1 Gen. 14.17-20 Melkizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wopambanazonse. Pamene Abrahamu ankabwerako kuchokera ku nkhondo, atagonjetsa mafumu aja, Melkizedeki adadzamchingamira, namdalitsa.
2Abrahamu adampatsa chigawo chachikhumi cha zonse zimene adaafunkha. Potsata tanthauzo la dzina lake, choyamba Melkizedeki ndi “Mfumu ya chilungamo,” pambuyo pake ndi “Mfumunso ya Salemu,” ndiye kuti, “Mfumu ya Mtendere”.
3Za bambo wake kapena mai wake, kapena makolo ake, palibe chilichonse chidalembedwa. Chimodzimodzi za kubadwa kwake ndi imfa yakenso. Ali ngati Mwana wa Mulungu, akupitiriza kukhala wansembe mpaka muyaya.
4Mukuwonatu tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu. Nanga Abrahamu, kholo lathu lija, kuchita kumpatsa chachikhumi cha zimene adaafunkha!
5Num. 18.21 Malamulo a Mose amati ana a Levi, amene ali ansembe, azilandira chachikhumi kwa Aisraele. Ndiye kuti iwo amalandira kwa abale ao, ngakhale abalewo nawonso ndi ana a Abrahamu.
6Melkizedeki sanali m'gulu la zidzukulu za Levi, komabe adalandira chachikhumi kwa Abrahamu. Ndipo adadalitsa Abrahamu, munthu amene anali atalandira malonjezo a Mulungu.
7Paja nchodziŵikiratu kuti munthu wodalitsa mnzake ndiye wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo.
8Kunena za ansembe olandira chachikhumi aja, amene ndi zidzukulu za Levi, iwoŵa ndi anthu otha kufa. Koma kunena za Melkizedeki, Malembo amamchitira umboni kuti ngwamoyo.
9Kwenikweni tingathe kunena kuti pamene Abrahamu ankapereka chachikhumi, Levi yemwe, amene amalandira chachikhumi, adaapereka nao chachikhumicho.
10Pakuti iye anali akadali m'thupi la kholo lake Abrahamu pamene Melkizedeki adadzamchingamira.
11Malamulo amene Aisraele adalandira, anali okhazikika pa unsembe wa Levi. Tsono achikhala kudaali kotheka kukhala angwiro mwa unsembe umenewu, sikukadafunikanso unsembe wina, wonga uja wa Melkizedeki, wosiyana ndi wonga uja wa Aroni.
12Pakuti pakakhala kusintha pa unsembe, ndiye kuti pa Malamulonso sipangalephere kukhala kusintha.
13Ambuye athu, amene mauŵa akunena za Iwo, anali a fuko lina. Ndipo palibiretu wa fuko limeneli amene adatumikirapo ku guwa lansembe.
14Nchodziŵikiratu kuti Ambuye athu aja anali a fuko la Yuda, ndipo Mose pokamba za fuko limeneli, sadanenepo kanthu za ansembe.
Za wansembe wina wonga Melkizedeki15Nkhaniyi imamveka bwino koposa pamene tiwona kuti pafika wansembe wina wonga Melkizedeki.
16Iyeyo sadakhale wansembe chifukwa cha malamulo okhudza kubadwa kwa anthu, koma chifukwa cha mphamvu za moyo wake umene uli wosatha.
17Mas. 110.4 Paja mau a Mulungu pomuchitira umboni akuti,
“Ndiwe wansembe mpaka muyaya,
unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
18Motero lamulo lakale lalekeka chifukwa linali lopanda mphamvu, linali lopanda phindu.
19Pajatu Malamulo a Mose sankatha kusandutsa munthu kuti akhale wangwiro. Koma m'malo mwake mwaloŵa chiyembekezo choposa, ndipo mwa chiyembekezo chimenechi timayandikira kwa Mulungu.
20Chinanso nchakuti Mulungu adaachita kulumbira. Amene ankaloŵa unsembe kale lija ankatenga udindo waowo popanda lumbiro.
21Mas. 110.4 Koma Yesu adaloŵa unsembe wake ndi lumbiro, pamene Mulungu adamuuza kuti,
“Ambuye adalumbira,
ndipo sadzasintha maganizo ake akuti,
ndiwe wansembe mpaka muyaya.”
22Kusiyana kokhudza lumbiroku kukutiwonetsa kuti Yesu ndi Nkhoswe yotsimikizira Chipangano choposa.
23Kusiyana kwina nkwakuti ansembe akale aja anali ambiri, chifukwa ankafa, sankatha kupitirira ndi udindo waowo.
24Koma Yesu ngwamuyaya, motero unsembe wake ngwosasinthika.
25Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.
26Tsono padaafunika kuti tikhale naye wotere mkulu wa ansembe onse: woyera mtima, wopanda choipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kubzola zonse zakumwambaku.
27Lev. 9.7 Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe.
28Malamulo a Mose amaika anthu amene ali ndi zofooka, kuti akhale akulu a ansembe onse. Koma mau a lumbiro la Mulungu lija limene lidabwera pambuyo pa Malamulowo, adaika Mwana wake, amene wakhala wangwiro kwamuyaya kuti akhale mkulu wa ansembe onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.