1Ndidati, “Ndidzasamala zochita zanga,
kuti ndisachimwe polankhula.
Ndidzatseka pakamwa panga nthaŵi zonse
pamene anthu oipa ali nane.”
2Motero ndidakhala chete osalankhula kanthu,
ndidakhala duu, koma popanda phindu,
chifukwa mavuto anga ankangokulirakulira.
3Mtima wanga udavutika,
ndipo pamene ndidasinkhasinkha,
mtima wanga udangoyaka moto.
Pompo ndidalankhula ndi mau akuti,
4“Inu Chauta, mundidziŵitse mathero a moyo wanga,
mundidziŵitse kuchepa kwa masiku anga.
Mundilangize kuti moyo wanga sukhalira kutha.
5“Onani, mwandipatsa masiku ochepa chabe,
nthaŵi ya moyo wanga siili kanthu pamaso panu.
Ndithudi, munthu aliyense ndi mpweya chabe.
6Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi,
amangovutika ndi zachabechabe.
Munthu amakundika chuma,
koma amene adzachidye ndi wosadziŵika.
7“Nanga tsopano, Inu Ambuye, ndikudikira chiyani?
Chikhulupiriro changa chili pa Inu.
8Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse.
Musandisandutse chinthu chochinyodola zitsiru.
9Ndine mbeŵeŵe, sinditsekula pakamwa panga,
pakuti ndinu amene mwachita zimenezi.
10“Chotsani chikoti chanu pa ine,
ndatheratu chifukwa cha mkwapulo wanu.
11Inu mumalanga munthu
pakumdzudzula chifukwa cha uchimo wake.
Mumaonongeratu zimene iye amazikonda,
monga m'mene chimachitira chifukufuku.
Zoonadi, munthu aliyense ndi mpweya chabe.
12“Mverani pemphero langa, Inu Chauta,
mumve kulira kwanga.
Musakhale chete pamene ndikulirira Inu.
Ndine mlendo wanu wosakhalitsa,
munthu wongokhala nawo
monga adaachitira makolo anga onse.
13Musandiyang'ane mwaukali,
choncho ndidzatha kusangalala,
ndisanafe ndi kuzimirira.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.