1Ine mkulune ndikulemba kalatayi kwa mai wosankhidwa ndi Mulungu, ndi kwa ana ake amene ndimaƔakonda kwenikweni. Ndipo sindine ndekha amene ndimakukondani, komanso onse odziƔa choona.
2Timakukondani chifukwa cha choona chimene chimakhala mwa ife, ndipo chidzakhala nafe mpaka muyaya.
3Mulungu Atate ndi Yesu Khristu, Mwana wa Atate, atikomere mtima ndi kutipatsa chifundo ndi mtendere m'choona ndi m'chikondi.
Za choona ndi chikondi4Ndidakondwera kwambiri kuti ndidapeza ana anu ena akuyenda motsata choona, monga Atate adatilamulira.
5Yoh. 13.34; 15.12, 17Ndiye tsopano ndikukupemphani mai: tizikondana. Pakutero sindikukulemberani lamulo latsopano ai, koma lomwe lija limene takhala nalo kuyambira pa chiyambi.
6Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi.
7Paja pakuwoneka anthu ambiri onyenga pa dziko lapansi. Iwo savomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu. Munthu wosavomereza zimenezi ndi wonyenga, ndiponso woukira Khristu.
8Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma yesetsani kuti mukalandire mphotho yathunthu.
9Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, koma amaonjezerapo zina, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsocho, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana.
10Wina aliyense akadza kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamlandire m'nyumba mwanu. Musampatse ndi moni womwe,
11pakuti wopatsa munthu wotere moni, akuvomereza zochita zake zoipa.
Mau otsiriza12Ndili ndi zambiri zoti ndikuuzeni, koma sindifuna kuzilemba m'kalata. Ndikuyembekeza kubwera kwanuko kuti tidzakambirane pakamwa mpakamwa. Pamenepo chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.
13Ana a mbale wanu wosankhidwa ndi Mulungu akuti moni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.