1“Iwe mwana wa munthu, ulalike zodzudzula Gogi. Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikudana nawe iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Meseki ndi ku Tubala.
2Ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira m'tsogolo. Ndidzakutenga kuchokera ku maiko akutali kumpoto, ndipo ndidzakutuma kuti ukalimbane ndi anthu okhala m'mapiri a ku Israele.
3Pambuyo pake ndidzathyola uta wa ku dzanja lako lamanzere, ndipo ndidzagwetsa mivi ya ku dzanja lako lamanja.
4Udzagwa ku mapiri a ku Israeleko, iweyo pamodzi ndi magulu ako onse ankhondo ndi onse amene amakuthandiza. Ndidzakusandutsa chakudya cha miimba ndi cha zilombo zakuthengo.
5Udzafera kuthengo, poti ndagamula choncho Ineyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
6Ndidzagwetsa moto pa dziko la Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere m'mbali mwa nyanja. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
7Ndidzamveketsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Aisraele. Ndipo sindidzalola kuti dzina langa liipitsidwenso. Anthu a m'maiko onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndine Woyera uja wa ku Israele.
8“Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithu zilikudza, zidzachitikadi. Ndiye tsiku limene ndidanena lija.
9Okhala m'mizinda ya Aisraele adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo zosiyidwa kuti azitenthe ngati nkhuni: ndiye kuti zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga ndi mikondo. Adzazisonkhere moto pa zaka zisanu ndi ziŵiri.
10Sadzatolera nkhuni ku thengo kapena kusalika zina ku nkhalango. Moto wao azidzasonkha ndi zidazo. Motero adzafunkha oŵafunkha, ndipo adzabera oŵabera. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Gogi aikidwa m'manda11“Pa tsiku limenelo Gogi ndidzampatsa malo a manda oti amuikemo ku dziko la Israele, m'chigwa cha anthu apaulendo, kuvuma kwa Nyanja Yakufa. Chigwacho chidzatsekera njira anthu odzera kumeneko, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzaikidwa kumeneko, ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
12Aisraele adzakhala akukwirira mitembo pa miyezi isanu ndi iŵiri, kuti ayeretse dziko.
13Anthu onse am'dzikomo adzakwirira nao, ndipo ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetse ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
14Miyezi isanu ndi iŵiri itapita, adzasankha anthu odzayendera m'dziko lonselo, kuti azifunafuna mitembo imene idatsalira ndi kumaikwirira, motero adzaliyeretseratu dzikolo.
15Popita m'dzikomo, azidzati wina akaona fupa la munthu, azidzaika chizindikiro pambali pake, mpaka fupalo litakwiriridwa m'chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
16Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu lankhondo. Motero dzikolo lidzakhala loyeretsedwa.”
17 Chiv. 19.17, 18 “Ndiye iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Uitane mbalame ndi nyama zonse zakuthengo, uziwuze kuti, ‘Sonkhanani mubwere kuno. Musonkhane kuchokera kumbali zonse. Mubwere ku phwando limene ndikukukonzerani ku mapiri a Israele. Phwando lake ndi lansembe. Kumeneko mudzadya nyama ndi kumwa magazi.
18Mudzadya nyama ya ankhondo amphamvu, ndipo mudzamwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo adaphedwa ngati nkhosa zamphongo, anaankhosa, mbuzi ndiponso ngati ng'ombe zamphongo zonenepa za ku Basani.
19Ku phwando lansembe limene ndikukukonzeranilo, mudzadya zonona mpaka kukhuta, mudzamwa magazi mpaka kuledzera.
20Zoonadi ku tebulo langa mudzakhuta podya akavalo ndi okwerapo ake, ankhondo amphamvu ndi asilikali amitundumitundu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Aisraele adzaŵabwezera pabwino21“ ‘Ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu yonse. Ndipo adzaona m'mene ndidzaŵalangire ndi dzanja langa, limene ndidzaŵasanjike.
22Kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, Aisraele adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wao.
23Anthu a m'maiko onse adzadziŵa kuti Aisraele adaatengedwa ukapolo chifukwa cha machimo ao, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho ndidaŵafulatira, ndipo ndidaŵapereka m'manja mwa adani ao. Motero onsewo adafa pa nkhondo.
24Ndidaŵachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwao ndi machimo ao, ndipo ndidaŵafulatiradi.
25“ ‘Tsono zimene Ine Ambuye Chauta ndikunena ndi izi: Tsopano a m'fuko la Yakobe ndidzaŵakhazikanso pabwino. Aisraelenso onse ndidzaŵachitira chifundo. Dzina langa loyera ndidzaliteteza.
26Anthuwo akadzakhazikika mwamtendere m'dziko lao, popanda wina woŵavuta, pamenepo adzaiŵala zamanyazi zao zimene zidaŵagwera chifukwa chosandikhulupirira Ine.
27Ndidzaŵabwezera kwao kuŵachotsa pakati pa mitundu ina ya anthu, ndi kuŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko a adani aowo. Motero ndidzaonetsa pamaso pa mitundu yambiri ya anthu kuti ndinedi Woyera.
28Choncho adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wao. Paja ndidaaŵatumiza ku ukapolo pakati pa mitundu ina ya anthu, kenaka ndidaŵabwezanso onse ku dziko lao, osasiyako ndi mmodzi yemwe.
29Sindidzaŵafulatiranso, popeza kuti ndidzatumiza mzimu wanga kwa Aisraele. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ”
EZEKIELE AONA NYUMBA YA MULUNGU YATSOPANO M'MASOMPHENYAWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.