1Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse.
Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu.
2Ndikugwada moŵerama
kumaso kwa Nyumba yanu yoyera.
Ndikutamanda dzina lanu
chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,
chifukwanso cha kukhulupirika kwanu.
Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu
kupambana chinthu china chilichonse.
3Pa tsiku limene ndidakuitanani,
Inu mudandiyankha,
mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
4Mafumu onse a m'dziko adzakutamandani, Inu Chauta,
chifukwa amva mau a pakamwa panu.
5Adzaimba nyimbo zotamanda njira za Chauta,
pakuti ulemerero wa Chauta ndi waukulu.
6Ngakhale Chauta ndi wamphamvu,
amasamalira anthu otsika,
koma anthu odzikuza amaŵadziŵira chapatali.
7Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto,
Inu mumasunga moyo wanga.
Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya,
dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
8Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi.
Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya.
Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.