Mt. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Wamkulu ndani?(Mk. 9.33-37; Lk. 9.46-48)

1 Lk. 22.24 Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adadzamufunsa Yesu kuti, “Kodi mu Ufumu wakumwamba wamkulu koposa onse ndani?”

2Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao,

3Mk. 10.15; Lk. 18.17ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.

4Nchifukwa chake munthu wodzichepetsa ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wakumwamba.

5Ndipo aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene.”

Za zochimwitsa(Mk. 9.42-48; Lk. 17.1-2)

6“Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukammiza m'nyanja pozama.

7Ali ndi tsoka anthu apansipano chifukwa cha zochimwitsa. Zochimwitsazo sizingalephere kuwoneka, koma ali ndi tsoka munthu wobweretsa zochimwitsayo.

8 Mt. 5.30 “Tsono ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli woduka dzanja kapena phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wosatha uli ndi manja onse kapena mapazi onse aŵiri.

9Mt. 5.29Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wa Gehena uli ndi maso aŵiri.”

Fanizo la nkhosa yotayika(Lk. 15.3-7)

10 Tob. 12.15 Lk. 19.10 “Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.”

[

11“Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzapulumutsa amene adatayika.”]

12“Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayika, kodi sangasiye 99 zina zija m'phiri nkukafunafuna imodzi yotayikayo?

13Ndithu ndikunenetsa kuti ataipeza, chimwemwe chake chokondwerera imeneyo chimapambana chokondwerera zina zija zimene sizidatayike.

14Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.

Zoyenera kuchita mbale akachimwa(Lk. 17.3)

15 Lk. 17.3 “Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.

16Deut. 19.15Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena aŵiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziŵiri kapena zitatu.

17Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho.

18 Mt. 16.19; Yoh. 20.23 “Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.

19“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani.

20Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Fanizo la wantchito wosakhululukira mnzake(Lk. 17.4)

21 Lk. 17.3, 4 Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?”

22Gen. 4.24Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.

23“Tsono Ufumu wakumwamba tingaufanizire motere: Panali mfumu ina imene idaaitanitsa antchito ake kuti iwonenso bwino ngongole zao.

24Atangoyamba kumene, adabwera ndi wantchito wina amene anali ndi ngongole ya ndalama zochuluka kwabasi.

25Ndiye popeza kuti adaasoŵa chobwezera ngongoleyo, mbuye wake uja adalamula kuti amgulitse wantchitoyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake ndi zake zonse, kuti ngongole ija ibwezedwe.

26Apo wantchito uja adamgwadira nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani ndithu zonse.’

27Mbuye wake uja adamumveradi chifundo, ndipo adamkhululukira ngongole ija, namlola kuti apite.

28“Koma pamene wantchitoyo ankatuluka, adakumana ndi mmodzi mwa antchito anzake, yemwe iye adaamkongoza ndalama zochepa. Adamgwira pa khosi mwaukali namuuza kuti, ‘Bweza ngongole yako ija.’

29Apo wantchito mnzake uja adadzigwetsa pansi ku mapazi ake nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani.’

30Koma iye adakana, nakamponyetsa m'ndende kuti mpaka abweze ndithu ngongoleyo.

31“Antchito anzake ena ataona zimenezi, adamva chisoni kwambiri. Adapita kukafotokozera mbuye wao zonsezo.

32Tsono mbuye wakeyo adamuitana namuuza kuti, ‘Wantchito woipa iwe, ine ndinakukhululukira ngongole yonse ija pamene unandidandaulira.

33Kodi sunayenera kuti iwenso umchitire chifundo wantchito mnzako, monga ndinakuchitira iwe chifundo?’

34Motero mbuye wakeyo adapsa mtima kwambiri, nampereka kuti akamzunze mpaka atabweza ngongole yonse ija.

35“Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help