1Pambuyo pake Ahitofele adauza Abisalomu kuti, “Mundilole ndisankhule anthu okwanira 12,000, ndinyamuke nawo kuti ndimthamangire Davide usiku uno.
2Tsono ndikamthira nkhondo atatopa ndiponso atataya mtima, ndipo ndikamchititsa mantha. Anthu onse amene ali naye adzathaŵa. Pamenepo ine ndidzangopha mfumu yokhayo.
3Tsono anthu onse ndidzabwera nawo kwa inu, ngati mkwati amene akubwerera kwa mwamuna wake. Imfa ya munthu mmodzi yekha, idzakhalitsa anthu onse pa mtendere.”
4Uphunguwo udakomera Abisalomu ndi atsogoleri onse a Aisraele.
5Apo Abisalomu adati, “Muitanenso Husai, Mwariki, ndipo timvenso zimene anene.”
6Husai atabwera kwa Abisalomu, Abisalomuyo adamuuza kuti, “Zimene wanena Ahitofele nzimenezi, kodi tichitedi monga m'mene watilangiziramo? Ngati si choncho, iweyo utiwuze chochita.”
7Husai adauza Abisalomu kuti, “Ulendo uno, malangizo amene wakupatsani Ahitofele si abwino konse.
8Mukudziŵa kuti bambo wanu ngwamphamvu, anthu akenso ngamphamvu, ndipo kuti onse ngokwiya ngati zimbalangondo zolandidwa ana ku thengo. Kuwonjezera pamenepo, bambo wanu ndi katswiri wa nkhondo. Sangagone pamodzi ndi anthu ake ankhondo usiku.
9Onani, ngakhale tsopano lino akubisala m'phanga lina, kapena ku malo ena ake. Motero ena mwa anthu anu atangophedwa poyamba pomwe, aliyense amene adzamve adzanena kuti, ‘Anthu amene ankatsata Abisalomu aphedwa.’
10Tsono ngakhale munthu wolimba mtima ngati mkango adzaguluka m'nkhongono. Paja Aisraele onse akudziŵa kuti bambo wanu ndi munthu wamphamvu, ndipo kuti anthu amene ali nawowo ngolimba mtima.
11“Ine malangizo anga ndi aŵa: Aisraele onse adzasonkhane kwa inu kuno, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, adzakhale ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Ndipo inu nomwe mudzapite nawo ku nkhondo.
12Tsono ife tidzampeza Davide kulikonse kumene adzapezeke, ndipo tidzamthira nkhondo monga m'mene mame amagwera ponseponse pa nthaka. Sipadzapulumuka ndi munthu mmodzi yemwe.
13Akakaloŵa mumzinda mwina, Aisraele onse adzabwera ndi zingwe kumzindako. Mzinda umenewo tidzauguzira ku chigwa, ndipo sipadzapezeka ndi kamwala komwe kumeneko.”
14Atamva zimenezi Abisalomu ndi Aisraele onse adati, “Malangizo koma aŵa a Husai Mwarikiyu, osati a Ahitofele aja ai.” Zidatero chifukwa Chauta ndiye adaakonza kuti malangizo abwino a Ahitofele alephereke, zinthu zisamuyendere bwino Abisalomu.
Husai achenjeza Davide.15Kenaka Husai adauza Zadoki ndi Abiyatara, ansembe aja, kuti, “Zimene Ahitofele adaalangiza Abisalomu ndi atsogoleri a Aisraele ndi izi, izi. Koma ineyo ndaŵalangiza izi, izi.
16Ndiye inu tsono mutumize mau mwamsanga kwa Davide omuuza kuti asagone pa madooko a Yordani ku chipululu. Koma mwa njira iliyonse, aoloke ndithu, kuti iye pamodzi ndi anthu onse amene ali naye angagwidwe ndi kuphedwa.”
17Tsono mwachizoloŵezi Yonatani ndi Ahimaazi ankadikira ku Enirogele, pafupi ndi Yerusalemu. Mdzakazi ndiye ankapita kukaŵauza zinthu, ndipo iwowo ankapita kukauza mfumu Davide. Pakuti iwowo sankayenera kuwonekera poloŵa mu mzinda.
18Koma tsiku lina mnyamata wina adaŵaona, nakauza Abisalomu. Choncho Yonatani ndi Ahimaazi adathaŵa mofulumira, nakafika ku Bahurimu ku nyumba ya munthu wina, amene anali ndi chitsime pakhomo pake. Aŵiriwo adatsikira m'chitsimemo.
19Tsono mkazi wa munthu uja adatenga chivundikiro, nachiika pamwamba pa chitsimecho, nkuyanikapo tirigu, kotero kuti chitsimecho sichinkadziŵika.
20Ankhondo a Abisalomu atabwera kwa mkaziyo kunyumba kuja, adamufunsa kuti, “Kodi mwaonako Ahimaazi ndi Yonatani pano?” Mkazi uja adaŵayankha kuti, “Amenewo aoloka mtsinjewu.” Koma ataŵafunafuna, osaŵapeza, ankhondowo adabwerera ku Yerusalemu.
21Ankhondo aja atapita, anthuwo adatuluka m'chitsime muja, ndipo adakauza mfumu Davide kuti, “Nyamukani, muwoloke mtsinje mofulumira, popeza kuti Ahitofele walangiza anthu ake zokuthirani nkhondo.”
22Pompo Davide adanyamukadi pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, naoloka mtsinje wa Yordani. Pamene kunkacha, nkuti anthu onse atatha kuwoloka Yordani.
23Ahitofele ataona kuti anthu sadatsate malangizo ake aja, adakwera bulu wake, napita kwao ku mzinda wake. Tsono adakonza zonse za m'nyumba mwake, nadzikhweza. Motero adafa, ndipo adaikidwa m'manda a bambo wake.
24Davide adafika ku Mahanaimu. Abisalomu adaoloka Yordani pamodzi ndi Aisraele onse aja.
25Abisalomu adaaika Amasa kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo m'malo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wina dzina lake Yetere Mwismaele, amene adaakwatira Abigala, mwana wa Nahasi, mlongo wa Zeruya amake a Yowabu.
26Tsono Aisraele pamodzi ndi Abisalomu adamanga zithando zankhondo m'dziko la Giliyadi.
27Davide atafika ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi Mwamoni wochokera ku Raba, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndiponso Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,
28adabwera ndi mabedi ambiri, mabeseni ambiri, ziŵiya zadothi, tirigu, barele, ufa, tirigu wokazinga, nyemba ndi mphodza.
29Adabweranso ndi uchi, chambiko, nkhosa ndi mafuta olimba a mkaka wang'ombe. Zonsezi adabwera nazo kuti Davide adye pamodzi ndi anthu amene anali naye. Iwowo ankati, “Anthuŵa ali ndi njala, atopa ndipo ali ndi ludzu kuchipululuko.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.