1Tsono Tobiyasi adayankha Tobiti bambo wake kuti “Zonse zimene mwandilamula ndidzachita, bambo.
2Koma kodi ndikatenga bwanji ndalamazo kwa munthuyo? Iye sandidziŵa, inenso sindimudziŵa. Kodi ndikampatsa chizindikiro chanji kuti akandidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo kuti andibwezere ndalamazo? Chinanso, njira zopita ku Mediya sindizidziŵa.”
3Tobiti adayankha Tobiyasi mwana wake kuti, “Iyeyo adandipatsa kalata ya chipangano chathu, ndipo inenso ndidampatsa kalata imene ndidaika pamodzi ndi ndalamazo. Tsopano papita zaka makumi aŵiri nditamsungiza ndalamazo. Tsono mwana wanga, ufune munthu wokhulupirika woti atsagane nawe mpaka udzabwerere, ndipo tidzamulipira. Ndiye iwe, ukalandire ndithu ndalamazo m'manja mwake mwa Gabaele.”
Mngelo Rafaele atsogolera Tobiyasi4 Ahe. 13.2 Tobiyasi adatuluka kukafuna munthu amene ankadziŵa njira ya ku Mediya, kuti apite naye. Atatuluka, adapeza mngelo Rafaele, koma sadadziŵe kuti ndi mngelo wa Mulungu.
5Adamufunsa kuti, “Kodi iwe bwenzi langa, kwanu nkuti?” Mngelo adayankha kuti, “Ndine mmodzi mwa abale ako Aisraele, ndabwera kuno kudzafuna ntchito.”
6Tobiyasi adamufunsa kuti, “Kodi njira ya ku Mediya umaidziŵa?” Iye adayankha kuti, “Ndimaidziŵa bwino. Ndidapitako kambirimbiri, njira zonse ndikuzidziŵa bwino. Ndinkapita ku Mediya kaŵirikaŵiri, ndipo kumeneko ndinkakhala kwa Gabaele, mbale wathu wa ku Ragesi, ku Mediyako. Ndi ulendo wa masiku aŵiri kuchokera ku Ekibatana kukafika ku Ragesi, chifukwa mzinda wa Ragesiwo uli pakati pa mapiri.”
7Apo Tobiyasi adati, “Tabaima pano, bwenzi langa. Ndipita kukadziŵitsa bambo wanga, chifukwa ndifuna kuti undiperekeze, ndipo ndidzakulipira.”
8Iye adati, “Chabwino, ndidikira pompano, komatu usachedwe.”
Tobiti akumana ndi Rafaele9Tobiyasi adaloŵa, nadziŵitsa bambo wake kuti, “Ndapeza wina mwa abale athu Aisraele amene wavomera kundiperekeza.” Bambo wake adati, “Tamuitana munthuyo kuti ndidziŵe mtundu wake ndi fuko lake, ndiwone ngati ngwokhulupirika kuti nkukuperekeza iwe mwana wanga.”
10Tobiyasi adatuluka nati, “Iwe, bambo wanga akukuitana.” Tsono adaloŵa naye, Tobiti nkumulonjera mngeloyo. Poyankha, iyeyo adati, “Mukhale ndi chimwemwe chachikulu.” Apo Tobiti adati, “Ha! Ndingakhalenso ndi chimwemwe bwanji? Ine ndine munthu wakhungu, sindiwona chilichonse. Ndimangokhala mu mdima ngati akufa, amene sapenya kuŵala. Ndili moyo pakati pa anthu akufa, ndimamva mau a anthu, koma anthuwo sindiŵaona.” Rafaele adayankha kuti, “Musavutike! Mulungu adzakuchiritsani posachedwa. Musadandaule!” Tsono Tobiti adati, “Tobiyasi mwana wanga akufuna kupita ku Mediya. Kodi ungathe kupita naye ndi kumlondolera njira? Ndidzakulipira, mbale wanga.” Mngeloyo adati, “Inde, ndingathe kupita naye. Ndikudziŵa miseu yonse, ku Mediya ndakhala ndikupitako kaŵirikaŵiri. Ndidayendamo m'zigwa zake zonse ndi m'mapiri ake onse, ndikudziŵa njira zake zonse.”
11Tobiti adafunsanso kuti, “Mbale wanga, kodi ndiwe wa banja la yani, ndipo ukuchokera fuko liti? Tandiwuza mbale wanga.”
12Iye adati, “Chifukwa chiyani mukufuna kudziŵa fuko langa?” Tobiti adayankha kuti, “Ndikufuna kudziŵa bwino kuti ndiwe mwana wa yani, ndiponso kuti dzina lako ndani.”
13Iye adati, “Ndine Azariyasi, mwana wa Ananiya wamkulu uja, mmodzi mwa achibale anu.”
14Tobiti adati, “Ai, takulandira kwathu kuno, mbale wanga. Usandipsere mtima chifukwa chakuti ndafuna kudziŵa zoona za banja lako. Koma ndikuwona kuti ndiwedi mbale wanga wa fuko labwino ndi laulemu. Ndimadziŵa Ananiya ndi Natani, ana aŵiri a Semeliyasi wamkulu. Iwo ankapita nane ku Yerusalemu ndi kupembedza nane pamodzi, ndipo sadaleke kuyenda m'njira yoona. Abale ako ndi anthu abwino, motero ndiwe wa mtundu waulemu. Takulandira kwathu kuno.”
15Ndipo adaonjeza kuti, “Ndidzakupatsa malipiro oyenerera tsiku lililonse, pamodzi ndi ndalama zina zofunikira pa ulendo wanuwo, molingana ndi zimene ndipatse mwana wanga.
16Gen. 24.7, 40Mperekeze bwino mwana wangayu, ndipo ndidzaonjezapo mphotho pa malipiro ako.”
17Mngeloyo adayankha kuti, “Ndipita naye, musaope. Zonse zidzatiyendera bwino popita kumeneko, ndipo tidzabweranso kuno tili bwino, chifukwa njira yake njosaopsa.” Apo Tobiti adati, “Madalitso a Mulungu akhale pa iwe, mbale wanga.” Tsono adaitana mwana wake, namuuza kuti, “Mwana wanga, konza zofunikira ulendo, upite ndi mbale wakoyu. Mulungu Wakumwamba akusungeni kumeneko ndi kukubwezerani kuno muli ndi moyo. Mngelo wake ayende nanu kukutchinjirizani.” Ponyamuka Tobiyasi adampsompsona atate ndi amai ake. Ndipo Tobiti adati, “Pita bwino, mwana wanga.”
18Amai ake a Tobiyasi adayamba kulira misozi nauza Tobiti kuti, “Akupitiranji mwana wanga? Ameneyu sindiye ndodo ya m'manja mwathu paja? Suja amatichirikiza ndi iyeyu?
19Ndithudi, si ndalama zokha zoti nkuikirapo mtima. Ndalama si chinthu chamtengowapatali ngati mwana wathu.
20Moyo umene Mulungu adatipatsa, utikwanira.”
21Tobiti adati, “Zichepe, zichepe! Mwana wathu apita ali ndi moyo ndipo adzabwereranso kuno ali ndi moyo. Tsiku limene adzabwerere, udzaona wekha kuti moyo wake ukali bwino ngati kale.
22Tsono iwe phee, usadandaule za ameneŵa, iwe mlongo wanga! Mngelo wabwino adzankha nawo, ulendo wake udzakhala wabwino, ndipo adzabwerera ali bwino.” Apo mai uja adaleka kudandaula.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.