1Ndipo anthu onse adasonkhana pamodzi pa bwalo la patsogolo pa Chipata cha Madzi. Tsono anthuwo adamuuza Ezara, amene anali mlembi, wansembe ndi mphunzitsi wa malamulo, kuti abwere ndi buku la Malamulo a Mose limene Chauta adaapatsa Israele.
2Pamenepo Ezarayo adabwera ndi buku la Malamulolo, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, ku msonkhano wa amuna ndi akazi ndi ana amene ankatha kumvetsa zinthu bwino.
3Tsono Ezara adaŵerenga bukulo atayang'ana bwalo la Chipata cha Madzi, kuyambira m'mamaŵa mpaka pa masana, pamaso pa amuna ndi akazi omwe, ndiponso onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Ndipo anthu onsewo ankatchera makutu kuti amve zoŵerengazo.
4Mlembi Ezara adaaimirira pa nsanja yamitengo, imene anthuwo adaamanga chifukwa cha msonkhanowo. Ku dzanja lake lamanja kudaaimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseiya. Ku dzanja lake lamanzere kudaaimirira Pedaya, Misaele, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndiponso Mesulamu.
5Tsono ataimirira pansanjapo, Ezara adafutukula buku, anthu onse akupenya. Pomwepo anthu onse adaimirira.
6Kenaka Ezara adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wamkulu!” Ndipo anthu onse adakweza manja nayankha kuti, “Inde momwemo, inde momwemo.” Pambuyo pake adaŵeramitsa mitu pansi ndipo adapembedza Chauta ali chizyolikire.
7Anthu ataimiriranso, Alevi adaŵathandiza kuti amvetse malamulo. Aleviwo anali aŵa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndiponso Pelaya.
8Aleviwo adaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu momveka bwino, ndipo adatanthauzira mauwo kuti anthu amvetse bwino.
9Tsono bwanamkubwa Nehemiya, pamodzi ndi Ezara wansembe ndi mphunzitsi wa malamulo, kudzanso Alevi amene ankaphunzitsa anthu, adauza anthu onse aja kuti, “Lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Ndiye kuti anthu onse ankalira atamva mau a Malamulowo.
10Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
11Choncho Alevi adacheteketsa anthu onse naŵauza kuti, “Musalirenso ai, pakuti lero ndi tsiku loyera, choncho musakhale ndi chisoni.”
12Pamenepo anthu onse adapita kwao kukadya ndi kumwa ndipo zakudya zina adagaŵirako anzao, kuti pakhale chikondwerero chachikulu, chifukwa chakuti tsopano anali atamvetsa bwino mau a Malamulo amene adaaŵerengedwawo.
Chikondwerero cha Misasa13Atsogoleri a mabanja, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, onse adabwera m'maŵa mwake kwa Ezara, mphunzitsi wa malamulo, kuti aphunzire mau a Malamulowo.
14Lev. 23.33-36, 39-43; Deut. 16.13-15 Tsono adapeza kuti m'buku la Malamulo mudalembedwa kuti Chauta adalamula kudzera mwa Mose kuti Aisraele azikhala m'zithando nthaŵi yonse ya chikondwerero cha pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri.
15Motero adafalitsa ndi kulengeza m'midzi yao yonse ndiponso m'Yerusalemu, kuti, “Pitani ku mapiri, mukatengeko nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wakuthengo, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa, ndiponso za mitengo ina ya masamba ambiri, kuti mumangire misasa monga momwe zidalembedwera.”
16Choncho anthuwo adapita nakatenga zonsezo ndipo aliyense adadzimangira misasa padenga pa nyumba yake, ndiponso m'mabwalo ao, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, m'bwalo la pa Chipata cha Madzi ndi m'bwalo la pa Chipata cha Efuremu.
17Motero onse amene adaasonkhana, ndiye kuti amene adaabwerako ku ukapolo, adamanga misasa, ndipo adakhala m'menemo. Kuyambira nthaŵi ya Yoswa, mwana wa Nuni, mpaka tsiku limenelo, Aisraele anali asanachitepo zoterozo. Motero kunali chikondwerero chachikulu kwambiri.
18Tsiku ndi tsiku kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lotsiriza, Ezara ankaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu. Anthu adachita chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu padachitika mwambo wotseka msonkhano, potsata buku la Malamulo lija.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.