1Chaka chachiŵiri cha ufumu wake, Nebukadinezara adalota maloto. Ndipo adavutika kwambiri mumtima mwake, osathanso kupeza tulo.
2Tsono adalamula kuti aitane amatsenga, oombeza, amaula ndi alauli, kuti amuululire zimene iye adaalota. Iwo adaloŵa naima pamaso pa mfumu.
3Mfumu idaŵauza kuti, “Ndalota maloto, ndipo mtima wanga ukuvutika kwambiri kuti ndidziŵe za maloto angawo.”
4Tsono alauli adalankhula m'Chiaramu kuti, “Mukhale ndi moyo wautali amfumu. Tiwuzeni zimene mwalota, tikufotokozerani tanthauzo lake.”
5Mfumu idaŵayankha kuti, “Zimene nditi ndichite ndi izi: Mukapanda kundiwuza inu nomwe malotowo ndi tanthauzo lake, ndikukadzulanikadzulani, ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa mabwinja.
6Koma mukandiwuza malotowo ndi tanthauzo lake, ndikupatsani mphatso zambiri, ndipo ndidzakulemekezani kwambiri. Tsono uzeni malotowo, ndi kumasula kwake.”
7Iwowo adayankhanso kachiŵiri kuti, “Amfumu atiwuze ife akapolo ao malotowo, tifotokoza tanthauzo lake.”
8Mfumu idati, “Nchodziŵikiratu kwa ine kuti mukungozengereza, chifukwa mwadziŵa kale kuti sindisintha maganizo.
9Ndiye mukapanda kundidziŵitsa malotowo, inutu chilango chake nchimodzi chokha. Mwavomerezana kuti mundiwuze zabodza, chifukwa mumaganiza kuti mwina patapita nthaŵi zinthu zisintha. Tsono ingondiwuzani malotowo, apo ndidzadziŵa kuti mungathedi kundimasulira.”
10Alauli adayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene angathe kuuza amfumu zimene akufuna. Palibe mfumu iliyonse yamphamvu ndi yomveka imene idaafunsapo zotere kwa amatsenga, oombeza, kapena alauli ake.
11Zimene inu amfumu mukutifunsa nzapatali. Palibe wina angathe kukuyankhani kupatula milungu yokha, imene imakhala kutali ndi anthu.”
12Itamva zimenezi mfumu idapsa mtima ndi kukwiya kwambiri, ndipo idalamula kuti anzeru onse a ku Babiloni aphedwe.
13Tsono adalengeza lamulo limeneli lakuti anzeru onse a ku Babiloni aphedwe. Ndipo adayamba kufunafuna Daniele ndi anzake kuti nawonso aphedwe.
Mulungu adziŵitsa Daniele tanthauzo lake la malotowo14Tsono Daniele adalankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mtsogoleri wa gulu la asilikali a mfumu, amene adatumidwa kukapha anzeru a ku Babiloni.
15Daniele adafunsa Ariyoki kuti, “Chifukwa chiyani lamulo la mfumu lili loŵaŵa chotere?” Ariyoki adafotokoza zonse kwa Daniele.
16Tsono Daniele adapita kwa mfumu, nakapempha nthaŵi yoti amasule malotowo.
17Pambuyo pake Daniele adapita kwao, ndipo adakakambira nkhaniyo anzake aja, Hananiya, Misaele ndi Azariya.
18Adaŵauza kuti apemphere kwa Mulungu Wakumwamba kuti aŵachitire chifundo, alole kuti afotokoze chinsinsicho, kuti asaphedwe pamodzi ndi anzeru ena aja a ku Babiloni.
19Choncho chinsinsicho chidaululidwa kwa Daniele m'masomphenya usiku. Pamenepo Daniele adayamba kutamanda Mulungu Wakumwamba.
20Adati,
“Dzina la Mulungu litamandike mpaka muyaya,
nzeru ndi mphamvu zonse nzake.
21Amalamulira nyengo ndi nthaŵi.
Amakweza mafumu, naŵatsitsanso.
Amapatsa nzeru kwa anthu anzeru,
amapatsa luntha kwa omvetsa zinthu.
22Amaulula zinsinsi zozama ndi zobisika.
Amadziŵa zimene zili mu mdima,
ndipo kuŵala kumakhala ndi Iye.
23Ndikukuthokozani ndi kukutamandani
Inu Mulungu wa makolo anga,
pakuti Inu mwandipatsa nzeru ndi mphamvu.
Mwandiwululira tsopano zimene ife tidakupemphani,
ndipo mwatidziŵitsa zinsinsi za mfumu.”
Daniele auza mfumu malotowo ndi kumasula kwake24Motero Daniele adapita kwa Ariyoki amene mfumu idamulamula kuti aphe anzeru onse a ku Babiloni. Adamuuza kuti, “Musaŵaphe anzeru aja, koma perekezeni kwa mfumu, ndipo ndikaimasulira maloto ake.”
25Ariyoki adapita nayedi msanga Daniele kwa mfumu ndipo adati, “Amfumu, pakati pa akapolo a ku Yuda, ndapeza wina amene akuti akumasulireni maloto anu.”
26Apo mfumu idafunsa Daniele, amene ankatchedwa Belitesazara, kuti, “Kodi ungathedi kundiwuza maloto anga ndi kumasula kwake?”
27Daniele adayankha mfumuyo kuti, “Palibe wanzeru, woombeza, wamatsenga kapena mlauli aliyense amene angathe kukuululirani chinsinsi chimene inu amfumu mukufuna kudziŵa.
