1Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani.
Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu,
thupi langa likulakalaka Inu
ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
2Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera
ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
3Ndidzakutamandani
chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo.
4Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga.
Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera.
5Mudzandikhutitsa ndi zonona,
ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala.
6Ndikagona pabedi panga ndimalingalira za Inu,
usiku wonse ndimasinkhasinkha za Inu.
7Inu mwakhala chithandizo changa,
motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu.
8Mtima wanga ukukangamira Inu,
dzanja lanu lamanja likundichirikiza.
9Koma anthu amene amayesayesa kuwononga moyo wanga,
adzatsikira ku dziko la anthu akufa.
10Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo,
motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe.
11Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu.
Onse olumbirira Iye, adzamtamanda,
koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.