1Abale, ndikulankhulatu ndi inu amene mumadziŵa za malamulo. Mukudziŵa bwino kuti malamulo amamkhudza munthu pokhapokha pamene munthuyo ali moyo.
2Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja.
3Nchifukwa chake ngati adzipereka kwa mwamuna wina, pamene mwamuna wake ali moyo, mkaziyo amati ngwachigololo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi uja wamasuka ku malamulo a ukwati, kotero kuti sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
4Chimodzimodzi inunso, abale anga. Mudachita ngati kufa ndi kulekana ndi Malamulo popeza kuti ndinu ziwalo za thupi la Khristu. Motero tsopano ndinu a wina wake, ndiye kuti a Iye amene adauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu zipatso.
5Pamene tinkatsata mkhalidwe wathu wachibadwa, zilakolako zoipa zimene Malamulo adaaziwutsa zinkagwira ntchito mwa ife, ndipo zidabala imfa.
6Koma tsopano tamasuka ku Malamulowo. Tidachita ngati kufa nkulekana ndi Malamulo amene kale ankatimanga. Tsopano Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mwa njira yatsopano, osatinso mwa njira yakale ija yakungotsata Malamulo olembedwa.
Za Malamulo ndi za uchimo7 Eks. 20.17; Deut. 5.21 Tsono tinene chiyani? Kodi tinene kuti Malamulo ndi auchimo? Mpang'ono pomwe. Koma Malamulowo ndiwo adandizindikiritsa za uchimo. Pakuti sindikadadziŵa kuipa kwa kusirira, Malamulo akadapanda kunena kuti, “Usasirire”.
8Chifukwa cha lamuloli, uchimo udapeza mpata woutsa mwa ine khalidwe la masiriro osiyanasiyana. Pakuti ngati palibe malamulo, uchimo sungachite kanthu.
9Ine kale ndinali ndi moyo opanda malamulo. Koma pamene ndidayamba kudziŵa malamulo, pomwepo uchimo udayamba kulimba,
10ndipo ine ndidakhala ngati ndafa. Tsono malamulo omwewo amene adaayenera kufikitsa anthu ku moyo, ine adandifikitsa ku imfa.
11Gen. 3.13Pakuti uchimo udapeza mpata chifukwa cha malamulo, ndipo mwa malamulowo udandinyenga ndi kundipha.
12Mosakayika konse, Malamulo a Mose ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo lamulo lililonse mwa Malamulowo ndi loyera, lolungama ndi labwino.
13Kodi tsono ndiye kuti chinthu chabwinochi chidandiphetsa? Mpang'ono pomwe. Koma uchimo ndiwo udandipha pakugwiritsa ntchito chinthu chabwinocho kuti khalidwe lenileni la uchimowo liwonekere poyera kuti ndi uchimodi. Motero kudzera mwa malamulo, uchimo umaoneka woipa kopitirira.
Za makhalidwe aŵiri olimbana m'kati mwa munthu14Tikudziŵa kuti Malamulo a Mose ndi opatsidwa ndi Mulungu. Koma ine ndine munthu wofooka chabe, wogulitsidwa ngati kapolo ku uchimo.
15Aga. 5.17Sindimvetsa bwino zimene ndimachita. Pakuti sindichita zimene ndifuna kuchita, koma zomwe ndimadana nazo, nzimene ine ndimazichita.
16Koma ngati sindifuna kuchita zoipa zimene ndimachita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti Malamulo aja ndi abwino.
17Motero zimene zimachitikazo, sindine amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine.
18Ndikudziŵa kuti mwa ine simukhala kanthu kabwino. Ndikamati, “ine”, ndikunena khalidwe langa lokonda zoipa. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, komabe sindizichita.
19Sindichita zabwino zimene ndifuna, koma ndimachita zoipa zimene sindifuna.
20Ngati ndichita zimene sindizifuna, sindinenso amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine.
21Motero ndimaona kuti chimene chimachitika nchakuti pamene ndifuna kuchita zabwino, zoipa zili nane pomwepo.
22Mtima wanga umakondwa ndi Malamulo a Mulungu,
23koma m'kati mwanga ndimaona lamulo lina lolimbana ndi lamulo limene mtima wanga wavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa kapolo wa lamulo la uchimo lokhala m'kati mwanga.
24Kalanga ine! Ndani adzandipulumutsa ku khalidwe langa lino londidzetsera imfa?
25Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Motero ineyo, ndi mtima wanga ndimatumikira Malamulo a Mulungu, chonsecho ndi khalidwe langa lokonda zoipa, ndimatumikira lamulo la uchimo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.