28Koma kuli Mulungu Kumwamba amene amaulula zinsinsi. Iyeyo wadziŵitsa mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika masiku akutsogolo. Tsono zinthu zimene mudaziwona muli m'tulo ndi izi:
29Amfumu, maganizo amene adakudzerani muli m'tulo anali a zinthu zimene zidzachitika kutsogolo. Mulungu woulula zinsinsi, wakudziŵitsani zimene zidzachitike.
30Chinsinsi chimenechi chaululidwa kwa ine, osati chifukwa chakuti ndine wanzeru kupambana anthu ena onse, koma kuti inu mfumu mudziŵe kumasula kwake, ndipo kuti mudziŵe maganizo amene aloŵa mumtima mwanu.
31“M'kulota kwanu, inu amfumu, mudapenya choumba chachikulu. Choumba chimenechi, chimene chinali chachikulu ndi chonyezimira kwambiri, chidaima pamaso panu, ndipo chinali chochititsa mantha zedi.
32Mutu wake unali wa golide wosalala, chifuwa ndi mikono zinali zasiliva, mimba ndi ntchafu zinali zamkuŵa.
33Miyendo yake inali yachitsulo. Mapazi anali a chitsulo chosakaniza ndi mtapo.
34Inu mukupenya, mwala udangodzitsakamukira ku phiri, munthu osaukankha konse. Udadzamenya mapazi a chitsulo ndi mtapo aja, nkuŵatswanya.
35Tsono chitsulo, mtapo, mkuŵa, siliva ndi golide uja, zonse zidaphwanyikira pamodzi. Ndipo zidauluzika ndi mphepo ngati mungu pa malo opunthira nthaŵi yachilimwe, osatsalapo nkanthu komwe. Koma mwala umene udaphwanya chithunziwo udasanduka phiri lalikulu, nkudzaza dziko lonse lapansi.
36“Inu amfumu, maloto aja ndi amenewo. Tsopano, tikumasulirani malotowo.
37Inu amfumu, mfumu ya mafumu, Mulungu Wakumwamba adakupatsani ufumu, mphamvu zonse, ulamuliro, ndi ulemerero.
38Adaika m'manja mwanu anthu ndi nyama zomwe ndiponso mbalame zamumlengalenga, ndipo akufuna kuti muzilamulira zonsezo kulikonse kumene zimakhala. Mutu wagolide uja ndi inuyo.
39Pambuyo pa ufumu wanu padzabwera ufumu wina wosakhala wamphamvu ngati wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, ufumu wake wamkuŵa, umene udzalamulira dziko lonse lapansi.
40Ndipo padzakhala ufumu wachinai, wolimba ngati chitsulo. Monga momwe chitsulo chimaphwanyira ndi kuwononga zinthu zonse, ufumuwo udzaphwanya ndi kuwononga maufumu ena onse aja.
41Monga m'mene mudaonera kuti mapazi ndi zala zake zinali za mtapo wosakaniza ndi chitsulo, ndiye kuti ufumuwo udzakhala wogaŵikana. Komabe udzakhala ndi mphamvu pang'ono, chifukwa cha chitsulo chija.
42Monga zala zakumwendo zinali mtapo wosakaniza ndi chitsulo, ndiye kuti ufumuwo mbali ina udzakhala wolimba, mbali ina udzakhala wofooka.
43Monga m'mene mudaonera kuti chitsulo chidasakanizika ndi mtapo, chonchonso anthu adzasakanizana ndipo sadzagwirizana kwenikweni, monga momwe chitsulo sichingathe kusakanizikira bwino ndi mtapo.
44Pa nthaŵi ya mafumu amenewo, Mulungu Wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzaonongeka. Udzaphwanya ndi kuŵatheratu maufumu ena onsewo, ndipo ufumu wokhawo udzakhala mpaka muyaya.
45Limeneli ndilo tanthauzo lake la mwala uja, umene mudauwona utangodzitsakamukira kuchokera ku phiri, munthu osaukankha konse, ndipo udaphwanya chitsulo, mkuŵa, mtapo, siliva ndi golide. Mulungu wamphamvu wakudziŵitsani zakutsogolo, amfumu. Ndakuuzani maloto anu mwatsatanetsatane, ndipo ndakufotokozerani tanthauzo lake lenileni.”
Mfumu ilemekeza Daniele46Pomwepo mfumu Nebukadinezara adadzigwetsa chafufumimba, ndipo adalambira Daniele. Adalamula kuti anthu atsire nsembe ndi kufukiza lubani kwa Daniele.
47Mfumuyo idati, “Zoonadi, Mulungu wako ndiyedi Mulungu wa milungu yonse, ndiponso ndiye Ambuye olamulira mafumu onse. Ndiye woulula zinsinsi, pakuti iweyo wathadi kundiwululira chinsinsi chimenechi.”
48Pambuyo pake mfumuyo idamkweza Daniele, ndipo idamchitira ulemu ndi kumpatsa mphatso zabwino zambiri. Adamuika kuti akhale wolamulira dera lonse la Babiloni, ndiponso kuti akhale mkulu woyang'anira anzeru ake onse.
49Chifukwa cha pempho la Daniele, mfumu idaika Sadrake, Mesaki ndi Abedenego kuti akhale oyang'anira ntchito za dera la Babiloni. Koma Daniele mwiniwake ankakhala m'bwalo la mfumu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.