Yob. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1“Zonse mukunenazi ndidaziwona ndi maso,

ndidazimva ndi makutu anga, ndipo ndidazimvetsa.

2Zimene inu mumadziŵa, inenso ndimazidziŵa.

Inu simundipambana ai.

3Koma ine ndikadakonda kulankhula ndi Mphambe,

ndikadakonda kukamba naye Mulungu

za mlandu wanga pamasompamaso.

4Inuyo ndinu okometsa zinthu ndi mabodza.

Nonsenu muli ngati asing'anga apakamwa chabe.

5Achikhala munangokhala chete,

apo mukadachita zanzeru

6Tsono mumve zimene nditi ndinene,

mumvere mau anga ofotokoza za mlandu wanga.

7Kodi chifukwa chiyani mukunama potchula Mulungu?

Chifukwa chiyani mukunena mabodza m'dzina lake?

8Kodi mukuti mukondere Mulungu?

Kodi mukuti muteteze Mulungu pa mlandu wake?

9Mulungu atayang'anitsitsa inu,

kodi nkukupezani kuti ndinu osalakwa?

Kodi mungathe kumnyenga

monga m'mene munthu anganyengere munthu mnzake?

10Ndithudi, adzakudzudzulani,

mukamachita zokondera m'seri.

11Kodi ulamuliro wake sungakuwopseni?

Kodi mphamvu zake sizingakuchititseni mantha?

12Miyambi yanuyi ndi yopandapake ngati phulusa.

Zimene mukulankhula kuti mudzitchinjirize nazo

zili ngati dothi.

13“Mukhale chete, ineyo ndilankhule,

ndipo zimene zichitike, zichitike.

14Ndili wokonzeka kuika moyo wanga pa chiswe,

kaya nkufa, ndife basi.

15Ngakhale Mulungu andiphe,

ndidzamkhulupirirabe,

ndipo ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.

16Kulimba mtima kwanga ndiye kudzandipulumutse,

poti munthu woipa sangafike pamaso pa Mulungu.

17Mumvetsere mau anga mosamala,

mutchere khutu zolankhula zanga.

18Mlandu wanga ndaukonza,

ndikudziŵa kuti sadzandipeza wolakwa.

19Kodi pali yani amene angatsutsane nane?

Ngati zili choncho,

ndidakangokhala chete, nkufa basi.

20Inu Mulungu, ndikukupemphani zinthu ziŵiri zokha,

sindidzayesa kukubisalirani.

21Muleke kundilanga,

kuwopa Inu kusandidetse nkhaŵa.

22Mundiitane tsono ndipo ndidzayankha.

Kapena mundilole kuti ndilankhule ndine,

Inuyo mundiyankhe.

23“Kodi zolakwa zanga nzingati,

ndipo machimo anga ndangati?

Mundidziŵitse kulakwa kwanga ndi kuchimwa kwanga.

24Chifukwa chiyani mukundifulatira?

Bwanji mukundiyesa mdani wanu?

25Kodi mukufuna kuwopsa ine,

tsamba louluka ndi mphepone?

Kapena mukuti mundithamangitse, ine mungu woumane?

26Inu mukundizenga zinthu

zondiŵaŵa, umafukula ngakhale

zolakwa za pa ubwana wanga.

27 Yob. 33.11 Inu mumamanga miyendo yanga ndi matangadza,

mumalonda mayendedwe anga onse,

mumazonda ndi poponda mapazi anga pomwe.

28Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa,

ngati chovala chodyewa ndi njenjete.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help