Yob. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Satana ayesa Yobe

1Kudaali munthu wina, dzina lake Yobe, amene ankakhala m'dziko la Uzi. Munthu ameneyo anali wosalakwa ndiponso wolungama. Ankaopa Mulungu namapewa zoipa.

2Anali ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri, ndi ana aakazi atatu.

3Anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ng'ombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500. Anali ndi antchito ambiri, choncho anali munthu wotchuka koposa anthu onse a m'maiko akuvuma.

4Ana ake aamuna ankachita phwando mosinthana, tsiku lina kwa wina, tsiku lina kwa wina. Ndipo ankaitana alongo ao atatu aja ku maphwando aowo.

5Tsono masiku a phwandowo akatha, Yobe ankadzuka m'mamaŵa napereka nsembe, kuperekera mwana aliyense, kuti anawo ayeretsedwe potsata malamulo a chipembedzo. Yobeyo ankati, “Mwina mwake, wina mwa ana angaŵa adachimwa, adatukwana Mulungu mumtima mwake.” Umu ndimo m'mene ankachitira Yobe nthaŵi zonse.

6 Gen. 6.2 Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi.

7Pamenepo Chauta adafunsa Satanayo kuti, “Nanganso iwe Satana, kutereku ukuchokera kuti?”

Iye adayankha kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira dzikoli.”

8Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wazindikirapo mtumiki wanga Yobe, kuti safanafana ndi wina aliyense pa dziko lapansi? Iye uja ndi munthu wosalakwa ndi wolungama. Amandimvera Ine Mulungu, ndipo amapewa zoipa.”

9Chiv. 12.10 Satana adafunsa Chauta kuti, “Kani mwayesa Yobe uja amangokumverani pachabe?

10Suja Inu mwakhala mukumteteza ponseponse iye uja, pamodzi ndi banja lake ndi zinthu zake zonse zimene ali nazo. Mudamdalitsanso pa ntchito zimene amachita, ndipo chuma chake nchochuluka kwambiri m'dzikomo.

11Koma tsopano tangoyesani kumchotsera zonse zimene ali nazo, muwona, adzakutukwanirani pamaso.”

12Chauta adauza Satana kuti, “Chabwino, zonse zimene Yobe ali nazo ndaziika m'manja mwako. Koma iye yekhayo usamkhudze.” Pamenepo Satanayo adachoka, kumsiya Chauta.

Ana a Yobe aphedwa, chumanso chiwonongeka

13Tsiku lina ana aamuna ndi ana aakazi a Yobe ankachita phwando m'nyumba mwa mkulu wao.

14Ndiye kudafika wamthenga kwa Yobe kudzamuuza kuti, “Ng'ombe zinalikulima, ndipo abulu analikudya pafupi pomwepo.

15Mwadzidzidzi nkubwera Aseba kudzatithira nkhondo nalanda ng'ombezo ndi abulu omwe. Ndipo apha antchito onse, koma ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”

16Iyeyo akulankhulabe, padafikanso wina, nati, “Kunagwa mphezi ndipo yapsereza nkhosa zonse pamodzi ndi abusa omwe, onse psiti. Ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”

17Ameneyu asanatsirize kulankhula, padafikanso wina, nati, “Kunafika magulu atatu a Akaldeya kudzatithira nkhondo. Atilanda ngamira zonse, ndipo apha antchito onse. Ndapulumukapo ndine ndekha kuti ndidzakuuzeni.”

18Iyeyo mau akali m'kamwa, padafikanso wina, nati, “Ana anu onse anali pa phwando m'nyumba ya mkulu wao.

19Mwadzidzidzi chayamba chimphepo champhamvu chochokera ku chipululu, nkudzaomba nyumbayo mbali zonse. Motero yagwa ndi kuŵapsinja anawo. Onse aphedwa, ndapulumukapo ndine ndekha kuti ndidzakuuzeni.”

20Yobe atamva zimenezo, adadzambatuka, nkung'amba zovala zake. Adameta tsitsi, ndipo adadzigwetsa pansi napembedza Mulungu.

21Mphu. 40.1; 11.14Adati,

“M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche,

namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche,

Chauta ndiye adapatsa,

Chauta ndiyenso walanda.

Litamandike dzina la Chauta.”

22Ngakhale zidaayenda motero, Yobe sadachimwe kapena kunena kuti, “Mulungu walakwa.”

Satana ayesanso Yobe
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help