1 Eks. 22.25; Lev. 25.35-38 Kukongoza mnzako ndi ntchito yachifundo,
kuthandiza mnzako ndiye kusunga malamulo.
2Mnzako akasauka umkongoze,
iweyo ukakhala ndi ngongole uzibweza msanga.
3Uzisunga mau ako ndi kukhala wokhulupirika kwa mnzako,
ndipo zonse zimene usoŵa udzazipeza bwino.
4Anthu ambiri amayesa kuti ngongole ndi mwai,
ndipo amavutitsa amene adaŵathandiza.
5Anthu ena amachita gwadugwadu kwa anzao kuti aŵakongoze,
amanong'ona pokamba za chuma cha mnzaoyo,
koma nthaŵi ikafika kuti abweze ngongole amazengereza,
amangobweza mau chabe ndi kudandaula kuti nthaŵi yachepa.
6Womkongozayo akamlonjerera mopanikiza,
iye amangobwezako pafupi hafu chabe.
Akalandirako hafuyo wokongoza uja amati ndi mwai.
Ngati wokongolayo sabweza,
ndiye kuti wokongoza uja watayadi ndalama zake,
ndipo wasanduka mdani popanda chifukwa.
Kenaka wokongola uja amayamba kutemberera ndi
kunyoza womkongozayo,
ndiye kuti m'malo mwa ulemu amambwezera chipongwe.
7Anthu ambiri amakana kukongoza,
osati chifukwa chouma mtima,
koma amaopa kutaya ndalama pachabe.
Za kuthandiza osauka8Komabe uziŵalezera mtima anthu osauka,
usamachedwe poŵachitira chifundo.
9Paja Malamulo amati, uzithandiza osauka,
usaŵabweze kwao ali chimanjamanja.
10Ndalama zako uziwonongerako bwenzi lako
kapena mbale wako,
zisachite dzimbiri ndi kuwonongeka utazikumbira pansi.
11Udziikire chuma potsata lamulo la Mulungu
Wopambanazonse.
Zimenezi zidzakuthandiza kupambana kukhala
ndi golide.
12Mosungira chuma uunjike ndalama zochitira
ntchito zachifundo,
zidzakupulumutsa pa mavuto onse.
13Chifundo chidzakutchinjiriza kwa mdani wako
kupambana chishango cholimba kapena mkondo wamphamvu.
Za zigwiriro14Munthu wabwino amapereka chigwiriro pamalo pa mnzake,
koma wopanda manyazi yekha ndi amene angakane
kumthandiza mnzakeyo.
15Ngati wina akuchitira zabwino zotero,
usaiŵale chifundo chakecho,
poti iye wadzipereka chifukwa cha iwe.
16Munthu woipa amangomwaza chuma cha amene
wamthandizapo,
17ndipo wosadziŵa kuyamika amaiŵala amene adampulumutsa.
18Kupereka chigwiriro pofuna kuthandiza ena
kudaonongeratu chuma cha anthu olemera ambiri,
ndipo kunaŵagwedeza ngati namondwe pa nyanja.
Kudakankhanso anthu omveka kuchoka kwao
ndi kumangoyendayenda m'maiko achilendo.
19Munthu woipa akakhalira ena mboni kuti
apezepo phindu,
adzangoputa milandu.
20Tsono uzimthandiza mnzako monga ungathere,
koma uchenjere kuti ungagwe m'mavuto nawenso.
Za ufulu wapanyumba21Zinthu zofunikira kwenikweni pa moyo ndi izi:
madzi, chakudya, zovala ndi nyumba yokhalamo.
22Ndi bwino kukhala wosauka
koma uli ndi nkako kakhumbi,
kupambana kumadya bwino
koma muli m'nyumba mwa wina.
23Kaya uli ndi zinthu zochepa kaya zambiri,
ukhutire nazo,
motero sadzakunena kuti umangodya nawo kwa ena.
24Ndi moyo wovutika kumangodikiza m'makomo mwa anthu.
Kumene wakakhala mlendoko, palibe chimene
unganenepo.
25Udzalandira alendo,
udzapatsa anthu zakumwa, iwo osathokoza,
m'malo mwake adzakupeputsa nkumati,
26“Mlendo iwe, bwera kuno, konza tebuloli.
Wakonza chiyani?
Bwera nacho ndidye.
27Mlendo iwe, tachoka pamenepa, akhalepo olemekezekaŵa.
Mbale wanga wadzandiyendera, ndikuŵafuna maloŵa.”
28Kwa munthu wanzeru nchinthu chopweteka:
kumtonzera ufulu,
kumchititsa manyazi ngati a munthu wangongole.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.