israele zonse zimene Chauta adamlamula kuti anene kwa anthuwo.
4Num. 21.21-35 Zimenezi zidachitika Moseyo atagonjetsa kale Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala ku Hesiboni, ndi mfumu Ogi wa ku Basani, amene ankakhala ku Asitaroti ndi ku Ederei.
5Mose adayamba kufotokozera anthu malamuloŵa ku tsidya la Yordani m'dziko la Mowabu, adati:
6Pamene tinali ku phiri la Horebu, Chauta, Mulungu wathu, adatiwuza kuti, “Inu mwakhalitsa kuphiri kuno.
7Nyamukani muyambepo kuyenda. Pitani ku dziko lamapiri la Aamori, ndi konse kumene kumakhala anzao a Aamoriwo ku chigwa cha Araba, ku dziko lamapiri ndi ku zigwa, ku Negebu ndi pamphepete pa Nyanja yaikulu, ku dziko la Akanani ndi ku Lebanoni, mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
8Ndi limenelitu dziko limene ndikulipereka kwa inu. Muloŵe ndi kukhazikika m'dzikoli limene Ine Chauta, Mulungu wanu, ndidalumbira kuti ndidzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, ndi zidzukulu zao zonse.”
Mose asankha aweruzi(Eks. 18.13-27)9Mose adatinso: Paja ndidakuuzani nthaŵi imeneyo kuti sindingathe kusenza ndekha udindo wokutsogolerani.
10Chauta, Mulungu wanu, wakuchulukitsani mpaka lero muli ngati nyenyezi zamumlengalenga.
11Chauta, Mulungu wa makolo anu, akulitse chiŵerengero chanu pochichulukitsa ndi chikwi chimodzi, ndipo akudalitseni monga momwe adalonjezera.
12Koma ine ndekha ndingathe bwanji kusenza udindo wokutsogolerani ndi womaweruzanso milandu pakati panu?
13Sankhani anthu ena anzeru, omvetsa ndi odziŵa zinthu bwino, pakati pa mafuko anu, ndipo ine ndidzaŵaika kuti akhale atsogoleri pakati panu.
14Ndipo inu mudaandiyankha kuti, “Zimene mwanenazi nzabwino, ife tidzachitadi.”
15Motero ndidasankha atsogoleri anu, anthu anzeru ndi odziŵa zinthu bwino, ndipo ndidaŵaika kuti aziyang'anira ena magulu a anthu zikwi zingapo, ena a anthu mazana angapo, ena a anthu makumi asanu, ndipo enanso a anthu khumi. Enanso ndidaŵasankha kuti akhale nduna pakati pa mafuko anuwo.
16Pa nthaŵi imene ija, ndidaŵalangiza aweruzi anuwo kuti, “Mumve milandu imene ili pakati pa anthu anu. Mlandu uliwonse muuweruze bwino, kaya ndi wa anthu a mtundu wanu, kapena wa alendo amene amakhala nao pakati panu.
17Musamakondere poweruza. Aliyense, munthu wamba kapena wamkulu, mumuweruze chimodzimodzi. Musamaopa wina aliyense, chifukwa chiweruzo chonse ndi cha Mulungu. Mlandu wina ukakulakani, mubwere nawo kwa ine, ndipo ndidzaugamula ndine.”
18Nthaŵi yomweyo, ndidakuuzani zonse zimene muyenera kuchita.
Za azondi otumidwa kuchokera ku Kadesi-Baranea(Num. 13.1-33)19Ife tidachita zimene Chauta, Mulungu wathu, adatilamula. Tidachoka ku phiri la Horebu ndipo tidabzola chipululu chachikulu ndi choopsa chija chimene mudachiwona pa njira yopita ku dziko lamapiri la Aamori. Titafika ku Kadesi-Baranea,
20ndidakuuzani kuti, “Tsopano, tafika ku dziko lamapiri la Aamori limene Mulungu wa makolo athu akutipatsa.
21Ndi limenelitu dziko lomwe Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani. Pitani, kakhaleni m'menemo monga momwe adakulamulirani. Musaope kapena kuchita mantha.”
22Koma paja inu mudabwera kwa ine nkumanena kuti, “Tiyeni titume anthu akaliwone dzikolo, kuti adzatiwuze njira yabwino yoti tidzadzere, ndipo adzatifotokozere za m'mene iliri mizinda yakumeneko.”
23Mau amenewo adandikomera, motero ndidasankha anthu khumi ndi aŵiri, mmodzi pa fuko lililonse.
