Amo. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atsutsa akazi a ku Samariya

1Mverani mau aŵa akazi inu okhala ku Samariya

amene mukungonenepa

ngati ng'ombe za m'dera la Basani,

inu amene mumavutitsa osauka

ndi kuzunza osoŵa.

Ntchito nkumangolamula amuna anu kuti,

“Tipatseni zoziziritsa kukhosi.”

2Ambuye Chauta, ndi kuyera kwao kuja,

alumbira kuti,

“Pali Ine ndemwe,

masiku a chilango chanu akudza ndithu!

Nthaŵiyo anthu adzakuguguzani ndi ngoŵe.

Adzakukokani ndi mbedza nonse mpaka wotsiriza.

3Mudzatulukira m'ming'alu ya malinga,

aliyense payekhapayekha

ndipo adzakutayani ku phiri la Halimoni.”

Akuterotu Chauta.

Aisraele alephera kuphunzirapo kanthu

4“Bwerani ku malo oyera ku Betele,

mudzachimwireko.

Bweranazoni nsembe zanu m'maŵa mulimonse,

bweranazoni zopereka zanu zachikhumi pa

masiku atatu aliwonse.

5Mupereke buledi wanu kuti muthokoze Mulungu.

Munene poyera ndi kulengeza zopereka zanu zaufulu,

pakuti nzimene mumakonda kuchita, inu Aisraele.”

Akutero Chauta.

6 Lun. 12.2, 10 “Ndine amene ndidakusendetsani milomo

m'mizinda yanu yonse.

Ndine amene ndidagwetsa njala konse kumene munkakhala.

Komabe simudabwerere kwa Ine.”

Akutero Chauta.

7“Ndinenso amene ndidamanga mvula

patangotsala miyezi itatu kuti mukolole.

Ndine amene ndinkagwetsa mvula pa mudzi wina,

koma pa mudzi wina ai.

Mvula inkagwa pa munda wina,

koma munda wina nkumakhala gwa,

chifukwa chosoŵa mvula.

8Motero midzi iŵiri kapena itatu

inkapita ku mudzi umodzi kuti ikamwe madzi,

koma osaŵakwanira.

Komabe simudabwerere kwa Ine.”

Akutero Chauta.

9“Ndidaumitsa mbeu zanu ndi matenda

ndiponso ndi chinoni.

Chidafotetsa mbeu za m'minda yanu yonse

ndi yamphesa yomwe.

Dzombe lidaononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi,

komabe simudabwerere kwa Ine.”

Akutero Chauta.

10“Ndidakugwetserani miliri yonga ya ku Ejipito ija.

Ndidaphetsa achinyamata anu ku nkhondo,

ndidapereka akavalo anu kwa adani.

Ndidakununkhitsani fungo la mitembo

lochokera ku misasa yanu yankhondo.

Komabe simudabwerere kwa Ine.”

Akutero Chauta.

11 Gen. 19.24 “Ndidaononga ena mwa inu,

monga momwe ndidaonongera Sodomu ndi Gomora.

Otsaliranu munali ngati zikuni zofumula pa moto.

Komabe simudabwerere kwa Ine.”

Akutero Chauta.

12“Tsono inu Aisraele ndidzakuteroni.

Ndipo chifukwa choti ndidzakuchitani zimenezi,

inu Aisraele,

konzekani kuti mukumane ndi Mulungu wanu.”

13Tsono tamvani,

Iyeyo ndiye amene amaumba mapiri

ndi kupanga mphepo,

ndiye amene amaululira munthu

za m'maganizo mwake,

ndiye amene amasandutsa usana kuti ukhale usiku,

ndiye amene amayenda pa zitunda za dziko lapansi.

Dzina lake ndi Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help