Yer. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Uchimo wa Yerusalemu

1“Thamangani uku ndi uku m'miseu ya Yerusalemu,

mudziwonere nokha.

Funafunani ku mabwalo ake

ngati mungapezeke munthu,

munthu wake wochita zolungama,

wofunitsitsa zoona,

kuti choncho Yerusalemu ndidzamkhululukire.

2Ngakhale anthu akulumbira m'dzina la Chauta wamoyo,

komabe akungolumbira monama.

3Kodi Inu Chauta, suja mumafuna anthu onena zoona?

Inu mudaŵakantha anthuwo,

koma iwo sadamve kuŵaŵa.

Mudaŵatswanya,

koma sadafune kutembenuka mtima.

Adaumitsa mitima yao ngati mwala,

adakana kwamtuwagalu kulapa.”

4Apo ndidati, “Ndi amphaŵi chabe aŵa,

alibe ndi nzeru zomwe.

Iwo sadziŵa njira ya Chauta,

sazindikira zimene Mulungu wao akufuna.

5Tsono ndidzapita kwa akuluakulu,

ndidzalankhula ndi amenewo.

Pakuti ndiwo angadziŵe njira ya Chauta,

ndi zimene Mulungu wao akufuna.”

Koma ndidaona kuti iwowonso adathyola goli la Chauta,

adadula nsinga zao.

6Nchifukwa chake mkango wam'malunje udzaŵapha,

mmbulu wochoka ku thengo udzaŵaononga.

Kambuku adzaŵalalira pafupi ndi mizinda yao.

Ndipo adzakadzula aliyense wotuluka,

poti zolakwa zao nzambiri,

abwereratu m'mbuyo kwambiri.

7Chauta akuti,

“Kodi ndingakukhululukireni bwanji pa zonsezi?

Ana anu adandisiya Ine,

ndipo adapembedza milungu imene siili milungu konse.

Ine ndidaŵapatsa zonse zimene ankasoŵa,

komabe adakonda kumachita chigololo,

namapita ku nyumba za akazi adama.

8Aliyense ankathamangira mkazi wa mnzake,

monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa.

9Ndiye ndingapande kuŵalanga chifukwa cha zimenezi?

Monga ndisaulipsire mtundu wochita zotere?

10Tsono ndidzatuma adani

kuti akaononge mizere ya mipesa yao,

komabe osati kotheratu.

Akasadze nthambi zake,

poti anthu ameneŵa si ake a Chauta.

11Anthu a ku Israele ndi a ku Yuda

onse akhala osakhulupirika kwa Ine,”

akuterotu Chauta.

Chauta akana Israele

12Anthuwo ankanama ponena za Chauta,

ankati, “Mulungu sangatichite kanthu.

Choipa sichidzatigwera,

sitidzaona nkhondo kapena njala.

13Mau a aneneri azikangopita ngati mphepo,

ndipo uthenga wao si wa kwa Mulungu.

Zimene amanena zidzaŵagwera iwo omwewo.”

14Nchifukwa chake tsono Chauta,

Mulungu Wamphamvuzonse, akuti,

“Poti iwowo atero,

mau anga ndidzaŵasandutsa moto m'kamwa mwako,

anthuwo ndidzaŵasandutsa nkhuni,

ndipo motowo udzaŵapserezeratu.”

15“Iwe Israele, ndikukudzetsera mtundu

wa anthu odzakuthira nkhondo,

mtundu wake ndi wochokera kutali.

Mtundu umenewu ndi wosagonjerapo,

mtundu wakalekale,

mtundu umene chilankhulo chake iwe suchidziŵa,

ndipo zimene akunena, iwe sungazimvetse.

16Ankhondowo mipaliro yao imapha anthu ambirimbiri,

onsewo ndi ngwazi zokhazokha pa nkhondo.

17Adzakutherani zokolola zanu ndi chakudya chanu.

Adzapha ana anu aamuna ndi aakazi,

adzakupheraninso nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu.

Adzaononga mipesa yanu ndi mikuyu yanu.

Adzagwetsa mwankhondo

mizinda yanu yamalinga imene mumaidalira.

18“Koma ngakhale pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu.

19Ndipo mukamafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta Mulungu wathu watichita zimenezi?’ Iwe Yeremiya uzidzayankha kuti, ‘Monga momwe mudasiyira Chauta, ndi kumatumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemonso ndimo m'mene inuyo muzidzatumikira anthu a m'dziko lachilendo.’ ”

20Mulalike kwa ana a Yakobe,

mulengeze kwa anthu a ku Yuda kuti,

21 Yes. 6.9, 10; Ezek. 12.2; Mk. 8.18 “Imvani izi,

inu anthu opusa, opanda ndi nzeru zomwe,

inu amene maso muli nawo, koma simupenya,

amene makutu muli nawo, koma simumva.

22 Yob. 38.8-11 Ine Chauta ndikuti,

Kodi simukuchita nane mantha?

Kodi simukunjenjemera pamaso panga?

Ndine amene ndidaika mchenga

kuti ukhale malire a nyanja,

malire amene nyanjayo singaŵabzole.

Mafunde ake, ngakhale aŵinduke bwanji,

sangathe kupitirirapo.

Ngakhale akokome chotani, sangathe kubzola.

23Koma anthu ameneŵa ndi okanika

ndiponso a mtima waupandu.

Adapatuka ndipo adapitiratu.

24Sadanenepo m'mitima mwao kuti,

‘Tiyeni tizimvera Chauta Mulungu wathu,

amene amatipatsa mvula pa nthaŵi yake,

mvula yachizimalupsa ndi yam'masika.

Ndipo salephera kutipatsa

nthaŵi ya kholola.’ ”

25Koma zolakwa zanu zaletsetsa zonsezi,

ndipo machimo anu akumanitsani zokoma.

26Paja mwa anthu anga muli ena achifwamba,

amene amalalira anzao

monga m'mene amachitira otchera mbalame.

Amatcha misampha nakola anthu.

27Nyumba zao nzodzaza ndi chuma chochipeza mwachinyengo,

ngati chitatanga chodzaza ndi mbalame.

Nchifukwa chake adasanduka otchuka ndi olemera.

28Adanenepa nkukhala a matupi osalala.

Ntchito zao zoipa nzopanda malire,

saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye,

kuti iyende bwino,

ndipo sateteza amphaŵi.

29Chauta akuti,

“Ndiye ndingapande kuŵalanga chifukwa cha zimenezi?

Monga ndisaulipsire mtundu wochita zotere?”

30M'dziko muno mwachitika chinthu chododometsa

ndi choopsa.

31Aneneri akulosa zabodza,

ndipo ansembe akuvomerezana nawo.

Komabe anthu anga akukondanso zomwezo.

Kodi mudzatani potsiriza?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help