24Iwoŵa adanyamuka napita ku dziko lamapirilo, mpaka adakafika ku chigwa cha Esikolo, ndipo adakalizonda dzikolo.
25Adabwerera atatengako zipatso, nafika nazo pakati pathu. Ndipo adatiwuza kuti, “Dziko limene Chauta, Mulungu wathu, akutipatsalo ndi lachonde.”
26 Deut. 9.23; Ahe. 3.16 Koma inu simudafune kupita, mudaukira ulamuliro wa Chauta, Mulungu wanu.
27Inu munkangodandaula m'mahema mwanu nkumati, “Chauta amadana nafe. Nchifukwa chake adatitulutsa ku dziko la Ejipito, natipereka kwa Aamori kuti atiphe.
28Kodi tikapeza dziko lanji kumeneko? Abale athu aja atidederetsa potiwuza kuti anthu akumeneko ngamphamvu ndi aatali kupambana ife. Akutinso mizindayo njaikulu, ya malinga ofika mpaka m'mwamba. Ndiponso akuti kumeneko adaona ziphona, zidzukulu za Aanaki.”
29Koma ine ndidakuuzani kuti, “Musaŵaope anthu amenewo.
30Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakutsogolerani, ndipo adzaponyanso nkhondo m'malo mwanu, monga momwe mudaonera ku Ejipito kuja
31Ntc. 13.18 ndi m'chipululu muja. Inu mudaona njira yonse m'mene adakufikitsirani kuno, kuti adakunyamulani monga momwe bambo amanyamulira mwana wake.”
32Ahe. 3.19 Koma ngakhale zidachitika zimenezo, inu simudakhulupirire Chauta, Mulungu wanu,
33amene nthaŵi zonse ankatsogola pa ulendo wanu, kuti akupezerenitu malo omangapo mahema anu. Iye ankayenda patsogolo panu m'maonekedwe a moto usiku, kuti akuunikireni njira, koma masana ankakhala ndi maonekedwe a mtambo.
Mulungu alanga Aisraele(Num. 14.20-45)34 Ahe. 3.18 Chauta atamva kudandaula kwanuko, adakwiya ndipo adalumbira kuti,
35“Mu mbadwo woipitsitsawu palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dziko lachondelo limene ndidalumbira kuti ndidzapatsa makolo anu.
36Koma Kalebe yekha, mwana wa Yefune, ndiye amene adzaloŵe. Iyeyo adakhala ndithu wokhulupirika kwa Ine, choncho dziko adalipenyalo ndidzalipatsadi kwa iye ndi kwa zidzukulu zake.”
37Chauta adandikwiyira inenso chifukwa cha inu.
38Adati, “Iwe Mose sudzaloŵa m'dzikomo, koma mthandizi wako Yoswa, mwana wa Nuni, ndiye adzaloŵe. Umlimbitse mtima Yoswayo, poti iyeyo ndiye adzatsogolere Aisraele pokaloŵa m'dzikomo.”
39Tsono Chauta adatiwuza tonsefe kuti, “Makanda anu amene mudati adzagwidwa ndi adani, ndiponso ana anu amene akadali aang'ono, amene sadziŵa chabwino kapena choipa pa lero lino, ndiwo adzaloŵe m'dzikolo. Ndidzalipatsa kwa iwowo ndipo adzakhalamo.
40Koma inu bwererani, muzipita ku chipululu, kulunjika ku Nyanja Yofiira.”
41Inu mudayankha kuti, “Ife tachimwira Chauta. Koma tsopano tidzamenya nkhondo monga momwe Chauta wathu adatilamulira.” Pamenepo aliyense mwa inu adatenga zida zake zankhondo, namaganiza kuti nkwapafupi kugonjetsa dziko lamapirilo.
42Koma Chauta adandiwuza kuti, “Uŵachenjeze kuti asaŵapute Aamoriwo, chifukwa Ine sindidzakhala nawo, ndipo adani aowo adzaŵagonjetsa.”
43Ndidakuuzani zimene Chauta adanena, koma inu simudasamale. Mudaukira Chauta, ndipo mudakaloŵa m'dziko lamapirilo, muli tumbatumba kunyada.
44Pamenepo Aamori okhala m'mapiriwo adakutulukirani nakuthamangitsani ngati njuchi, ndipo adakukanthani kuchokera ku Seiri mpaka ku Horoma.
45Tsono inu pobwera mudalira kuti Chauta akuthandizeni, koma Chauta sadakumvereni kapena kukutcherani khutu.
46Nchifukwa chake mudakhalako masiku ambiri ku Kadesi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.