1 pamodzi ndi amai ao. Mfumu idaafuna kuŵaumiriza, pakuŵazunza ndi zikoti ndi zingwe zokwapulira, kuti adye nyama yankhumba, imene Malamulo ankaletsa.
2Mmodzi mwa iwowo adalankhula m'malo mwa onse, adati, “Kodi mukuyembekeza kumva chiyani pakutifunsafunsa? Ifetu tili okonzeka kufa, koma zophwanya malamulo a makolo athu ai.”
3Mfumu idapsa mtima, ndipo idalamula kuti aike ziwaya ndi miphika pa moto.
4Antchito adachita zimenezo mwamsanga. Ndipo mfumu idalamula kuti amdule lilime amene ankalankhulayo, ndipo kuti asende khungu la pamutu pake, ndi kumdula manja ndi mapazi ake, abale akewo ndi amai ake omwe akuwona.
5Atampandula chotero, mfumu idalamula kuti amuike pa moto akupumabe, ndipo amkazinge pa chiwaya. Utsi wochokera pa chiwaya udadzaza ponsepo, koma amai ake ndi abale ake adalimbitsana mtima kuti afe mopanda mantha.
6Deut. 32.36Adati, “Ambuye Mulungu akutiyang'ana ndipo mosapeneka akutimvera chisoni, monga momwe Mose adaatsimikizira pa nyimbo yake yotsutsa anthu osamvera, imene imati, ‘Adzachitira atumiki ake chifundo.’ ”
7Woyambayo atafa chotero, adabwera ndi wachiŵiri kuti iyenso amuzunze. Ozunzawo adasenda khungu la kumutu kwake tsitsi lili komweko, ndipo adamfunsa kuti, “Kodi ukuvomera kudya nyama yankhumba, kapena tikudule chiwalochiwalo?”
8Iye adayankha m'chilankhulo cha makolo ake kuti, “Sindidya ai.” Tsono iyenso anthu adamuzunza ngati mbale wake woyamba uja.
9Ali pafupi kufa, iye adati, “Iwe woipawe, ukutilanda moyo uno, koma Mfumu ya zolengedwa zonse idzatiwukitsa kuti itipatse moyo wosatha, ife amene tikuphedwa chifukwa chomvera Malamulo ake.”
10Pambuyo pake adazunza wachitatu. Ozunzawo atamulamula, pompo iye adapereka lilime lake natambalitsa manja ake mopanda mantha.
11Adalankhula molimba mtima kuti, “Ndidalandira ziwalozi kwa Mulungu, koma tsopano kwa ine Malamulo ake ndiye chinthu chachikulu koposa ziwalozo. Ndipo ndikukhulupirira kuti Iyeyo adzandibwezera ziwalo zangazo.”
12Mfumu pamodzi ndi onse amene anali naye pomwepo adadabwa ndi kulimba mtima kwa mnyamatayo, popeza kuti mazunzowo sankaŵayesa kanthu.
13Atafa iyeyo, adazunza wachinai ndi mazunzo a mtundu womwewo.
14Ali pafupi kufa iye adati, “Ngodala amene aphedwa ndi anthu, nakhulupirira Mulungu kuti adzaŵaukitsa. Koma iwe Antioko, kuuka kopatsa moyo sudzakuwona ai.”
15Kenaka adabwera ndi wachisanu nayamba kumuzunzanso. Koma iye adapenyetsetsa mfumu, nati,
16“Iwe ngakhale ndiwe munthu chabe, uli ndi mphamvu zolamula anthu ena, ndipo umachita zokomera iweyo. Koma usamaganize kuti Mulungu wasiya mtundu wathu.
17Tadikira, udzaona mphamvu zake zazikulu zimene adzakusautsa nazo, iweyo pamodzi ndi zidzukulu zako.”
18Pambuyo pake adabwera ndi wachisanu ndi chimodzi. Ali pafupi kufa iye adati, “Usadzinyenge. Ifeyo tikuwona zovuta zimenezi chifukwa tidachimwira Mulungu wathu, nchifukwa chake zoipa zoterezi zatigwera.
19Koma iwe, usaganize kuti sudzalangidwa nako kulimbana ndi Mulungu ukuchitaku.”
20Mai wao ndiye adakhala wodabwitsa kupambana onse, ndipo ngwoyenera kumkumbukira ndithu. Ngakhale adaona ana ake alikufa tsiku limodzi, adapirira zimenezo molimba mtima chifukwa chokhulupirira Ambuye.
21Adalangiza aliyense m'chilankhulo cha makolo ake. Chifukwa cha nzeru zake zotamandika, adalimbitsa maganizo ake achikazi ndi mtima wachimuna.
