1Tsono Yoswa adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele ku Sekemu. Adaitana akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a Aisraele, ndipo onsewo adafika pamaso pa Mulungu.
2Gen. 11.27 Adauza anthu onsewo kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena ndi izi, akuti, ‘Kale makolo anu ankakhala pa mbali ina ya mtsinje wa Yufurate, ndi kumapembedza milungu ina. Mmodzi mwa makolo ameneŵa anali Tera, bambo wa Abrahamu ndi Nahori.
3Gen. 12.1-9; Gen. 21.1-3 Tsono Abrahamuyo ndidamtenga ndi kumchotsa m'dzikomo patsidya pa Yufurate, ndipo ndidamtsogoza kupita naye ku dziko la Kanani. Ndidampatsa zidzukulu zambiri. Ndidampatsa Isaki,
4Gen. 25.24-26; Gen. 36.8; Deut. 2.5; Gen. 46.1-7 ndipo Isakiyo ndidampatsa Yakobe ndi Esau. Dziko lamapiri la Seiri ndidapatsa Esau kuti likhale choloŵa chake, koma Yakobe ndi ana ake adatsikira ku Ejipito.
5Eks. 3.1—12.42 Pamenepo ndidatuma Mose ndi Aroni ku Ejipitoko, ndipo ndidazunza kwambiri Aejipitowo. Pambuyo pake ndidakutulutsani inu.
6Eks. 14.1-31 Nditatulutsa makolo anu ku dziko la Ejipito, ndidafika nawo ku Nyanja Yofiira, koma Aejipito okwera pa magaleta ndi pa akavalo adaŵatsatira mpaka kunyanjako.
7Makolo anuwo atapemphera mokhulupirira kwa Ine, ndidaika mtambo wakuda pakati pa iwo ndi Aejipitowo, ndipo nyanja idaŵamiza Aejipito onsewo. Mudapenya ndi maso anu zomwe ndidachita Ejipito, ndipo mudakhala nthaŵi yaitali m'chipululu.
8 Num. 21.21-35 “ ‘Pambuyo pake Ine ndidakufikitsani ku dziko la Aamori, amene ankakhala kuvuma kwa mtsinje wa Yordani. Adalimbana nanu iwowo, koma Ine ndidaŵapereka m'manja mwanu, mwakuti mudalanda dziko lao, chifukwa Ine ndidaŵaononga inu mukufika.
9Num. 22.1—24.25 Tsono Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Amowabu, adalimbana ndi Israele. Iyeyu adatumiza mau kwa Balamu mwana wa Beori, nampempha kuti akutemberereni.
10Koma Ine sindidamvere Balamuyo, motero iyeyo adakudalitsani, ndipo ndidakupulumutsani m'manja mwa Balaki.
11Yos. 3.14-17; Yos. 6.1-21 Mudaoloka Yordani ndi kufika ku Yeriko. Anthu a ku Yeriko adalimbana nanu, kudzanso Aamori, Aperizi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi. Ine ndidaŵapereka m'manja mwanu.
12Eks. 23.28; Deut. 7.20 Ndine amene ndidatumiza zoluma zija kuti zizunze mafumu a Aamori aja, ndipo onsewo adapirikitsidwa pamaso panu. Si malupanga kapena mauta anu amene adachititsa zimenezi ai.
13Deut. 6.10, 11 Ndidakupatsani dziko limene inuyo simudaligwirire ntchito, pamodzi ndi mizinda imene simudaimange. Mukukhala kumeneko ndi kumangodya mphesa ndi olivi, zimene inu simudabzale.’
14“Tsono inu, opani Chauta ndipo mumtumikire moona ndi mokhulupirika. Chotsani milungu imene makolo anu ankaipembedza pambali pa mtsinje wa Yufurate ndi ku Ejipito, ndipo mutumikire Chauta.
15Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”
16Apo anthuwo adayankha kuti, “Zoti nkusiya Chauta ndi kumakatumikira milungu ina ndiye ai, ife sitingathe kuchita zotere mpang'ono pomwe.
17Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adatulutsa makolo athu pamodzi ndi ife tomwe mu ukapolo, ku dziko la Ejipito. Ndipo tidaonanso ndi maso athu zinthu zazikulu zimene adachita.
18Ife tikufika, Chauta ankapirikitsa Aamori amene ankakhala m'dziko lino. Motero nafenso tidzatumikira Chauta, chifukwa ndiye Mulungu wathu.”
19Pamenepo Yoswa adauza anthuwo kuti, “Mwina mwaketu inu simungathe kutumikira Chauta chifukwa ndi Mulungu woyera, wosalola kupikisana naye. Ndipo sadzakulekererani mukumpandukira ndi kumamchimwira.
20Mukasiya Chauta, Mulungu wanu, ndi kumakatumikiranso milungu yachilendo, adzakufulatirani, ndipo adzakulangani. Adzakuwonongani ngakhale kuti kale adakuchitirani zabwino.”
21Ndipo anthuwo adauza Yoswa, kuti, “Iyai! Ife tidzatumikira Chauta.”
22Tsono Yoswa adaŵauza kuti, “Inu mukudzichitira nokha umboni kuti mwasankhula kutumikira Chauta.” Anthuwo adavomera kuti, “Inde, mboni ndife tomwe.”
23Yoswa adatinso, “Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu, ndipo muzipembedza Chauta, Mulungu wa Israele, mokhulupirika.”
24Anthuwo adauza Yoswa kuti, “Tidzatumikira Chauta, Mulungu wathu, ndipo tidzamvera malamulo ake.”
25Motero Yoswa adapangana nawo anthu pa tsiku limenelo, ndipo ku Sekemu komweko Yoswa adapatsa anthuwo malamulo ndi malangizo.
26Yoswayo adalemba malamulo ameneŵa m'buku la malamulo a Mulungu, ndipo adatenga chimwala chachikulu nachiimiritsa patsinde pa mtengo wa thundu pa malo opatulika a Chauta.
27Ndipo adauza anthuwo kuti, “Mwala umenewu udzakhala mboni yotitsutsa. Mau amene Chauta walankhula ndi ifeŵa, mwalawu wamva. Motero udzakhala mboni yokutsutsani, ngati mudzakane Mulungu wanu.”
28Tsono Yoswa adaŵalola anthuwo kuti aliyense abwerere ku dziko lake.
Kumwalira kwa Yoswa ndi Eleazara.29Zitatha zimenezi, Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Chauta, adamwalira. Anali ndi zaka 110 zakubadwa.
30Yos. 19.49, 50 Adamuika m'dziko lake ku Timnati-Sera, m'dziko lamapiri la Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gasi.
31Aisraele adatumikira Chauta pa nthaŵi yonse ya moyo wa Yoswa ndiponso pa nthaŵi ya atsogoleri amene adakhala ndi moyo Yoswa atafa. Atsogoleriwo adadziŵa ntchito zonse zimene Chauta adachitira Israele.
32 Gen. 33.19; 50.24, 25; Eks. 13.19; Yoh. 4.5; Ntc. 7.16 Mafupa a Yosefe amene Aisraele adaŵatenga ku Ejipito, adakaŵaika ku Sekemu m'kadziko kamene Yakobe adaagula kwa ana a Hamori, bambo wa Sekemu, pa mtengo wa ndalama zasiliva zana limodzi. Ndipo dzikolo lidasanduka choloŵa cha zidzukulu za Yosefe.
33Eleazara, mwana wa Aroni, nayenso adamwalira, ndipo adamuika ku Gibea m'mudzi wa mwana wake Finehasi, umene adaamupatsa m'dziko lamapiri la Efuremu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.