1 2Maf. 24.18-20; 2Mbi. 36.11-13 Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinai, Zedekiya ataloŵa ufumu wa ku Yuda, Hananiya mwana wa Azuri mneneri wa ku Gibiyoni, adalankhula nane ku Nyumba ya Chauta. Ansembe ndi anthu onse alikumva, iye adati,
2Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndathyola goli laukapolo la mfumu ya ku Babiloni.
3Zisanathe zaka ziŵiri, ndidzabwezera ziŵiya zonse za ku Nyumba yanga ku malo ano, zimene Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adazichotsa kuno kupita nazo ku Babiloni.
4Ndidzambwezanso ku malo ano Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda. Ndidzabweza akapolo onse ochokera ku Yuda amene adatengedwa kupita ku Babiloni. Motero ndidzathyola goli laukapolo la mfumu ya ku Babiloni.”
5Apo mneneri Yeremiya adayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anali m'Nyumba ya Chauta. Adati,
6“Inde momwemo! Chauta achitedi choncho. Chauta achitedi zimene walosazi, pakubwezera ziŵiya za ku Nyumba yake ndi akapolo onse ku malo ano kuchokera ku Babiloni.
7Komabe ungomva zimene nditi ndikuuze iweyo ndi anthu onse.
8Aneneri amene adatsogola kale ankalosa za nkhondo, za njala ndi za mliri, zodzagwera maiko ambiri ndi maufumu otchuka.
9Koma ngati mneneri alosa za mtendere, zimene walosazo zikachitikadi, pamenepo zidzadziŵika kuti Chauta adamtumadi.”
10Pamenepo mneneri Hananiya adachotsa goli m'khosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola.
11Adauza anthu onse kuti, “Chauta akuti, ‘Umu ndimo m'mene ndidzathyolera goli laukapolo la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Ndidzalichotsa m'khosi mwa anthu a mitundu yonse zisanathe zaka ziŵiri.’ ” Zitatero mneneri Yeremiya adachokapo.
12Patapita nthaŵi pang'ono Hananiya atathyola goli m'khosi mwa Yeremiya, Chauta adauza Yeremiya kuti,
13“Pita ukamuuze Hananiya mau a Chauta akuti, ‘Iweyo wathyola goli lamtengo, m'malo mwake Ine ndidzaika goli lachitsulo.
14Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndaika goli lachitsulo m'khosi mwa anthu a mitundu yonseyi, kuti azitumikira Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Adzamutumikiradi, ndipo ndampatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”
15Tsono Yeremiya adauza Hananiya kuti, “Mvera, iwe Hananiya, Chautatu sadakutume, ndipo iweyo wanyenga anthuŵa kuti azimvera ulosi wabodza.
16Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, ‘Chenjera, ndidzakuchotsa pa dziko lapansi. Ufa chaka chino chisanathe, chifukwa chakuti wakhala ukulalikira zopandukira Chauta.’ ”
17Zidachitikadi kuti mneneri Hananiya adafa chaka chomwecho, mwezi wachisanu ndi chiŵiri.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.