22Adauza ana ake kuti, “Ine sindikudziŵa kaya inuyo mudapangidwa bwanji m'mimba mwanga. Mpweya ndi moyo sindidakupatseni ndine. Ziwalo za matupi anu, sindidakonze ndine.
23Adachita zimenezo ndi Mlengi wa zonse, amene amakonza za kubadwa kwa anthu ndi kulongosola chiyambi cha zinthu zonse. Mwa chifundo chake adzakubwezeraninso mpweya ndi moyo, poti mwadziiŵala chifukwa cha kukonda Malamulo ake.”
24Antioko ankaganiza kuti maiyo akumpeputsa, choncho adaipidwa nawo mau akewo. Popeza kuti mwana wamng'ono anali moyobe, mfumu idayesa kumkopa osati ndi mau chabe, koma adamlonjeza molumbira kuti adzampatsa chuma ndi zina zambiri zosiririka, akasiya miyambo ya makolo ake. Adatinso adzakhala bwenzi la mfumu nadzalandira udindo wapamwamba.
25Koma mnyamatayo sadasamale mau akewo. Apo mfumu idauza mai wake kuti amlangize mwana wakeyo nzeru zoti apulumutse moyo wake.
26Mfumuyo itakamba naye kwambiri, maiyo adavomera kutero.
27Koma atamuŵeramira mwana wake uja, adapusitsa mfumu yankhalweyo ponena m'chilankhulo cha makolo ake kuti, “Mwana wanga, undimvere chifundo. Ine ndidakusunga miyezi isanu ndi inai m'mimba mwanga, ndipo ndidakuyamwitsa zaka zitatu. Ndidakulera, ndidakudyetsa ndi kukusamala mpaka chaka chimene chino.
28Ndapota nawe mwana wanga, uyang'ane kumwamba ndi dziko lino lapansi. Uwone zonse zimene zimakhalamo, ndipo uzindikire kuti ndi Mulungu amene adazilenga zonsezo, pomwe panalibe kanthu kalikonse. Momwemonso adalenga mtundu wonse wa anthu.
29Usamuwope wopha anthuyu, koma ulimbe mtima ngati abale ako ndi kulola kufa, kuti mwa chifundo cha Mulungu iwenso ndidzakupeze pamodzi ndi abale akowo.”
30Mai wake akulankhulabe, mnyamatayo adati, “Kodi anthunu, mukudikira chiyani? Malamulo a mfumu sindiŵamvera, ine ndimamvera Malamulo amene Mose adasiyira makolo athu.
31Ndipo iwe amene udaganiza zoipa zamitundumitundu zosautsira Ahebri, dzanja la Mulungu sudzalilewa ai.
32Ifetu tikusauka chifukwa cha zolakwa zathu.
33Ambuye amoyo atikwiyira nthaŵi pang'ono, kuti atilange ndi kutiwongola, koma adzayanjananso ndi atumiki ake.
34Koma iwe wosamverawe, wonyansitsa kwambiri mwa anthu onse, usanyade mopusa ndi kukhulupirira zachabe pamene mukuzunza ana a Mulungu.
35Ndithu sunapulumukebe ku mlandu wa Mulungu Wamphamvuzonse amene amaona zonse.
36Abale athu atapirira zosautsa nthaŵi pang'ono, afika ku moyo wosatha umene Mulungu adatilonjeza. Koma iwe, Mulungu adzakuweruza ndipo udzalandira chilango cholingana ndi kunyada kwako.
37Ine monga momwe adachitira abale anga, ndikupereka pano thupi langa ndi moyo wanga, chifukwa cha malamulo a makolo athu. Ndikupempha Mulungu kuti amvere chifundo fuko lathu mwamsanga, koma akusautse iweyo ndi kukuzunza, mpaka utavomera kuti Iye yekha ndiye Mulungu.
38Ndikupemphanso kuti pa imfa yanga ndi ya abale anga, Wamphamvuzonse aleke pomwepo mkwiyo wake umene udaayeneradi kugwera fuko lathu lonse.”
39Pamenepo mfumu idapsa mtima kwambiri niipidwa nazo zonyozazo. Idazunza mnyamatayo kupambana ena aja.
40Tsono mwanayo adafa ali wangwiro, ataika chikhulupiriro chake mwa Ambuye.
41Potsiriza pake adapha mai wao, ana ake onse aja ataphedwa.
42Zithere pomwepa nkhani zosimba za m'mene Ayuda ankaŵakakamizira kuti adye zansembe zoletsedwa, ndiponso za kuzunzidwa kwao.
Nkhondo zoyamba za Yudasi wotchedwa MakabeoWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.