1Chauta ndiye mbusa wanga,
sindidzasoƔa kanthu.
2 Chiv. 7.17 Amandigoneka pa busa lamsipu.
Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.
3Amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera m'njira za chilungamo
malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
4Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii,
sindidzaopa choipa chilichonse,
pakuti Inu Ambuye mumakhala nane.
Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
5Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona.
Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta,
mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.
6Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu
zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga.
Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.