Hos. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1“Ansembe inu, imvani izi!

Aisraele inu, mumvetsere nonse.

Inu a m'banja la mfumu, mvetserani mau anga.

Chilango chidzakugwerani,

chifukwa inu munali msampha ku Mizipa,

mudachita ngati kuyala ukonde ku phiri la Tabori.

2Opandukawo azama kwambiri m'machimo ao,

Ine ndidzaŵalanga onsewo.

3“Aefuremu ndikuŵadziŵa,

Aisraele ndi osabisika kwa Ine.

Aefuremu akhala osakhulupirika,

Aisraele adziipitsa.”

Hoseya achenjeza za kupembedza mafano

4Ntchito zao zoipa zatseka njira yao

yobwerera kwa Mulungu wao,

pakuti mtima wa kusakhulupirika uli mwa iwo,

ndipo salabadako za Chauta.

5Kudzikuza kwa Israele

kwasanduka umboni womutsutsa.

Zoonadi Efuremu adzagwa ndi machimo ake.

Nayenso Yuda adzateronso.

6Anthu amapereka nsembe zankhosa ndi zang'ombe

pofunafuna Chauta,

koma samupeza, waŵachokera.

7Adachita zosakhulupirika kwa Chauta,

motero ana ao nawonso si ake a Mulungu.

Tsono chipembedzo chao chachikunja chidzaŵaonongetsa

pamodzi ndi minda yao.

Nkhondo pakati pa Yuda ndi Israele

8Imbani malipenga ankhondo ku Gibea!

Lizani mbetete ku Rama!

Chenjezani a ku Betehaveni!

Inu a ku Benjamini tsogolani!

9Efuremu adzasanduka bwinja pa tsiku lachilango.

Ndikulengeza zoona kwa inu nonse Aisraele.

10Chauta akuti,

“Atsogoleri a ku Yuda amachita nkhondo

kuti afutuze malire.

Nchifukwa chake ndidzaŵamiza ndi mkwiyo wanga

ngati madzi achigumula.

11Aefuremu akuŵapondereza,

akuŵalanga chifukwa chomvera za ena.

12Nchifukwa chake ndidzaononga Efuremu,

monga momwe njenjete zimaonongera nsalu,

ndidzakhala ngati chilonda choola pa anthu a ku Yuda.

13“Tsono anthu a ku Efuremu ataona kuti akudwala,

ndipo Ayuda ataona kuti ali ndi mabala,

Aefuremuwo adapita kwa Aasiriya,

Ayuda natuma uthenga kwa mfumu yaikulu,

kuti iŵathandize.

Koma siingathe kuŵachiritsa kapena kupoletsa mabala ao.

14Ndidzalumphira Aefuremu ngati mkango,

ndidzambwandira Ayuda ngati msona wa mkango.

Ine mwini ndidzaŵakadzula nkuchokapo.

Pamene ndizidzaŵaguza,

palibe wina aliyense wotha kudzaŵalanditsa.

15“Ndidzabwerera ku malo anga,

mpaka anthu anga atasaukiratu,

ndi kuyamba kundifunafuna.

M'mavuto ao adzayesetsa kundipeza.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help