1Malo amene mumakhalamo, Inu Chauta Wamphamvuzonse,
ndi okoma kwambiri.
2Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,
kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta.
Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe
ndi mtima wanga wonse.
3Ngakhale timba amapeza malo okhalapo,
nayenso namzeze amamanga chisa chake
m'mene amagonekamo ana ake, pafupi ndi maguwa anu,
Inu Chauta Wamphamvuzonse,
Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
4Ngodala anthu amene amakhala m'Nyumba mwanu,
namaimba nyimbo zotamanda Inu nthaŵi zonse.
5Ngodala anthu amene mphamvu zao nzochokera kwa Inu,
amene m'mitima mwao amafunitsitsa
kudzera m'miseu yopita ku Ziyoni.
6Akamadutsa chigwa cha Baka chopanda madzi,
amachisandutsa malo a akasupe,
mvula yachizimalupsa imachidzaza ndi zithaphwi.
7Mphamvu zao zimanka zichulukirachulukira.
Mulungu wa milungu adzaoneka m'Ziyoni.
8Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,
imvani pemphero langa.
Tcherani khutu, Inu Mulungu wa Yakobe.
9Inu Mulungu, ndinu chishango chathu,
yang'anani nkhope ya wodzozedwa wanu.
10Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri
kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse.
Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga
kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa.
11Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango,
amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu.
Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
12Inu Chauta Wamphamvuzonse,
ngwodala munthu woika chikhulupiriro chake pa Inu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.