1Mulungu ndi wodziŵika m'dziko la Yuda,
dzina lake ndi lolemekezeka mu Israele.
2Hema lake adalimanga ku Yerusalemu.
Malo ake okhalamo ali kumeneko ku Ziyoni.
3Kumeneko adathyola mivi youluzika,
zishango, malupanga
ndi zida zonse zankhondo za adani ake.
4Inu Mulungu, mukuwonetsa ulemerero ndi mphamvu
kupambana mapiri a zofunkha.
5Mudalanda zofunkha za anthu olimba mtima,
mudaŵagonetsa tulo tofa nato,
ankhondo onse sankatha kuchita kanthu ndi manja ao.
6Pamene mudaŵaopsa, Inu Mulungu wa Yakobe,
onse okwera pa akavalo ndi akavalo ao omwe
adagwa nangoti kakasi.
7Zoonadi, Inu ndinu woopsa.
Angathe kuima pamaso panu ndani
pamene mkwiyo wanu wayaka?
8Chiweruzo chanu mudachilengeza kumwamba,
anthu a pa dziko lapansi adaopa nakhala chete,
9pamene Inu Mulungu mudaimirira kuti muweruze anthu,
ndi kupulumutsa opsinjidwa onse a pa dziko lapansi.
10Zoonadi, mkwiyo wa anthu umabweretsa ulemu kwa Inu,
opulumuka ku mkwiyowo mumaŵasunga pafupi ndi Inu.
11Lumbirani kwa Chauta, Mulungu wanu,
ndipo muchitedi zimene mwalumbirazo.
Onse omzungulira abwere ndi mphatso
kwa Iye amene ayenera kumuwopa,
12ndiye amene amathetsa mphamvu akalonga
ndipo amaopsa mafumu a pa dziko lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.